< Ezekieli 19 >
1 “Imba nyimbo ya madandawulo, kuyimbira akalonga a ku Israeli.
2 Uzinena kuti, “‘Amayi ako anali ndani? Anali ngati mkango waukazi! Iwo unabwatama pakati pa mikango yayimuna; unkalera ana ake pakati pa misona.
3 Unalera mmodzi mwa ana ake, ndipo mwanayo anasanduka mkango wamphamvu. Unaphunzira kugwira nyama, ndipo unayamba kudya anthu.
4 Anthu amitundu anamva za mkangowo, ndipo tsiku lina unagwa mʼmbuna mwawo. Iwo anawukoka ndi ngowe kupita nawo ku dziko la Igupto.
5 “‘Amayi aja ataona kuti mwana ankamukhulupirira uja wagwidwa ndi kuti chiyembekezo chake chapita padera, amayiwo anatenganso mwana wina namusandutsa mkango wamphamvu.
6 Unkayendayenda pakati pa mikango inzake, pakuti tsopano unali mkango wamphamvu. Unaphunzira kugwira nyama ndipo unayamba kudya anthu.
7 Unagwetsa malinga awo, ndikuwononga mizinda yawo. Onse a mʼdzikomo anachita mantha chifukwa cha kubangula kwake.
8 Pamenepo mitundu ya anthu, makamaka ochokera madera ozungulira, inabwera kudzalimbana nawo. Anawutchera ukonde wawo, ndipo tsiku lina unagwera mʼmbuna mwawo.
9 Anawukoka ndi ngowe nawuponya mʼchitatanga. Anabwera nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ndipo mfumuyo inawuponya mʼndende ndi cholinga choti liwu lake lisamamvekenso ku mapiri a Israeli.
10 “‘Amayi ako anali ngati mpesa mʼmunda wamphesa wodzalidwa mʼmbali mwa madzi. Unabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri chifukwa cha kuchuluka kwa madzi.
11 Nthambi zake zinali zolimba, zoyenera kupangira ndodo yaufumu. Unatalika nusomphoka pakati pa zomera zina. Unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake, ndi nthambi zake zambiri.
12 Koma unazulidwa mwaukali ndipo unagwetsedwa pansi. Unawuma ndi mphepo ya kummawa, zipatso zake zinayoyoka; nthambi zake zolimba zinafota ndipo moto unapsereza mtengo wonse.
13 Ndipo tsopano anawuwokeranso ku chipululu, dziko lowuma ndi lopanda madzi.
14 Moto unatulukanso mu mtengomo ndi kupsereza nthambi ndi zipatso zake. Palibe nthambi yolimba inatsala pa mtengowo yoyenera kupangira ndodo yaufumu. Imeneyi ndi nyimbo yachisoni ndipo yasanduka nyimbo ya pa maliro.’”