< Ezekieli 16 >
1 Yehova anayankhula nane kuti,
여호와의 말씀이 또 내게 임하여 가라사대
2 “Iwe mwana wa munthu, udzudzule Yerusalemu za ntchito zake zonyansa.
인자야 예루살렘으로 그 가증한 일을 알게 하여
3 Umuwuze kuti, ‘Ambuye Yehova akukuwuza, iwe Yerusalemu kuti: Kwawo kwa makolo ako ndi ku Kanaani ndipo iwe unabadwira komweko. Abambo ako anali Mwamori, amayi ako anali Mhiti.
이르기를 주 여호와께서 예루살렘에 대하여 말씀하시되 네 근본과 난 땅은 가나안이요 네 아비는 아모리 사람이요 네 어미는 헷사람이라
4 Pa tsiku lomwe unabadwa sanadule mchombo wako. Sanakusambitse mʼmadzi kuti uyere. Sanakuthire mchere kapena kukukulunga mʼnsalu.
너의 난 것을 말하건대 네가 날 때에 네 배꼽줄을 자르지 아니하였고 너를 물로 씻어 정결케 하지 아니하였고 네게 소금을 뿌리지 아니하였고 너를 강보에 싸지도 아니하였나니
5 Palibe ndi mmodzi yemwe anakusamala kapena kukumvera chisoni kuti akuchitire zimenezi. Mʼmalo mwake anakutaya panja poyera, chifukwa ananyansidwa nawe pa tsiku lako lobadwa.
너를 돌아 보아 이 중에 한 가지라도 네게 행하여 너를 긍휼히 여긴 자가 없었으므로 네가 나던 날에 네 몸이 꺼린바 되어 네가 들에 버리웠었느니라
6 “‘Tsono pamene ndinkadutsa, ndinakuona ukuvimvinizika mʼmagazi ako. Ndinakuyankhula uli mʼmagazi ako omwewo kuti, ‘Khala ndi moyo,’
내가 네 곁으로 지나 갈 때에 네가 피투성이가 되어 발짓하는 것을 보고 네게 이르기를 너는 피투성이라도 살라 다시 이르기를 너는 피투성이라도 살라 하고
7 ndi kuti ukule ngati mbewu ya mʼmunda. Iwe unakula ndipo unatalika ndi kutha msinkhu. Mawere ako anayamba kumera ndi tsitsi lakonso linayamba kutalika. Komabe unali wamaliseche ndi wausiwa.
내가 너로 들의 풀 같이 많게 하였더니 네가 크게 자라고 심히 아름다우며 유방이 뚜렷하고 네 머리털이 자랐으나 네가 오히려 벌거벗은 적신이더라
8 “‘Tsono pamene ndinkadutsanso ndinaona kuti nthawi yako yomanga banja inakwana. Tsono ndinakufunditsa chovala changa ndi kubisa umaliseche wako. Ndinachita nawe pangano la ukwati ndipo unakhala wanga, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.
내가 네 곁으로 지나며 보니 네 때가 사랑스러운 때라 내 옷으로 너를 덮어 벌거벗은 것을 가리우고 네게 맹세하고 언약하여 너로 내게 속하게 하였었느니라 나 주 여호와의 말이니라
9 “‘Ine ndinakusambitsa mʼmadzi kutsuka magazi ako ndikukudzoza mafuta.
내가 물로 너를 씻겨서 네 피를 없이 하며 네게 기름을 바르고
10 Ndinakuveka zovala zopetapeta ndi nsapato za chikopa. Ndinakuveka zovala zabafuta ndi kukuveka zovala za bafuta.
수 놓은 옷을 입히고 물돼지 가죽신을 신기고 가는 베로 띠우고 명주로 덧입히고
11 Ndinakukongoletsa ndi zokometsera zamtengowapatali: ndinakuveka zibangiri mʼmanja mwako ndi mkanda mʼkhosi mwako,
패물을 채우고 팔고리를 손목에 끼우고 사슬을 목에 드리우고
12 ndipo ndinakuveka chipini pa mphuno yako, ndolo ku makutu ako ndiponso chipewa chaufumu pa mutu wako.
코고리를 코에 달고 귀고리를 귀에 달고 화려한 면류관을 머리에 씌웠나니
13 Choncho unavala zokongoletsa zagolide ndi siliva. Zovala zako zinali zabafuta, zasilika ndi za nsalu zopetapeta. Chakudya chako chinali ufa wosalala uchi ndi mafuta a olivi. Motero unakhala wokongola kwambiri ndipo unasanduka mfumukazi.
이와 같이 네가 금, 은으로 장식하고 가는 베와 명주와 수놓은 것을 입으며 또 고운 밀가루와 꿀과 기름을 먹음으로 극히 곱고 형통하여 왕후의 지위에 나아갔느니라
14 Ndipo mbiri ya kukongola kwako inawanda pakati pa anthu a mitundu ina, chifukwa ulemerero umene ndinakupatsa unapititsa patsogolo kukongola kwako, akutero Ambuye Yehova.
네 화려함을 인하여 네 명성이 이방인 중에 퍼졌음은 내가 네게 입힌 영화로 네 화려함이 온전함이니라 나 주 여호와의 말이니라
15 “‘Koma iwe unatama kukongola kwako ndipo unayamba kuchita zadama chifukwa cha kutchuka kwako. Unkachita chigololo ndi kumangodzipereka kwa aliyense wodutsa ndipo kukongola kwako kunakhala kwake.
그러나 네가 네 화려함을 믿고 네 명성을 인하여 행음하되 무릇 지나가는 자면 더불어 음란을 많이 행하므로 네 몸이 그들의 것이 되도다
16 Unatenga zovala zako zina nukakongoletsera malo opembedzerako mafano, ndipo kumeneko umachitirako zigololo. Zinthu izi sizinachitikepo nʼkale lomwe ndipo sizidzachitikanso.
네가 네 의복을 취하여 색스러운 산당을 너를 위하여 만들고 거기서 행음하였나니 이런 일은 전무후무하니라
17 Unatenga zokongoletsera zopangidwa ndi golide ndi siliva zimene ndinakupatsa ndipo unadzipangira wekha mafano aamuna amene unkachita nawo za dama.
네가 또 나의 준 금, 은 장식품으로 너를 위하여 남자 우상을 만들어 행음하며
18 Ndipo iwe unatenga zovala zako zopetapeta ndi kuveka mafano. Mafuta anga ndi lubani wanga unapereka kwa mafanowo.
또 네 수 놓은 옷으로 그 우상에게 입히고 나의 기름과 향으로 그 앞에 베풀며
19 Chakudya chimene ndinakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi, zimene ndinkakudyetsa nazo unazitenga nʼkuzipereka kwa mafanowo ngati nsembe ya fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
또 내가 네게 주어 먹게 한 내 식물 곧 고운 밀가루와 기름과 꿀을 네가 그 앞에 베풀어 향기를 삼았나니 과연 그렇게 하였느니라 나 주 여호와의 말이니라
20 “‘Ndipo unatenga ana ako aamuna ndi ana aakazi amene unandibalira ine, ndipo unakawapereka ngati nsembe kwa mafanowo. Kodi zigololo zakozo sizinakukwanire
또 네가 나를 위하여 낳은 네 자녀를 가져 그들에게 드려 제물을 삼아 불살랐느니라 네가 너의 음행을 작은 일로 여겨서
21 kuti uziphanso ana anga ndi kuwapereka ngati nsembe kwa mafano akowo?
나의 자녀들을 죽여 우상에게 붙여 불 가운데로 지나가게 하였느냐
22 Chifukwa cha zadama zako zonyansazi unayiwala masiku a ubwana wako pamene unali wamaliseche, wausiwa ndiponso womangovivinizika mʼmagazi.
네 어렸을 때에 벌거벗어 적신이었으며 피투성이가 되어서 발짓하던 것을 기억지 아니하고 네가 모든 가증한 일과 음란을 행하였느니라
23 “‘Tsoka! Tsoka kwa iwe, akutero Ambuye Yehova chifukwa powonjezera pa zoyipa zako zonse,
나 주 여호와가 말하노라 너는 화 있을진저 화 있을진저 네가 모든 악을 행한 후에
24 wadzimangira wekha nsanja ndi guwa pa mabwalo onse.
너를 위하여 누를 건축하며 모든 거리에 높은 대를 쌓았도다
25 Pa msewu uliwonse wamanga nsanjazo. Motero wanyazitsa kukongola kwako podzipereka kwa aliyense amene adutsapo.
네가 높은 대를 모든 길 머리에 쌓고 네 아름다움을 가증하게 하여 모든 지나가는 자에게 다리를 벌려 심히 행음하고
26 Umachita chigololo ndi Aigupto, anthu adama oyandikana nawe. Choncho unandikwiyitsa chifukwa unachulukitsa za dama zako.
하체가 큰 네 이웃나라 애굽 사람과도 행음하되 심히 음란히 하여 내 노를 격동하였도다
27 Nʼchifukwa chake ndinatambasula dzanja langa kukukantha ndi kuchepetsa dziko lako. Ndinakupereka kwa adani ako, Afilisti amene amayipidwa ndi makhalidwe ako onyansa.
그러므로 내가 내 손을 네 위에 펴서 네 일용 양식을 감하고 너를 미워하는 블레셋 여자 곧 네 더러운 행실을 부끄러워하는 자에게 너를 붙여 임의로 하게 하였거늘
28 Chifukwa cha chilakolako chako unachitanso zadama ndi Aasiriya. Ngakhale unachita nawo chigololo koma sunakhutitsidwebe.
네가 음욕이 차지 아니하여 또 앗수르 사람과 행음하고 그들과 행음하고도 오히려 부족히 여겨
29 Choncho unapitirirabe kuchita chigololo ndi Ababuloni, anthu a mʼdziko lokonda zamalonda. Ngakhale unachita izi, komabe sunakhutitsidwe.
장사하는 땅 갈대아에까지 심히 행음하되 오히려 족한 줄을 알지 못하였느니라
30 “‘Ambuye Yehova akuti: Mtima wako ndi wofowoka kwambiri chifukwa unachita zonsezo monga ngati mkazi wopanga manyazi.
나 주 여호와가 말하노라 네가 이 모든 일을 행하니 이는 방자한 음부의 행위라 네 마음이 어찌 그리 약한지
31 Unamanga nsanja pa msewu uliwonse. Unamanganso kachisi pabwalo lililonse. Komabe sunachite ngati mkazi wadama chifukwa unakana malipiro.
네가 누를 모든 길 머리에 건축하며 높은 대를 모든 거리에 쌓고도 값을 싫어하니 창기 같지도 않도다
32 “‘Iwe mkazi wachigololo! Umakonda amuna achilendo kupambana mwamuna wakowako!
그 지아비 대신에 외인과 사통하여 간음하는 아내로다
33 Amuna ndiwo amapereka malipiro kwa mkazi wadama. Koma iwe ndi amene ukupereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse. Choncho umazinyengerera kuti zizibwera kwa iwe kuchokera mbali zonse kudzagona nawe.
사람들은 모든 창기에게 선물을 주거늘 오직 너는 네 모든 정든 자에게 선물을 주며 값을 주어서 사방에서 와서 너와 행음하게 하니
34 Chotero iwe ukusiyana ndi akazi ena achigololo, pakuti palibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye unkapereka ndalama osati ena kukupatsa ndalama ayi. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.
너의 음란함이 다른 여인과 같지 아니함은 행음하려고 너를 따르는 자가 없음이며 또 네가 값을 받지 아니하고 도리어 줌이라 그런즉 다른 여인과 같지 아니하니라
35 “‘Tsono mkazi wachigololo iwe, imva mawu a Yehova!
그러므로 너 음부야 여호와의 말을 들을지어다
36 Ambuye Yehova akuti, popeza unavula ndi kuonetsa umaliseche wako mopanda manyazi, unachita chigololo ndi zibwenzi zako pamodzi ndi mafano ako onyansa, komanso popeza unapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zoperekedwa kwa mafano,
나 주 여호와가 말하노라 네가 네 누추한 것을 쏟으며 네 정든 자와 행음함으로 벗은 몸을 드러내며 또 가증한 우상을 위하여 네 자녀의 피를 그 우상에게 드렸은즉
37 nʼchifukwa chake Ine ndidzasonkhanitsa zibwenzi zako zonse, zimene unkasangalala nazo, amene unkawakonda ndi amene unkawada. Ndidzawasonkhanitsa motsutsana nawe kuchokera ku madera onse okuzungulira ndipo Ine ndidzakuvula pamaso pawo, ndipo iwo adzaona umaliseche wako wonse.
내가 저의 즐거워하는 정든 자와 사랑하던 모든 자와 미워하던 모든 자를 모으되 사방에서 모아 너를 대적하게 할 것이요 또 네 벗은 몸을 그 앞에 드러내어 그들로 그것을 다 보게 할 것이며
38 Ine ndidzakulanga monga mmene amalangira akazi amene amachita chigololo ndiponso opha anthu. Chifukwa cha ukali wanga ndi nsanje yanga, ndidzakhetsa magazi ako mokwiya kwambiri.
내가 또 간음하고 사람의 피를 흘리는 여인을 국문함 같이 너를 국문하여 진노의 피와 투기의 피를 네게 돌리고
39 Ndidzakupereka mʼmanja mwa zibwenzi zako ndi kuwononga nyumba zopembedzera mafano ako. Iwo adzakuvula zovala zako ndi kutenga zodzikometsera zako zabwino. Choncho adzakusiya wa maliseche ndi wausiwa.
내가 또 너를 그들의 손에 붙이리니 그들이 네 누를 헐며 네 높은 대를 훼파하며 네 의복을 벗기고 네 장식품을 빼앗고 네 몸을 벌거벗겨 버려두며
40 Iwo adzabweretsa gulu la anthu limene lidzakuponya miyala ndi kukutematema ndi malupanga awo.
무리를 데리고 와서 너를 돌로 치며 칼로 찌르며
41 Adzatentha nyumba zako ndi kukulanga iwe pamaso pa akazi ambiri. Ndidzathetsa chigololo chako, ndipo sudzalipiranso zibwenzi zako.
불로 너의 집들을 사르고 여러 여인의 목전에서 너를 벌할지라 내가 너로 곧 음행을 그치게 하리니 네가 다시는 값을 주지 아니하리라
42 Ukali wanga udzalekera pamenepo ndipo sindidzakuchitiranso nsanje. Ndidzakhala chete osakwiyanso.
그리한즉 내가 네게 대한 내 분노가 그치며 내 투기가 네게서 떠나고 마음이 평안하여 다시는 노하지 아니하리라
43 “‘Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako koma unandikwiyitsa ndi zinthu zonsezi, Ine ndidzakubwezera ndithu chilango pamutu pako chifukwa cha zimene wachita, akutero Ambuye Yehova. Paja unawonjezera chigololo pa machitidwe ako onyansa.
네가 어렸을 때를 기억지 아니하고 이 모든 일로 나를 격노케 하였은즉 내가 네 행위대로 네 머리에 보응하리니 네가 이 음란과 네 모든 가증한 일을 다시는 행하지 아니하리라 나 주 여호와의 말이니라
44 “‘Taona, onse onena miyambi adzakuphera mwambi wakuti, ‘Make mbuu, mwana mbuu.’
무릇 속담하는 자가 네게 대하여 속담하기를 어미가 어떠하면 딸도 그렇다 하리라
45 Ndiwedi mwana weniweni wamkazi wa mayi wako, amene amanyoza mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mʼbale weniweni wa abale ako, amene amanyoza amuna awo ndi ana awo. Amayi ako anali Mhiti ndipo abambo ako anali Mwamori.
너는 그 남편과 자녀를 싫어한 어미의 딸이요 너는 그 남편과 자녀를 싫어한 형의 동생이로다 네 어미는 헷 사람이요 네 아비는 아모리 사람이며
46 Mkulu wako anali Samariya, ndipo iye pamodzi ndi ana ake aakazi ankakhala cha kumpoto kwako. Mngʼono wako, Sodomu ankakhala cha kummwera kwako pamodzi ndi ana ake aakazi.
네 형은 그 딸들과 함께 네 좌편에 거하는 사마리아요 네 아우는 그 딸들과 함께 네 우편에 거하는 소돔이라
47 Iwe sunangotsatira kokha njira zawo zoyipa ndi kuchita zonyansa zawo, koma patangopita nthawi pangʼono machitidwe ako oyipa anaposa awo.
네가 그들의 행위대로만 행치 아니하며 그 가증한 대로만 행치 아니하고 그것을 적게 여겨서 네 모든 행위가 그보다 더욱 부패하였도다
48 Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ngakhale mʼbale wako Sodomu ndi ana ake aakazi sanachitepo zimene iwe ndi ana ako aakazi munachita.
나 주 여호와가 말하노라 내가 나의 삶을 두고 맹세하노니 네 아우 소돔 곧 그와 그 딸들은 너와 네 딸들의 행위 같이 행치 아니하였느니라
49 “‘Tsono tchimo la mʼbale wako Sodomu linali ili: Iye ndi ana ake aakazi ankanyadira kuchuluka kwa chakudya ndi chuma chawo. Koma sanalabadireko kuthandiza osauka ndi aumphawi.
네 아우 소돔의 죄악은 이러하니 그와 그 딸들에게 교만함과 식물의 풍족함과 태평함이 있음이며 또 그가 가난하고 궁핍한 자를 도와주지 아니하며
50 Anali odzitukumula ndipo ankachita zonyansa pamaso panga. Nʼchifukwa chake ndinawachotsa monga mmene waoneramu.
거만하여 가증한 일을 내 앞에서 행하였음이라 그러므로 내가 보고 곧 그들을 없이 하였느니라
51 Samariya sanachite ngakhale theka la machimo amene unachita. Iwe wachita zinthu zonyansa zambiri kuposa iwo, motero kuti abale ako awiriwo amaoneka ngati olungama kuyerekeza ndi iye.
사마리아는 네 죄의 절반도 범치 아니하였느니라 네가 그들보다 가증한 일을 심히 행한고로 너의 가증한 행위로 네 형과 아우를 의롭게 하였느니라
52 Tsono iwenso uyenera kuchita manyazi popeza waonetsa abale ako ngati osachimwa. Popeza kuti machimo ako ndi onyansa kwambiri kupambana awo, tsonotu iwowo akuoneka olungama kupambana iweyo. Choncho iwenso uchite manyazi ndi kunyozedwa popeza unaonetsa abale ako ngati olungama.
네가 네 형과 아우를 논단하였은즉 너도 네 수치를 담당할지니라 네가 그들보다 더욱 가증한 죄를 범하므로 그들이 너보다 의롭게 되었나니 네가 네 형과 아우를 의롭게 하였은즉 너는 놀라며 네 수치를 담당할지니라
53 “‘Koma, ndidzadalitsanso Sodomu ndi ana ake aakazi. Ndidzadalitsanso Samariya ndi ana ake aakazi. Pa nthawi yomweyo ndidzakudalitsanso iwe Yerusalemu.
내가 그들의 사로잡힘 곧 소돔과 그 딸들의 사로잡힘과 사마리아와 그 딸들의 사로잡힘과 그들 중에 너의 사로잡힌 자의 사로잡힘을 돌이켜서
54 Ndidzatero kuti uchite manyazi ndi kunyozeka chifukwa cha zonse zimene unachita powatonthoza anthuwa.
너로 네 수욕을 담당하고 너의 행한 모든 일을 인하여 부끄럽게 하리니 이는 네가 그들에게 위로가 됨이라
55 Motero mʼbale wako Sodomu ndi ana ake akadzakhala monga mmene analili poyamba paja, ndiponso mʼbale wako Samariya akadzakhalanso monga mmene anali poyamba paja, ndiye kuti iwenso ndi ana ako mudzakhala monga mmene munalili payamba paja.
네 아우 소돔과 그 딸들이 옛 지위를 회복할 것이요 사마리아와 그 딸들도 그 옛 지위를 회복할 것이며 너와 네 딸들도 너희 옛 지위를 회복할 것이니라
56 Kale lija pamene unkanyada, suja unkanyogodola mʼbale wako Sodomu
네가 교만하던 때에 네 아우 소돔을 네 입으로 말하지도 아니하였나니
57 kuyipa kwako kusanadziwike? Koma tsopano wafanana naye. Wasandukano chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse owazungulira ndiponso kwa Afilisti. Ndithu onse amene akuzungulira amakunyoza.
곧 네 악이 드러나기 전에며 아람 딸들이 너를 능욕하기 전에며 너의 사방에 둘러 있는 블레셋 딸들이 너를 멸시하기 전에니라
58 Choncho udzalangidwa chifukwa cha zigololo zako ndi machitidwe anu onyansa, akutero Yehova.
네 음란과 네 가증한 일을 네가 담당하였느니라 나 여호와의 말이니라
59 “‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulanga molingana ndi zimene unachita. Iwe unanyoza lumbiro lako pophwanya pangano langa.
나 주 여호와가 말하노라 네가 맹세를 멸시하여 언약을 배반하였은즉 내가 네 행한 대로 네게 행하리라
60 Komabe, Ine ndidzakumbukira pangano limene ndinachita nawe mʼmasiku a unyamata wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha ndi iwe.
그러나 내가 너의 어렸을 때에 너와 세운 언약을 기억하고 너와 영원한 언약을 세우리라
61 Tsono udzakumbukira njira zako zakale. Udzachita manyazi polandiranso abale ako, wamkulu ndi wamngʼono yemwe. Ndidzawaperekanso kwa iwe kuti akhale ngati ana ako ngakhale kuti sali a mʼpangano langa ndi iwe.
네가 네 형과 아우를 접대할 때에 네 행위를 기억하고 부끄러워할 것이라 내가 그들을 네게 딸로 주려니와 네 언약으로 말미암음이 아니니라
62 Kotero ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
내가 네게 내 언약을 세워서 너로 나를 여호와인 줄 알게 하리니
63 Ndikadzakukhululukira zoyipa zako zonse zimene unachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzatha nʼkuyankhula komwe, akutero Ambuye Yehova.’”
이는 내가 네 모든 행한 일을 용서한 후에 너로 기억하고 놀라고 부끄러워서 다시는 입을 열지 못하게 하려 함이니라 나 주 여호와의 말이니라 하셨다 하라