< Ezekieli 14 >

1 Tsiku lina ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kwa ine ndipo anakhala pansi pamaso panga.
et venerunt ad me viri seniorum Israhel et sederunt coram me
2 Ndipo Yehova anandipatsa uthenga uwu nati,
et factus est sermo Domini ad me dicens
3 “Iwe mwana wa munthu, anthu awa ayika mtima pa mafano awo. Ayikanso maso awo pa zinthu zina zoyipa zopunthwitsa. Kodi ayembekezera kuti ndiwayankhe chimene atandifunse?
fili hominis viri isti posuerunt inmunditias suas in cordibus suis et scandalum iniquitatis suae statuerunt contra faciem suam numquid interrogatus respondebo eis
4 Tsono yankhula nawo ndi kuwawuza kuti zimene akunena Ambuye Yehova: ‘Ngati Mwisraeli aliyense ayika mtima wake pa mafano ndi kuyika maso ake pa zinthu zoyipa zopunthwitsa, kenaka nʼkupita kwa mneneri, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha molingana ndi kuchuluka kwa mafano ake.
propter hoc loquere eis et dices ad eos haec dicit Dominus Deus homo homo de domo Israhel qui posuerit inmunditias suas in corde suo et scandalum iniquitatis suae statuerit contra faciem suam et venerit ad prophetam interrogans per eum me ego Dominus respondebo ei in multitudine inmunditiarum suarum
5 Ine ndidzachita zimenezi kuti mwina nʼkukopa mitima ya anthu a Israeli, amene andisiya chifukwa cha mafano awo.’
ut capiatur domus Israhel in corde suo quo recesserunt a me in cunctis idolis suis
6 “Nʼchifukwa chake uwawuze Aisraeli kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Lapani! Siyani mafano anu ndi ntchito zanu zonse zonyansa!
propterea dic ad domum Israhel haec dicit Dominus Deus convertimini et recedite ab idolis vestris et ab universis contaminationibus vestris avertite facies vestras
7 “‘Ngati Mwisraeli wina aliyense kapena mlendo wina aliyense wokhala pakati pa Israeli adzichotsa yekha kwa Ine ndi kuyika mtima pa mafano ake ndi kuyikanso maso ake pa zinthu zopunthwitsa ndipo kenaka nʼkupita kwa mneneri kukafunsa nzeru, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha.
quia homo homo de domo Israhel et de proselytis quicumque advena fuerit in Israhel si alienatus fuerit a me et posuerit idola sua in corde suo et scandalum iniquitatis suae statuerit contra faciem suam et venerit ad prophetam ut interroget per eum me ego Dominus respondebo ei per me
8 Ine ndidzalimbana naye munthu ameneyo ndipo ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo. Ndidzamuchotsa pakati pa anthu anga. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
et ponam faciem meam super hominem illum et faciam eum in exemplum et in proverbium et disperdam eum de medio populi mei et scietis quia ego Dominus
9 “‘Ndipo ngati mneneri anyengedwa nanenera, Ine Yehova ndiye ndamunyenga mneneri ameneyo, ndipo ndidzatambasula dzanja langa kumukantha ndi kumuwononga pakati pa anthu anga Aisraeli.
et propheta cum erraverit et locutus fuerit verbum ego Dominus decepi prophetam illum et extendam manum meam super eum et delebo eum de medio populi mei Israhel
10 Iwo adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Chilango cha wodzafunsira nzeru kwa mneneri chidzafanana ndi chilango cha mneneriyo.
et portabunt iniquitatem suam iuxta iniquitatem interrogantis sic iniquitas prophetae erit
11 Ndidzachita zimenezi kuti Aisraeli asasocherenso kundisiya Ine ndi kuti asadziyipitsenso ndi machimo awo. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, akutero Ambuye Yehova.’”
ut non erret ultra domus Israhel a me neque polluatur in universis praevaricationibus suis sed sit mihi in populum et ego sim eis in Deum ait Dominus exercituum
12 Yehova anayankhula nane kuti,
et factus est sermo Domini ad me dicens
13 “Iwe mwana wa munthu, ngati dziko lindichimwira posandikhulupirira, Ine ndidzatambasula dzanja langa kulikantha pochepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala pa dzikolo ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe.
fili hominis terra cum peccaverit mihi ut praevaricetur praevaricans extendam manum meam super eam et conteram virgam panis eius et inmittam in eam famem et interficiam de ea hominem et iumentum
14 Ngakhale anthu atatu awa, Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, akanangopulumutsa moyo wawo chifukwa cha chilungamo chawo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
et si fuerint tres viri isti in medio eius Noe Danihel et Iob ipsi iustitia sua liberabunt animas suas ait Dominus exercituum
15 “Kapena ndikanatumiza zirombo mʼdziko monse ndi kulisiya lopanda anthu, ndipo dzikolo nʼkukhala chipululu chakuti munthu sangadutse chifukwa cha zirombo.
quod si et bestias pessimas induxero super terram ut vastem eam et fuerit invia eo quod non sit pertransiens propter bestias
16 Apanso, ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo okha akanapulumuka, koma dziko likanasanduka chipululu.’
tres viri isti qui fuerint in ea vivo ego dicit Dominus Deus quia nec filios nec filias liberabunt sed ipsi soli liberabuntur terra autem desolabitur
17 “Kapena ndikanatumiza lupanga mʼdzikolo ndi kunena kuti, ‘Lupanga lipite mʼdziko monse,’ ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe.
vel si gladium induxero super terram illam et dixero gladio transi per terram et interfecero de ea hominem et iumentum
18 Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna kapena ana aakazi. Iwo okha akanapulumuka.’
et tres viri isti fuerint in medio eius vivo ego dicit Dominus Deus non liberabunt filios neque filias sed ipsi soli liberabuntur
19 “Kapena ndikanatumiza mliri mʼdzikomo ndi kuonetsa ukali wanga pokhetsa magazi, kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe.
si autem et pestilentiam inmisero super terram illam et effudero indignationem meam super eam in sanguine ut auferam ex ea hominem et iumentum
20 Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti ngakhale Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, sakanatha ngakhale kupulumutsa mwana wamwamuna kapena wamkazi. Akanangodzipulumutsa okha chifukwa cha chilungamo chawo.
et Noe et Danihel et Iob fuerint in medio eius vivo ego dicit Dominus Deus quia filium et filiam non liberabunt sed ipsi iustitia sua liberabunt animas suas
21 “Pakuti Ambuye Yehova akuti: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzatumiza pa Yerusalemu zilango zanga zinayi izi: lupanga, njala, zirombo ndi mliri kuti ziwononge anthu ake ndi nyama zomwe!
quoniam haec dicit Dominus Deus quod si et quattuor iudicia mea pessima gladium et famem et bestias malas et pestilentiam misero in Hierusalem ut interficiam de ea hominem et pecus
22 Komabe padzakhala ena opulumuka, ana aamuna ndi ana aakazi amene adzatulutsidwa mʼdzikomo. Iwo adzabwera kwa inu, ndipo mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo, mitima yanu idzakhala pansi mukadzakumbukira chilango chimene ndinachita pa Yerusalemu.
tamen relinquetur in ea salvatio educentium filios et filias ecce ipsi egredientur ad vos et videbitis viam eorum et adinventiones eorum et consolabimini super malo quod induxi in Hierusalem in omnibus quae inportavi super eam
23 Mitima yanu idzakhala pansi mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo. Tsono mudzadziwa kuti Yerusalemu sindinamuchite zimenezi popanda chifukwa, akutero Ambuye Yehova.”
et consolabuntur vos cum videritis viam eorum et adinventiones eorum et cognoscetis quod non frustra fecerim omnia quae feci in ea ait Dominus Deus

< Ezekieli 14 >