< Ezekieli 12 >
1 Yehova anayankhula nane kuti,
2 “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu owukira, iwowo maso openyera ali nawo, koma sakuona ndipo makutu omvera ali nawo, koma sakumva chifukwa choti ndi anthu owukira.
3 “Choncho, iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Unyamuke nthawi yamasana iwo akuona. Uchite ngati wanyamuka kuchoka kumene ukukhala kupita ku dziko lachilendo iwowo akuona. Mwina adzamvetsetsa, paja ndi anthu aupandu.
4 Utulutse katundu wako wopita naye ku ukapolo nthawi ya masana iwo akuona. Ndipo nthawi ya madzulo, iwo akuona, uchoke monga ngati ukupita ku ukapolo.
5 Iwo akuona, ubowole pa khoma ndipo utulutsirepo katundu wako.
6 Usenze katundu wako pa phewa iwo akuona, ndipo upite kunja ku mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone pansi, pakuti ndakusandutsa iwe chizindikiro chochenjeza Aisraeli.”
7 Choncho ine ndinachita monga momwe anandilamulira. Nthawi yamasana ndinatulutsa zinthu zanga nditazimanga ngati ndikupita ku ukapolo. Ndipo nthawi yamadzulo ndinabowola khoma ndi manja anga. Pamene chisisira chinkayamba, ndinasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye iwo akuona.
8 Mmawa mwake Yehova anandiyankhula nati:
9 “Iwe mwana wa munthu, kodi anthu aupandu a Israeli sanakufunse kuti ukuchita chiyani?
10 “Uwawuze kuti, ‘zimene ndikunena Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndi izi: Uthengawu ndi wonena za kalonga wa ku Yerusalemu pamodzi ndi banja lonse la Israeli amene akukhala kumeneko.’
11 Uwawuze kuti, ‘Ndiwe chizindikiro chowachenjeza.’ “Zidzakuchitikirani monga momwe zakuchitikira iwemu. Iwo adzatengedwa kupita ku ukapolo.”
12 “Kalonga wawo adzatenga katundu wake nʼchisisira nʼkunyamuka. Adzatulukira pa bowo limene anthu anabowola pa khoma. Adzaphimba nkhope yake kuti asaone kumene akupita.
13 Ndidzayala ukonde wanga pa iye ndi kumukola mu msampha wanga. Ndidzabwera naye ku Babuloni, dziko la Akaldeya, koma sadzaliona dzikolo, ndipo adzafera kumeneko.
14 Ine ndidzabalalitsa kumbali zonse zinayi onse okhala naye pafupi, ndiwo omuthandiza ake pamodzi ndi ankhondo ake. Ndidzawalondola ndi lupanga losolola.
15 “Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira ku mayiko ena.
16 Koma ndidzasiyako ena pangʼono amene adzapulumuke ku lupanga, njala ndi mliri, kuti akafotokoze ntchito zawo zonse zonyansa pakati pa anthu achilendo kumene akupitako. Pamenepo adzadziwa kuti ndine Yehova.”
17 Pambuyo pake Yehova anandiyankhulanso nati,
18 “Iwe mwana wa munthu, uzinjenjemera ukamadya chakudya chako, ndipo uzinthunthumira ndi mantha ukamamwa madzi ako.
19 Uwawuze anthu a mʼdzikomo kuti izi ndi zimene Ambuye Wamphamvuzonse akunena za anthu okhala mu Yerusalemu ndi dziko la Israeli: Iwo adzadya chakudya chawo ndi mantha ndi kumwa madzi awo ndi nkhawa. Zonse za mʼdziko lawo zidzalandidwa chifukwa cha ziwawa za anthu onse okhala mʼmenemo.
20 Mizinda imene ili ndi anthu idzasakazika ndipo dziko lidzasanduka chipululu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
21 Yehova anayankhulanso nane kuti,
22 “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukunenedwa mu Israeli ndi wotani: ‘Masiku akupita koma masomphenya onse sakukwaniritsidwa?’
23 Choncho uwawuze anthuwo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndidzawuthetsa mwambi umenewu ndipo sadzawunenanso mu Israeli.’ Uwawuze kuti, ‘masiku ayandikira oti zonse zimene ndinanena mʼmasomphenya zichitikedi.
24 Pakuti masiku amenewo sikudzakhalanso masomphenya abodza kapena kuwombeza kwa chinyengo pakati pa anthu a Israeli.
25 Koma Ine Ambuye ndidzayankhula chimene ndikufuna, ndipo chidzachitikadi, osachedwa ayi. Pakuti mʼmasiku anu omwe ano, inu anthu opanduka, ndidzakwaniritsa chilichonse chimene ndidzanena. Ndikutero Ine Yehova.’”
26 Yehova anandiyankhula nati:
27 “Iwe mwana wa munthu, Aisraeli akunena kuti, ‘masomphenya amene ukuona sadzachitika kwa zaka zambiri. Iwo akuti ukulosa za zinthu zimene zidzachitika ku tsogolo kwambiri.’
28 “Choncho uwawuze kuti, ‘zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso; chilichonse chimene ndikunena chidzachitikadi. Ndikutero Ine Yehova.’”