< Ezekieli 11 >

1 Pamenepo Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kubwera nane ku chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Kumeneko pa khomo la chipata panali anthu 25, ndipo ndinaona pakati pawo atsogoleri awa: Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya.
Puis l'Esprit m'enleva et me transporta à la porte orientale de la maison de l'Éternel, à celle qui regarde l'Orient; et voici, à l'entrée de la porte vingt-cinq hommes; je vis au milieu d'eux Joazania, fils d'Azzur, et Pélatia, fils de Bénaja, chefs du peuple.
2 Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi anthu amene akukonza zoyipa ndi kupereka malangizo oyipa mu mzindamo.
Et l'Éternel me dit: Fils de l'homme, ce sont là les hommes qui ont des pensées d'iniquité, et qui donnent de mauvais conseils dans cette ville.
3 Iwo amawuza anthu kuti, ‘Nthawi sinafike yoti timange Nyumba? Mzindawu uli ngati mʼphika umene uli pa moto ndipo ife tili ngati nyama mu mʼphikamo.
Ils disent: Ce n'est pas l'heure de bâtir des maisons; cette ville, c'est la chaudière, et nous la viande.
4 Choncho iwe mwana wa munthu, unenere mowadzudzula. Nenera ndithu.’”
C'est pourquoi prophétise contre eux, prophétise, fils de l'homme!
5 Ndipo Mzimu wa Yehova unandigwera ndipo unandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Yehova ndi izi. Iye akuti. ‘Izi ndi zimene mukunena, Inu Aisraeli, koma Ine ndikudziwa zimene zili mu mtima mwanu.’
Et l'Esprit de l'Éternel tomba sur moi, et me dit: Parle; ainsi a dit l'Éternel: Vous parlez de la sorte, maison d'Israël, et ce qui vous monte à l'esprit, je le sais.
6 Mwapha anthu ambiri mu mzinda muno ndipo mwadzaza misewu yake ndi mitembo.
Vous avez multiplié les meurtres dans cette ville, et vous avez rempli ses rues de cadavres.
7 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mitembo imene mwayiponya mʼmisewuyo ndiyo nyama ndipo mzinda uno ndiwo mʼphika, koma Ine ndidzakuthamangitsanimo.
C'est pourquoi, ainsi a dit le Seigneur, l'Éternel: Les morts que vous avez étendus au milieu d'elle, c'est la viande, et elle, la chaudière; mais vous, on vous fera sortir de son sein.
8 Inu mumaopa lupanga, koma lupangalo ndi limene ndidzakubweretsereni, akutero Ambuye.
Vous avez peur de l'épée, mais je ferai venir sur vous l'épée, dit le Seigneur, l'Éternel.
9 Ine ndidzakuthamangitsani mu mzinda ndipo ndidzakuperekani mʼdzanja la alendo kuti akulangeni.
Je vous ferai sortir de cette ville; je vous livrerai entre les mains des étrangers, et j'exécuterai mes jugements contre vous.
10 Mudzaphedwa ndi lupanga ndipo ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Vous tomberez par l'épée, je vous jugerai sur les frontières d'Israël, et vous saurez que je suis l'Éternel.
11 Mzinda uno sudzakhala ngati mʼphika wokutetezani ndipo simudzakhalanso ngati nyama ya mʼmenemo. Ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli.
Cette ville ne sera point pour vous une chaudière dans laquelle vous seriez la chair; c'est sur les frontières d'Israël que je vous jugerai.
12 Ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Inu simunatsatire malangizo anga kapena kusunga malamulo anga koma mwakhala mukutsata zochita za mitundu ina ya anthu imene yakuzungulirani.’”
Et vous saurez que je suis l'Éternel, dont vous n'avez pas observé les statuts, ni gardé les ordonnances; mais vous avez agi d'après les lois des nations qui vous avoisinent.
13 Tsono pamene ndinkanenera, Pelatiya mwana wa Benaya anafa. Pomwepo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba ndipo ndinafuwula ndi mawu aakulu kuti “Mayo, Ambuye Yehova! Kodi mudzawatheratu Aisraeli onse otsala?”
Et, comme je prophétisais, Pélatia, fils de Bénaja, mourut. Alors je tombai sur la face, et m'écriai à haute voix: Ah! Seigneur, Éternel, veux-tu anéantir le reste d'Israël?
14 Yehova anayankhula nane kuti,
Et la parole de l'Éternel me fut adressée en ces mots:
15 “Anthu okhala ku Yerusalemu akuwanena abale ako, anthu a ku ukapolo, onse a banja la Israeli, kuti, ‘Anthu onse amene anatengedwa ukapolo ali kutali ndi Yehova. Dziko lanu Yehova anatipatsa kuti likhale lathulathu.’”
Fils de l'homme, ce sont tes frères, oui, tes frères, les gens de ta parenté et la maison d'Israël tout entière, à qui les habitants de Jérusalem ont dit: Demeurez loin de l'Éternel; c'est à nous que ce pays a été donné en héritage.
16 “Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’
C'est pourquoi dis-leur: Ainsi a dit le Seigneur, l'Éternel: Quoique je les tienne éloignés parmi les nations, quoique je les aie dispersés en divers pays, pourtant je serai pour eux un asile quelque temps dans les pays où ils sont allés.
17 “Nʼchifukwa chake uwawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kuti, Ndidzawasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuwasonkhanitsira pamodzi kuchokera ku mayiko kumene ndinawabalalitsirako. Pambuyo pake ndidzawapatsa dziko la Israeli.
C'est pourquoi dis-leur: Ainsi a dit le Seigneur, l'Éternel: Je vous rassemblerai du milieu des peuples, je vous recueillerai des divers pays où vous êtes dispersés, et je vous donnerai la terre d'Israël.
18 “Akadzalowa mʼdzikomo adzachotsa mafano awo onse oyipa ndi onyansa.
Ils y entreront, et feront disparaître de son sein toutes les idoles et toutes les abominations.
19 Ndidzawapatsa mtima watsopano ndipo ndidzayika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wowuma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzawapatsa mtima wofewa ngati mnofu.
Je leur donnerai un même cœur, et je mettrai en eux un esprit nouveau; j'ôterai de leur chair le cœur de pierre, et je leur donnerai un cœur de chair,
20 Motero adzatsata malamulo anga ndipo adzasunga mosamala malamulo anga. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo.
Afin qu'ils marchent selon mes statuts, qu'ils gardent et observent mes ordonnances; ils seront mon peuple et je serai leur Dieu.
21 Koma kunena za amene akupembedza mafano oyipa ndi onyansa, ndidzawalanga chifukwa cha zimene achita. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
Mais pour ceux dont le cœur marche au gré de leurs idoles et de leurs abominations, je ferai retomber leur conduite sur leur tête, dit le Seigneur, l'Éternel.
22 Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo.
Puis les chérubins déployèrent leurs ailes, les roues s'élevèrent avec eux, ainsi que la gloire du Dieu d'Israël, qui était au-dessus d'eux, tout en haut.
23 Ulemerero wa Yehova unakwera ndi kusiya mzindawo ndipo unakayima pa phiri cha kummawa kwake kwa mzindawo.
Et la gloire de l'Éternel s'éleva du milieu de la ville, et s'arrêta sur la montagne qui est à l'Orient de la ville.
24 Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kukandifikitsa. Zimenezi zinkachitika mʼmasomphenya monga mmene Mzimu wa Mulungu unkandionetsera. Kenaka masomphenya amene ndinkawaonawo anayamba kuzimirira.
L'Esprit m'enleva et me transporta en vision, par l'Esprit de Dieu, en Caldée auprès de ceux de la captivité, et la vision que j'avais vue disparut de devant moi.
25 Ndipo ndinafotokozera akapolowo zonse zimene Yehova anandionetsa.
Alors je racontai à ceux qui avaient été emmenés captifs, toutes les choses que l'Éternel m'avait révélées.

< Ezekieli 11 >