< Eksodo 8 >
1 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Ukamuwuze Farao kuti, Lolani anthu anga kuti apite, akandipembedze.
Poi il Signore disse a Mosè: «Và a riferire al faraone: Dice il Signore: Lascia andare il mio popolo perché mi possa servire!
2 Ndipo ngati simulola kuti apite Ine ndidzalanga dziko lonse la Igupto polidzaza ndi achule.
Se tu rifiuti di lasciarlo andare, ecco, io colpirò tutto il tuo territorio con le rane:
3 Mtsinje wa Nailo udzadzaza ndi achule. Achulewo adzatuluka ndi kukalowa mʼnyumba yaufumu, ku chipinda chogona ndi pa bedi lako, mʼnyumba za nduna zako ndi pa anthu ako ndi mophikira buledi ndiponso mopangira bulediyo.
il Nilo comincerà a pullulare di rane; esse usciranno, ti entreranno in casa, nella camera dove dormi e sul tuo letto, nella casa dei tuoi ministri e tra il tuo popolo, nei tuoi forni e nelle tue madie.
4 Achulewo adzakulumphira iwe ndi anthu ako ndiponso nduna zako.”
Contro di te e contro tutti i tuoi ministri usciranno le rane».
5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Loza ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Igupto.’”
Il Signore disse a Mosè: «Comanda ad Aronne: Stendi la mano con il tuo bastone sui fiumi, sui canali e sugli stagni e fà uscire le rane sul paese d'Egitto!».
6 Kotero Aaroni analoza dzanja lake pa madzi a ku Igupto, ndipo achule anatuluka nadzaza dziko lonse la Igupto.
Aronne stese la mano sulle acque d'Egitto e le rane uscirono e coprirono il paese d'Egitto.
7 Koma amatsenga anachita zinthu zomwezo mʼmatsenga awo. Iwonso anatulutsa achule mʼdziko lonse la Igupto.
Ma i maghi, con le loro magie, operarono la stessa cosa e fecero uscire le rane sul paese d'Egitto.
8 Kenaka, Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Pemphera kwa Yehova kuti achulewa achoke kwa ine ndi anthu anga, ndipo ine ndidzalola kuti anthu anu apite kukapereka nsembe kwa Yehova.”
Il faraone fece chiamare Mosè e Aronne e disse: «Pregate il Signore, perché allontani le rane da me e dal mio popolo; io lascerò andare il popolo, perché possa sacrificare al Signore!».
9 Mose anati kwa Farao, “Inu mungonditchulira nthawi imene mukufuna kuti ndikupempherereni, nduna zanu pamodzi ndi anthu anu kuti achule achoke mʼnyumba zanu ndi kuti atsale okhawo ali mu mtsinje wa Nailo.”
Mosè disse al faraone: «Fammi l'onore di comandarmi per quando io devo pregare in favore tuo e dei tuoi ministri e del tuo popolo, per liberare dalle rane te e le tue case, in modo che ne rimangano soltanto nel Nilo».
10 Farao anati, “Mawa.” Mose anamuyankha kuti, “Chabwino zidzakhala monga mwaneneramu, kuti mudzadziwe kuti palibe wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu.
Rispose: «Per domani». Riprese: «Secondo la tua parola! Perché tu sappia che non esiste nessuno pari al Signore, nostro Dio,
11 Achule adzachoka mʼnyumba yanu, mʼnyumba za nduna zanu pamodzi ndi za anthu anu. Koma adzatsala mu mtsinje wa Nailo basi.”
le rane si ritireranno da te e dalle tue case, dai tuoi servitori e dal tuo popolo: ne rimarranno soltanto nel Nilo».
12 Mose ndi Aaroni anachoka, ndipo Mose anapemphera kwa Yehova kuti achotse achule amene anatumiza kwa Farao.
Mosè e Aronne si allontanarono dal faraone e Mosè supplicò il Signore riguardo alle rane, che aveva mandate contro il faraone.
13 Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha. Achule amene anali mʼnyumba, mʼmabwalo ndi mʼminda anafa
Il Signore operò secondo la parola di Mosè e le rane morirono nelle case, nei cortili e nei campi.
14 Aigupto anawunjika achulewo milumilu ndipo dziko linanunkha.
Le raccolsero in tanti mucchi e il paese ne fu ammorbato.
15 Koma Farao ataona kuti zinthu zinayambanso kukhala bwino, anawumitsanso mtima wake ndipo sanamverenso mawu a Mose ndi Aaroni, monga momwe Yehova ananenera.
Ma il faraone vide ch'era intervenuto il sollievo, si ostinò e non diede loro ascolto, secondo quanto aveva predetto il Signore.
16 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti akweze ndodo yake ndi kumenya fumbi la pa nthaka, ndipo fumbilo lidzasanduka nsabwe pa dziko lonse la Igupto.”
Quindi il Signore disse a Mosè: «Comanda ad Aronne: Stendi il tuo bastone, percuoti la polvere della terra: essa si muterà in zanzare in tutto il paese d'Egitto».
17 Iwo anachita momwemo, ndipo pamene Aaroni anakweza ndodo yake ndi kumenya fumbi, nsabwe zinafika pa munthu aliyense ndi pa ziweto. Fumbi lonse la mʼdziko la Igupto linasanduka nsabwe.
Così fecero: Aronne stese la mano con il suo bastone, colpì la polvere della terra e infierirono le zanzare sugli uomini e sulle bestie; tutta la polvere del paese si era mutata in zanzare in tutto l'Egitto.
18 Koma amatsenga atayesa kupanga nsabwe mwa matsenga awo, analephera. Ndipo nsabwezo zinali pa munthu aliyense ndi pa ziweto zawo.
I maghi fecero la stessa cosa con le loro magie, per produrre zanzare, ma non riuscirono e le zanzare infierivano sugli uomini e sulle bestie.
19 Amatsenga anati kwa Farao, “Izi wachita ndi Mulungu.” Koma mtima wa Farao unali wowumabe ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananenera.
Allora i maghi dissero al faraone: «E' il dito di Dio!». Ma il cuore del faraone si ostinò e non diede ascolto, secondo quanto aveva predetto il Signore.
20 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze.
Poi il Signore disse a Mosè: «Alzati di buon mattino e presentati al faraone quando andrà alle acque; gli riferirai: Dice il Signore: Lascia partire il mio popolo, perché mi possa servire!
21 Koma ngati suwalola anthu anga kuti apite, Ine ndidzatumiza pa iwe ntchentche zoluma ndi pa nduna zako ndi anthu ako ndi mʼnyumba zanu. Mʼnyumba za Aigupto mudzadzaza ntchentche zoluma. Ngakhale pa nthaka pamene akhalapo padzadzaza ndi ntchentche zoluma.’”
Se tu non lasci partire il mio popolo, ecco manderò su di te, sui tuoi ministri, sul tuo popolo e sulle tue case i mosconi: le case degli Egiziani saranno piene di mosconi e anche il suolo sul quale essi si trovano.
22 “Koma pa tsikulo ndidzapatula dera la Goseni, kumene kumakhala anthu anga, motero kuti sikudzakhala ntchentche zoluma. Choncho iwe udzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndikulamulira dziko lino.
Ma in quel giorno io eccettuerò il paese di Gosen, dove dimora il mio popolo, in modo che là non vi siano mosconi, perché tu sappia che io, il Signore, sono in mezzo al paese!
23 Ndidzasiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako. Chizindikiro chozizwitsa ichi chidzachitika mawa.”
Così farò distinzione tra il mio popolo e il tuo popolo. Domani avverrà questo segno».
24 Ndipo Yehova anachita zimenezi: Ntchentche zoluma zochuluka zinalowa mʼnyumba yaufumu ya Farao ndi nyumba za nduna zake. Choncho ntchentche zolumazi zinawononga dziko lonse la Igupto.
Così fece il Signore: una massa imponente di mosconi entrò nella casa del faraone, nella casa dei suoi ministri e in tutto il paese d'Egitto; la regione era devastata a causa dei mosconi.
25 Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kaperekeni nsembe kwa Mulungu wanu mʼdziko lomwe lino.”
Il faraone fece chiamare Mosè e Aronne e disse: «Andate a sacrificare al vostro Dio nel paese!».
26 Koma Mose anati, “Sitingathe kutero pakuti nsembe zathu kwa Yehova Mulungu ndi zowayipira Aigupto. Ngati tipereke nsembe zowayipira Aigupto mʼmaso mwawo, adzatiponya miyala kuti tife.
Ma rispose Mosè: «Non è opportuno far così perché quello che noi sacrifichiamo al Signore, nostro Dio, è abominio per gli Egiziani. Se noi facciamo un sacrificio abominevole agli Egiziani sotto i loro occhi, forse non ci lapideranno?
27 Ife tiyenera kuyenda ulendo wa masiku atatu kupita ku chipululu kukapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wathu monga anatilamulira.”
Andremo nel deserto, a tre giorni di cammino, e sacrificheremo al Signore, nostro Dio, secondo quanto egli ci ordinerà!».
28 Farao anati, “Ine ndikulolani kuti mupite ku chipululu kukapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu, koma musapite kutali kwambiri. Tsopano ndipempherereni.”
Allora il faraone replicò: «Vi lascerò partire e potrete sacrificare al Signore nel deserto. Ma non andate troppo lontano e pregate per me».
29 Mose anayankha kuti, “Ine ndikangochoka pano, ndikapemphera kwa Yehova ndipo mawa lomweli ntchentche zoluma zidzachoka kwa Farao, nduna zake pamodzi ndi anthu ake. Koma Farao, onetsetsani kuti musachitenso zachinyengo ndi kuwakaniza anthu kuti asakapereke nsembe kwa Yehova.”
Rispose Mosè: «Ecco, uscirò dalla tua presenza e pregherò il Signore; domani i mosconi si ritireranno dal faraone, dai suoi ministri e dal suo popolo. Però il faraone cessi di burlarsi di noi, non lasciando partire il popolo, perché possa sacrificare al Signore!».
30 Choncho Mose anasiyana ndi Farao nakapemphera kwa Yehova.
Mosè si allontanò dal faraone e pregò il Signore.
31 Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha: Ntchentche zoluma zinachoka kwa Farao ndi nduna zake ndiponso kwa anthu ake. Palibe ngakhale imodzi yomwe inatsala.
Il Signore agì secondo la parola di Mosè e allontanò i mosconi dal faraone, dai suoi ministri e dal suo popolo: non ne restò neppure uno.
32 Koma nthawi imeneyinso Farao anawumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti anthu atuluke.
Ma il faraone si ostinò anche questa volta e non lasciò partire il popolo.