< Eksodo 40 >
1 Kenaka Yehova anati kwa Mose,
2 “Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi.
3 Uyikemo bokosi la umboni ndipo uphimbe bokosilo ndi katani.
4 Ulowetsemo tebulo ndi kuyika zimene zimakhala pamenepo. Kenaka ulowetse choyikapo nyale ndipo uyikepo nyale zake.
5 Uyike guwa lofukiza la golide patsogolo pa bokosi la umboni ndipo uyike katani ya pa chipata cha chihema.
6 “Uyike guwa lansembe yopsereza patsogolo pa chipata cha chihema, tenti ya msonkhano.
7 Uyike beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uyikemo madzi.
8 Upange bwalo lozungulira chihemacho ndipo uyike katani ya pa chipata cha bwalolo.
9 “Utenge mafuta wodzozera ndipo udzoze chihema ndi chilichonse chili mʼmenemo ndipo zidzakhala zoyeretsedwa.
10 Kenaka udzoze guwa lansembe lopsereza ndi ziwiya zake zonse. Ulipatule guwalo ndipo lidzakhala loyera kwambiri.
11 Udzoze beseni ndi miyendo yake ndipo uzipatule.
12 “Ubwere ndi Aaroni ndi ana ake pa chipata cha tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi.
13 Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe.
14 Ubweretse ana ake ndipo uwaveke minjiro.
15 Uwadzoze monga momwe unadzozera abambo awo, kotero kuti anditumikire monga ansembe. Kudzozedwako kudzakhala unsembe wawo pa mibado ndi mibado”
16 Mose anachita zonse monga Yehova anamulamulira.
17 Kotero anayimika chihema tsiku loyamba la mwezi woyamba mʼchaka chachiwiri.
18 Nthawi imene Mose anayimika chihema, anayika matsinde mʼmalo ake, kuyimitsa maferemu, kulowetsa mitanda ndi kuyika nsichi.
19 Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose.
20 Iye anatenga miyala ya umboni nayika mʼbokosi lija ndi kuyika chivundikiro pamwamba pake.
21 Kenaka analowetsa bokosilo mʼchihema ndipo anapachika katani ndi kubisa bokosi la umboni monga momwe Yehova analamulira iye.
22 Mose anayika tebulo mu tenti ya msonkhano kumpoto kwa chihema, kunja kwa katani,
23 ndipo anayikapo buledi pamaso pa Yehova, monga momwe Yehova analamulira Mose.
24 Iye anayikanso choyikapo nyale mu tenti ya msonkhano moyangʼanana ndi tebulo mbali yakummwera kwa chihema.
25 Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose.
26 Mose anayika guwa la golide mu tenti ya msonkhano patsogolo pa katani
27 ndipo anapserezapo lubani wonunkhira monga Yehova anamulamulira.
28 Kenaka anayika katani ya pa chipata cha chihema.
29 Iye anayika guwa lansembe yopsereza pafupi ndi chipata cha chihema, tenti ya msonkhano, ndipo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya ufa monga Yehova anamulamulira.
30 Iye anayika beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo anathiramo madzi wosamba,
31 ndipo Mose, Aaroni ndi ana ake amasamba manja ndi mapazi awo.
32 Iwo amasamba nthawi zonse akamalowa mu tenti ya msonkhano kapena kuyandikira guwa lansembe monga Yehova analamulira Mose.
33 Kenaka Mose anamanga bwalo kuzungulira chihema ndi guwa lansembe ndipo anayika katani ya pa chipata cha bwalo. Kotero Mose anamaliza ntchito.
34 Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.
35 Mose sanathe kulowa mu tenti ya msonkhano chifukwa mtambo unali utakhazikika pa chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.
36 Pa maulendo awo onse, mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso pamene analipo.
37 Koma ngati mtambo sunachoke, iwo sankasamukanso mpaka tsiku limene udzachoke.
38 Kotero mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema usana, ndi mtambo wamoto umakhala usiku, pamaso pa nyumba yonse ya Israeli pa masiku onse aulendo wawo.