< Eksodo 4 >
1 Mose anayankha, “Aisraeliwo sakandikhulupirira ndipo sakandimvera. Iwowo adzati, ‘Yehova sanakuonekere iwe.’”
摩西回答說:「他們必不信我,也不聽我的話,必說:『耶和華並沒有向你顯現。』」
2 Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?” Mose anayankha kuti, “Ndodo.”
耶和華對摩西說:「你手裏是甚麼?」他說:「是杖。」
3 Yehova anati, “Tayiponya pansi.” Mose anayiponya pansi ndipo inasanduka njoka ndipo anayithawa.
耶和華說:「丟在地上。」他一丟下去,就變作蛇;摩西便跑開。
4 Kenaka Yehova anati kwa iye, “Igwire mtchira.” Ndipo Mose anayigwira mchira njokayo ndipo inasandukanso ndodo mʼdzanja lake.
耶和華對摩西說:「伸出手來,拿住牠的尾巴,牠必在你手中仍變為杖;
5 Yehova anati, “Ukachite zimenezi ndipo akakukhulupirira kuti Yehova, Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo, wakuonekera iwe.”
如此好叫他們信耶和華-他們祖宗的上帝,就是亞伯拉罕的上帝,以撒的上帝,雅各的上帝,是向你顯現了。」
6 Yehova anatinso, “Pisa dzanja lako mʼmalaya akowo.” Choncho Mose anapisa dzanja lake mʼmalaya ake ndipo pamene analitulutsa, linali la khate kuchita kuti mbuu ngati ufa.
耶和華又對他說:「把手放在懷裏。」他就把手放在懷裏,及至抽出來,不料,手長了大痲瘋,有雪那樣白。
7 Yehova anati, “Tsopano pisanso dzanja lako mʼmalaya.” Mose anapisanso dzanja lakelo mʼmalaya ake ndipo atalitulutsa, linali labwinobwino, ngati thupi lake lonse.
耶和華說:「再把手放在懷裏。」他就再把手放在懷裏,及至從懷裏抽出來,不料,手已經復原,與周身的肉一樣;
8 Tsono Yehova anati “Akakapanda kukukhulupirira, osalabadira chozizwitsa choyambacho, akakhulupirira ndithu chifukwa cha chozizwitsa chachiwiricho.
又說:「倘或他們不聽你的話,也不信頭一個神蹟,他們必信第二個神蹟。
9 Koma ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwiri izi kapena kukumvera, ukatunge madzi a mu mtsinje wa Nailo ndi kuwathira pa mtunda powuma ndipo madziwo adzasanduka magazi.”
這兩個神蹟若都不信,也不聽你的話,你就從河裏取些水,倒在旱地上,你從河裏取的水必在旱地上變作血。」
10 Mose anati kwa Yehova, “Chonde Ambuye, chikhalire ine ndakhala munthu wosatha kuyankhula bwino. Ngakhale tsopano pamene mukundiyankhula, lilime langa ndi lolemera. Ndine wachibwibwi.”
摩西對耶和華說:「主啊,我素日不是能言的人,就是從你對僕人說話以後,也是這樣。我本是拙口笨舌的。」
11 Yehova anati kwa iye, “Kodi anapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosayankhula kapena wosamva? Ndani amapanga munthu kukhala wopenya kapena wosaona? Kodi si Ine Yehova?
耶和華對他說:「誰造人的口呢?誰使人口啞、耳聾、目明、眼瞎呢?豈不是我-耶和華嗎?
12 Tsopano pita, Ine ndidzakuthandiza kuyankhula ndipo ndidzakulangiza zoti ukanene.”
現在去吧,我必賜你口才,指教你所當說的話。」
13 Koma Mose anati, “Chonde Ambuye, pepani, tumani wina kuti akachite zimenezi.”
摩西說:「主啊,你願意打發誰,就打發誰去吧!」
14 Kenaka Yehova anamupsera mtima Mose ndipo anati, “Kodi suli ndi mʼbale wako Aaroni wa fuko la Levi? Ine ndikudziwa kuti iye amayankhula bwino. Iye wanyamuka kale kudzakumana nawe ndipo adzasangalala akadzakuona.
耶和華向摩西發怒說:「不是有你的哥哥利未人亞倫嗎?我知道他是能言的;現在他出來迎接你,他一見你,心裏就歡喜。
15 Iwe udzayankhula naye ndi kumuwuza mawu oti akanene. Ine ndidzakuthandizani kuyankhula nonse awirinu ndi kukulangizani zoti mukachite.
你要將當說的話傳給他;我也要賜你和他口才,又要指教你們所當行的事。
16 Iye akayankhula kwa anthu mʼmalo mwako. Iye adzakhala wokuyankhulira ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu kwa iye.
他要替你對百姓說話;你要以他當作口,他要以你當作上帝。
17 Koma utenge ndodo imene ili mʼdzanja lakoyo kuti ukachite nayo zizindikiro zozizwitsa.”
你手裏要拿這杖,好行神蹟。」
18 Tsono Mose anabwerera kwa Yetero, mpongozi wake ndipo anati kwa Iye, “Chonde ndiloleni kuti ndibwerere ku Igupto kwa anthu anga kuti ndikaone ngati ali moyo.” Yeteri anati, “Pitani mu mtendere.”
於是,摩西回到他岳父葉忒羅那裏,對他說:「求你容我回去見我在埃及的弟兄,看他們還在不在。」葉忒羅對摩西說:「你可以平平安安地去吧!」
19 Nthawiyi Yehova anali atamuwuza kale Mose ku Midiyani kuti, “Bwerera ku Igupto, pakuti anthu onse amene amafuna kukupha aja anamwalira.”
耶和華在米甸對摩西說:「你要回埃及去,因為尋索你命的人都死了。」
20 Kotero Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, ndipo anawakweza pa bulu nayamba ulendo wobwerera ku Igupto. Ndipo anatenga ndodo ya Mulungu ija mʼdzanja lake.
摩西就帶着妻子和兩個兒子,叫他們騎上驢,回埃及地去。摩西手裏拿着上帝的杖。
21 Yehova anati kwa Mose, “Ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao zodabwitsa zonse zimene ndayika mphamvu mwa iwe kuti ukachite. Koma Ine ndidzawumitsa mtima wake kotero kuti sadzalola anthuwo kuti apite.
耶和華對摩西說:「你回到埃及的時候,要留意將我指示你的一切奇事行在法老面前。但我要使他的心剛硬,他必不容百姓去。
22 Ndipo iwe ukati kwa Farao, ‘Yehova akuti, Israeli ali ngati mwana wanga wachisamba.’
你要對法老說:『耶和華這樣說:以色列是我的兒子,我的長子。
23 Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’”
我對你說過:容我的兒子去,好事奉我。你還是不肯容他去。看哪,我要殺你的長子。』」
24 Pambuyo pake Mose ali mʼnjira, pamalo wogona, Yehova anakumana naye, ndipo anafuna kumupha.
摩西在路上住宿的地方,耶和華遇見他,想要殺他。
25 Koma Zipora anatenga mwala wakuthwa nachita mdulidwe mwana wake ndipo khungulo analikhudzitsa pa mapazi a Mose. Iye anati “Zoonadi, kwa ine ndiwe mkwati wamagazi.”
西坡拉就拿一塊火石,割下他兒子的陽皮,丟在摩西腳前,說:「你真是我的血郎了。」
26 Choncho Yehova anamuleka Mose wosamupha. Pa nthawiyo, Zipora anati, “Mkwati wa magazi,” ponena za mdulidwe.
這樣,耶和華才放了他。西坡拉說:「你因割禮就是血郎了。」
27 Yehova anati kwa Aaroni, “Pita ku chipululu ukakumane ndi Mose.” Iye anapitadi nakakumana ndi Mose pa phiri la Mulungu namupsompsona.
耶和華對亞倫說:「你往曠野去迎接摩西。」他就去,在上帝的山遇見摩西,和他親嘴。
28 Kenaka Mose anamufotokozera Aaroni chilichonse chimene Yehova anamutuma kuti akanene. Anamufotokozera za zizindikiro zozizwitsa zimene anamulamulira kuti akazichite.
摩西將耶和華打發他所說的言語和囑咐他所行的神蹟都告訴了亞倫。
29 Mose ndi Aaroni anapita kukasonkhanitsa pamodzi akuluakulu onse a Aisraeli.
摩西、亞倫就去招聚以色列的眾長老。
30 Ndipo Aaroni anawafotokozera zonse zimene Yehova ananena kwa Mose. Anachita zizindikirozo pamaso pa anthu onse,
亞倫將耶和華對摩西所說的一切話述說了一遍,又在百姓眼前行了那些神蹟,
31 ndipo anakhulupirira. Iwo atamva kuti Yehova anadzawayendera ndi kuti waona mmene akuzunzikira, anaweramitsa mitu pansi napembedza.
百姓就信了。以色列人聽見耶和華眷顧他們,鑒察他們的困苦,就低頭下拜。