< Eksodo 39 >

1 Anapanga zovala za ansembe, zovala potumikira ku malo wopatulika pogwiritsa ntchito nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira. Anapanganso zovala zopatulika za Aaroni monga momwe Yehova analamulira Mose.
Y del cárdeno, y púrpura, y carmesí, hicieron las vestiduras del ministerio para ministrar en el santuario; y asimismo hicieron las santas vestiduras que eran para Aarón, como Jehová lo mandó a Moisés.
2 Popanga efodi, iwo anagwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yosalala yofewa.
Hizo también el efod de oro, cárdeno, y púrpura, y carmesí, y lino torcido.
3 Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso.
Y extendieron las planchas de oro, y cortaron los hilos para tejer entre el cárdeno, y entre la púrpura, y entre el carmesí, y entre el lino, por obra de artífice.
4 Iwo anapanga efodi imene inali ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa, tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga.
Hiciéronle los espaldares que se juntasen, y juntábanse en sus dos lados.
5 Lamba womangira efodi anali wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Anali nsalu imodzi ndi efodiyo, wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala, monga momwe Yehova analamulira Mose.
Y el cinto del efod, que estaba sobre él, era de lo mismo, conforme a su obra de oro, cárdeno, y púrpura, y carmesí, y lino torcido, como Jehová lo había mandado a Moisés.
6 Iwo anakonza miyala ya onikisi ndi kuyiika mu zoyikamo zake zagolide ndipo anazokota mayina a ana a Israeli monga amachitira pa chidindo.
Y labraron las piedras oniquinas cercadas de engastes de oro, grabadas de grabadura de sello con los nombres de los hijos de Israel:
7 Kenaka anayimangirira pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli monga momwe Yehova analamulira Mose.
Y púsolas sobre las hombreras del efod, por piedras de memoria a los hijos de Israel, como Jehová lo había mandado a Moisés.
8 Iwo anapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri. Anachipanga ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino.
Hizo también el pectoral de obra de artífice, como la obra del efod, de oro, cárdeno, y púrpura, y carmesí, y lino torcido.
9 Kutalika kwake kunali kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, chinali chopinda pawiri.
Era cuadrado: doblado hicieron el pectoral, su longura era de un palmo, y de otro palmo su anchura, doblado.
10 Kenaka anayikapo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba anayika miyala ya rubi, topazi ndi berili;
Y engastaron en él cuatro ordenes de piedras. El orden era un rubí, una esmeralda, y una crisólita, el primer orden.
11 mzere wachiwiri anayikapo miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi;
El segundo orden, un carbunclo, un zafiro, y un diamante.
12 mzere wachitatu anayikapo miyala ya opera, agate ndi ametisiti;
El tercer orden, un topacio, una turquesa, y un ametisto.
13 mzere wachinayi anayikapo miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi anayiyika mu zoyikamo zagolide.
Y el cuarto orden, un tarsis, un ónix, y un jaspe, cercadas y engastadas en sus engastes de oro.
14 Miyalayo inalipo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse unazokotedwa ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli.
Las cuales piedras eran conforme a los nombres de los hijos de Israel doce, conforme a los nombres de ellos, de grabadura de sello, cada una conforme a su nombre, según las doce tribus.
15 Anapanga timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe.
Hicieron también sobre el pectoral las cadenas pequeñas de hechura de trenza, de oro puro.
16 Anapanganso zoyikamo zake zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anamangirira mphetezo pa ngodya ziwiri za chovala chapachifuwa.
Hicieron asimismo los dos engastes, y las dos sortijas de oro, las cuales dos sortijas de oro pusieron en los dos cabos del pectoral.
17 Anamangirira timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho.
Y pusieron las dos trenzas de oro en aquellas dos sortijas en los cabos del pectoral.
18 Ndipo mbali ina ya timaunyoloto anamangirira pa zoyikapo zake ziwiri zija, ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi.
Y los dos cabos de las dos trenzas pusieron en los dos engastes, los cuales pusieron sobre las hombreras del efod en la parte delantera de él.
19 Anapanganso mphete ziwiri zagolide ndipo analumikiza ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija.
E hicieron otras dos sortijas de oro, que pusieron en los dos cabos del pectoral en su orilla a la parte baja del efod.
20 Kenaka anapanga mphete zina ziwiri zagolide ndi kuzilumikiza kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi.
Hicieron más otras dos sortijas de oro, las cuales pusieron en las dos hombreras del efod abajo en la parte delantera, delante de su juntura sobre el cinto del efod.
21 Anamangirira mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi ija monga Yehova analamulira Mose.
Y ataron el pectoral de sus sortijas a las sortijas del mismo efod con un cordón de cárdeno, para que estuviese sobre el cinto del mismo efod, y el pectoral no se apartase del efod, como Jehová lo había mandado a Moisés.
22 Anayipangira efodiyo mkanjo wamtundu wa mtambo, wolukidwa ndi mmisiri waluso.
Hizo también el manto del efod de obra de tejedor todo de cárdeno.
23 Mkanjowo unali ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo panali chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike.
Con su collar en medio de él, como el collar de un coselete, con un borde al rededor del collar, porque no se rompiese.
24 Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, analumikiza mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yofewa yosalala ndi yopetedwa bwino yomwe inazungulira mkanjo.
E hicieron en las orillas del manto las granadas de cárdeno, y púrpura, y carmesí, y lino torcido.
25 Ndipo anapanga maberu agolide wabwino kwambiri ndipo analumikiza mozungulira mpendero pakati pa makangadzawo.
Hicieron también las campanillas de oro puro, las cuales campanillas pusieron entre las granadas por las orillas del manto al derredor, entre las granadas.
26 Kotero panali mphonje imodzi ndi belu limodzi kuzungulira mpendero wa mkanjo wovala potumikira monga momwe Yehova analamulira Mose.
Una campanilla y una granada, una campanilla y una granada, en las orillas del manto, al rededor, para ministrar, como Jehová lo mandó a Moisés.
27 Kwa Aaroni ndi ana ake anawapangira minjiro ya nsalu yofewa yosalala, yolukidwa bwino ndi munthu waluso,
E hicieron las túnicas de lino fino de obra de tejedor para Aarón, y para sus hijos.
28 nduwira ya nsalu yofewa yosalala, lamba wa nsalu yofewa yosalala, womanga mʼmutu, ndi makabudula amʼkati a nsalu yofewa yosalala olukidwa bwino.
Asimismo la mitra de lino fino, y las orladuras de los chapeos de lino fino, y los pañetes de lino, de lino torcido.
29 Anapanga lamba wolukidwa bwino wa nsalu yofewa ndi yosalala ya mtundu wa mtambo yapepo ndi yofiira. Ili linaliluso la munthu wopanga zokometsera monga Yehova analamulira Mose.
Ítem, el cinto de lino torcido, y de cárdeno, y púrpura, y carmesí, de obra de recamador, como Jehová lo mandó a Moisés.
30 Iwo anapanga duwa lagolide wabwino kwambiri ngati chidindo ndipo anazokotapo mawu akuti, Wopatulikira Yehova.
Ítem, hicieron la plancha, la corona de la santidad, de oro puro, y escribieron en ella de grabadura de sello el rotulo, Santidad a Jehová.
31 Kenaka analimangira ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira, monga momwe Yehova analamulira Mose.
Y pusieron sobre ella un cordón de cárdeno para ponerla sobre la mitra encima, como Jehová lo había mandado a Moisés.
32 Tsopano ntchito yonse ya tenti ya msonkhano inatha. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose.
Y fue acabada toda la obra del tabernáculo, del tabernáculo del testimonio. E hicieron los hijos de Israel como Jehová lo había mandado a Moisés: así lo hicieron.
33 Kenaka anabweretsa chihema kwa Mose. Tenti ndi zipangizo zake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake;
Y trajeron el tabernáculo a Moisés; el tabernáculo y todos sus vasos, sus corchetes, sus tablas, sus barras, y sus columnas y sus basas,
34 chophimba cha chikopa cha nkhosa yayimuna chonyikidwa mu utoto ofiira, chophimba cha chikopa cha akatumbu ndi nsalu zophimba;
Y la cobertura de pieles rojas de carneros, y la cobertura de pieles de tejones, y el velo del pabellón,
35 bokosi la umboni pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake;
El arca del testimonio, y sus barras, y la cubierta,
36 tebulo pamodzi ndi zipangizo zake ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova;
La mesa, todos sus vasos, y el pan de la proposición,
37 choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri pamodzi ndi nyale zake ndi zipangizo zake zonse, ndiponso mafuta anyalezo;
El candelero limpio, sus candilejas, las candilejas de la ordenanza, y todos sus vasos, y el aceite de la luminaria,
38 guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani onunkhira ndi nsalu yotchinga pa khomo lolowera mu tenti;
Y el altar de oro, y el aceite de la unción, y el perfume aromático, y el pabellón para la puerta del tabernáculo,
39 guwa lamkuwa ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse; beseni ndi miyendo yake;
El altar de metal, y su criba de metal, sus barras, y todos sus vasos, y la fuente y su basa,
40 nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; zingwe zake ndi zikhomo za tenti; zipangizo zonse za chihema, tenti ya msonkhano;
Las cortinas del patio, y sus columnas y sus basas, y el pabellón para la puerta del patio, y sus cuerdas, y sus estacas, y todos los vasos del servicio del tabernáculo, del tabernáculo del testimonio,
41 ndiponso zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.
Las vestiduras del servicio para ministrar en el santuario, las santas vestiduras para Aarón el sacerdote, y las vestiduras de sus hijos para ministrar en el sacerdocio.
42 Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose.
Conforme a todas las cosas que Jehová había mandado a Moisés, así hicieron los hijos de Israel toda la obra.
43 Mose anayendera ntchitoyo ndipo anaona kuti anayichita monga momwe Yehova analamulira. Kotero Mose anawadalitsa.
Y vio Moisés toda la obra, y he aquí que la habían hecho como Jehová había mandado; y bendíjolos.

< Eksodo 39 >