< Eksodo 32 >

1 Anthu ataona kuti Mose akuchedwa kutsika mʼphiri, anasonkhana kwa Aaroni ndipo anati, “Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.”
Когда народ увидел, что Моисей долго не сходит с горы, то собрался к Аарону и сказал ему: встань и сделай нам бога, который бы шел перед нами, ибо с этим человеком, с Моисеем, который вывел нас из земли Египетской, не знаем, что сделалось.
2 Aaroni anawayankha kuti, “Vulani ndolo zagolide zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi aakazi ndipo muzibweretse kwa ine.”
И сказал им Аарон: выньте золотые серьги, которые в ушах ваших жен, ваших сыновей и ваших дочерей, и принесите ко мне.
3 Kotero anthu onse anavula ndolo zagolide ndi kubwera nazo kwa Aaroni.
И весь народ вынул золотые серьги из ушей своих и принесли к Аарону.
4 Choncho Aaroni analandira golideyo ndipo anamuwumba ndi chikombole ndi kupanga fano la mwana wangʼombe. Kenaka anthu aja anati, “Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.”
Он взял их из рук их, и сделал из них литого тельца, и обделал его резцом. И сказали они: вот бог твой, Израиль, который вывел тебя из земли Египетской!
5 Aaroni ataona izi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa mwana wangʼombeyo ndipo analengeza kuti, “Mawa kudzakhala chikondwerero cha Yehova.”
Увидев сие, Аарон поставил пред ним жертвенник, и провозгласил Аарон, говоря: завтра праздник Господу.
6 Kotero tsiku linalo anthu anadzuka mmamawa ndithu ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Atatha kupereka nsembezo, anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.
На другой день они встали рано и принесли всесожжения и привели жертвы мирные: и сел народ есть и пить, а после встал играть.
7 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, “Tsika msanga, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto aja adziyipitsa kwambiri.
И сказал Господь Моисею: поспеши сойти отсюда, ибо развратился народ твой, который ты вывел из земли Египетской;
8 Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, ‘Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’”
скоро уклонились они от пути, который Я заповедал им: сделали себе литого тельца и поклонились ему, и принесли ему жертвы и сказали: вот бог твой, Израиль, который вывел тебя из земли Египетской!
9 Yehova anati kwa Mose, “Ine ndikuwadziwa anthu amenewa. Iwowa ndi ankhutukumve.
И сказал Господь Моисею: Я вижу народ сей, и вот, народ он - жестоковыйный;
10 Chifukwa chake undileke kuti mkwiyo wanga uyake pa iwo ndi kuwawononga. Ndipo Ine ndidzakusandutsa kuti ukhale mtundu waukulu.”
итак оставь Меня, да воспламенится гнев Мой на них, и истреблю их, и произведу многочисленный народ от тебя.
11 Koma Mose anapempha chifundo cha Mulungu wake ndipo anati, “Chonde Yehova, chifukwa chiyani mwakwiyira anthu awa amene munawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu.
Но Моисей стал умолять Господа, Бога своего, и сказал: да не воспламеняется, Господи, гнев Твой на народ Твой, который Ты вывел из земли Египетской силою великою и рукою крепкою,
12 Kodi mukufuna kuti Aigupto azinena kuti, ‘Munali ndi cholinga choyipa chofuna kuwaphera ku mapiri kuno ndi kuwawonongeratu pa dziko lapansi pamene munkawatulutsa ku Igupto kuja?’ Ayi, chonde mkwiyo wanu woyaka ngati motowu ubwezeni ndipo sinthani maganizo ofunira zoyipa anthu anu.
чтобы Египтяне не говорили: на погибель Он вывел их, чтобы убить их в горах и истребить их с лица земли; отврати пламенный гнев Твой и отмени погубление народа Твоего;
13 Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, ‘Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’”
вспомни Авраама, Исаака и Израиля Иакова, рабов Твоих, которым клялся Ты Собою, говоря: умножая умножу семя ваше, как звезды небесные, и всю землю сию, о которой Я сказал, дам семени вашему, и будут владеть ею вечно.
14 Choncho Yehova analeka ndipo sanawachitire choyipa anthu ake monga anaopsezera.
И отменил Господь зло, о котором сказал, что наведет его на народ Свой.
15 Mose anatembenuka ndi kutsika phiri miyala iwiri ya pangano ili mʼmanja mwake. Miyalayi inalembedwa mbali zonse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.
И обратился и сошел Моисей с горы; в руке его были две скрижали откровения каменные, на которых написано было с обеих сторон: и на той и на другой стороне написано было;
16 Miyalayi anayikonza ndi Mulungu. Malembawo analemba ndi Mulungu mozokota pa miyalapo.
скрижали были дело Божие, и письмена, начертанные на скрижалях, были письмена Божии.
17 Pamene Yoswa anamva phokoso la anthu anati kwa Mose, “Ku msasa kuli phokoso la nkhondo.”
И услышал Иисус голос народа шумящего и сказал Моисею: военный крик в стане.
18 Mose anayankha kuti, “Phokoso limeneli sindikulimva ngati phokoso la opambana nkhondo, kapena kulira kwa ongonjetsedwa pa nkhondo. Koma ndikulimva ngati phokoso la anthu amene akuyimba.”
Но Моисей сказал: это не крик побеждающих и не вопль поражаемых; я слышу голос поющих.
19 Mose atayandikira msasa ndi kuona mwana wangʼombe ndiponso kuvina, anakwiya kwambiri ndipo anaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwake, ndi kuyiphwanya pa tsinde la phiri.
Когда же он приблизился к стану и увидел тельца и пляски, тогда он воспламенился гневом и бросил из рук своих скрижали и разбил их под горою;
20 Ndipo iye anatenga mwana wangʼombe amene anthu anapanga uja ndi kumuwotcha pa moto ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi. Kenaka anawaza fumbilo mʼmadzi ndi kuwamwetsa Aisraeli madziwo.
и взял тельца, которого они сделали, и сжег его в огне, и стер в прах, и рассыпал по воде, и дал ее пить сынам Израилевым.
21 Tsono Mose anafunsa Aaroni kuti, “Kodi anthu awa anakuchita chiyani kuti uwachimwitse koopsa chotere?”
И сказал Моисей Аарону: что сделал тебе народ сей, что ты ввел его в грех великий?
22 Aaroni anayankha kuti, “Musakwiye mbuye wanga. Inu mukudziwa kuti anthu awa ndi ovuta.
Но Аарон сказал Моисею: да не возгорается гнев господина моего; ты знаешь этот народ, что он буйный.
23 Iwo anati kwa ine, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa ife mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.’
Они сказали мне: сделай нам бога, который шел бы перед нами; ибо с Моисеем, с этим человеком, который вывел нас из земли Египетской, не знаем, что сделалось.
24 Choncho ine ndinawawuza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.”
И я сказал им: у кого есть золото, снимите с себя. Они сняли и отдали мне; я бросил его в огонь, и вышел этот телец.
25 Mose anaona kuti anthuwo anali osokonezekadi chifukwa Aaroni anawalekerera mpaka kusanduka anthu osekedwa pakati pa adani awo.
Моисей увидел, что это народ необузданный, ибо Аарон допустил его до необузданности, к посрамлению пред врагами его.
26 Choncho iye anayima pa chipata cholowera mu msasa ndipo anati, “Aliyense amene ali mbali ya Yehova abwere kwa ine.” Ndipo Alevi onse anapita mbali yake.
И стал Моисей в воротах стана и сказал: кто Господень, иди ко мне! И собрались к нему все сыны Левиины.
27 Ndipo iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena, ‘Pitani ku misasa konse, mulowe ku zipata zonse ndipo aliyense akaphe mʼbale wake, kapena mnzake kapena mnansi wake.’”
И он сказал им: так говорит Господь Бог Израилев: возложите каждый свой меч на бедро свое, пройдите по стану от ворот до ворот и обратно, и убивайте каждый брата своего, каждый друга своего, каждый ближнего своего.
28 Alevi anachita zomwe Mose analamula, ndipo tsiku limenelo panafa anthu pafupifupi 3,000.
И сделали сыны Левиины по слову Моисея: и пало в тот день из народа около трех тысяч человек.
29 Kenaka Mose anati, “Lero mwadzipatula nokha kukhala ansembe otumikira Yehova. Mwachita izi popeza aliyense wa inu wapha mwana wake kapena mʼbale wake. Tsono lero Yehova wakudalitsani.”
Ибо Моисей сказал им: сегодня посвятите руки ваши Господу, каждый в сыне своем и брате своем, да ниспошлет Он вам сегодня благословение.
30 Mmawa mwake Mose anati kwa anthu onse, “Inu mwachita tchimo lalikulu. Koma tsopano ine ndipita ku phiri kwa Yehova mwina ndikatha kukupepeserani chifukwa cha tchimo lanu.”
На другой день сказал Моисей народу: вы сделали великий грех; итак я взойду к Господу, не заглажу ли греха вашего.
31 Kotero Mose anabwereranso kwa Yehova ndipo anati, “Aa! Anthu awa achita tchimo lalikulu! Iwo adzipangira milungu yagolide.
И возвратился Моисей к Господу и сказал: о, Господи! народ сей сделал великий грех: сделал себе золотого бога;
32 Koma tsopano, chonde akhululukireni tchimo lawo. Ngati simutero, ndiye mundifute ine mʼbuku limene mwalemba.”
прости им грех их, а если нет, то изгладь и меня из книги Твоей, в которую Ты вписал.
33 Yehova anamuyankha Mose kuti, “Ndidzafuta mʼbuku aliyense amene wandichimwira.
Господь сказал Моисею: того, кто согрешил предо Мною, изглажу из книги Моей;
34 Tsopano pita ukawatsogolere anthu kumalo kumene ine ndinanena, ndipo mngelo wanga adzakutsogolerani. Komabe, nthawi yanga ikadzafika kuti ndiwalange, ndidzawalanga chifukwa cha tchimo lawo.”
итак иди, сойди, веди народ сей, куда Я сказал тебе; вот Ангел Мой пойдет пред тобою, и в день посещения Моего Я посещу их за грех их.
35 Ndipo Yehova anawakantha anthuwo ndi mliri chifukwa anawumiriza Aaroni kuti awapangire fano la mwana wangʼombe.
И поразил Господь народ за сделанного тельца, которого сделал Аарон.

< Eksodo 32 >