< Eksodo 31 >

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose,
The LORD spoke to Moses, saying,
2 “Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda.
"Look, I have called by name Bezalel the son of Uri, the son of Hur, of the tribe of Judah:
3 Ndipo ndamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi:
and I have filled him with the Spirit of God, in wisdom, and in understanding, and in knowledge, and in all manner of workmanship,
4 Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa,
to devise skillful works, to work in gold, and in silver, and in bronze,
5 kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja.
and in cutting of stones for setting, and in carving of wood, to work in all manner of workmanship.
6 Ndasankhanso Oholiabu mwana wa Ahisamaki wa fuko la Dani. Ndiponso ndapereka nzeru kwa anthu aluso motero adzagwira ntchito zonse zimene ndakulamulira kuti zichitike monga izi:
I, look, I have appointed with him Oholiab, the son of Ahisamach, of the tribe of Dan; and in the heart of all who are wise-hearted I have put wisdom, that they may make all that I have commanded you:
7 Kupanga tenti ya msonkhano, bokosi laumboni pamodzi ndi chophimbira chake, ndiponso zonse za mu tenti,
the Tent of Meeting, the ark of the testimony, the mercy seat that is on it, all the furniture of the Tent,
8 tebulo ndi zida zake, choyikapo nyale cha golide wabwino kwambiri ndi ziwiya zake zonse, guwa lofukizirapo lubani,
the table and its vessels, the pure lampstand with all its vessels, the altar of incense,
9 guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, beseni ndi nsichi yake,
the altar of burnt offering with all its vessels, the basin and its base,
10 ndiponso zovala zonse zolukidwa, zovala zopatulika za Aaroni wansembe pamodzi ndi za ana ake, zovala pamene akutumikira monga ansembe,
the finely worked garments—the holy garments for Aaron the priest—the garments of his sons to minister in the priest's office,
11 ndiponso mafuta odzozera ndi lubani wonunkhira wa ku malo opatulika. Iwo azipanga monga momwe Ine ndinakulamulira.”
the anointing oil, and the incense of sweet spices for the holy place: according to all that I have commanded you they shall do."
12 Ndipo Yehova anati kwa Mose,
The LORD spoke to Moses, saying,
13 “Uza ana a Israeli kuti azisunga Masabata anga. Ichi chidzakhala chizindikiro pakati pa inu ndi Ine pamodzi ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo, chosonyeza kuti Ine ndine amene ndimakuyeretsani.
"Speak also to the children of Israel, saying, 'Most certainly you shall keep my Sabbaths: for it is a sign between me and you throughout your generations; that you may know that I am the LORD who sanctifies you.
14 “Motero muzisunga tsiku la Sabata chifukwa ndi loyera kwa inu. Aliyense amene adetsa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.
You shall keep the Sabbath therefore; for it is holy to you. Everyone who profanes it shall surely be put to death; for whoever does any work in it, that soul shall be cut off from among his people.
15 Mugwire ntchito kwa masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, lopuma, tsiku lopatulika la Yehova. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa.
Six days shall work be done, but on the seventh day is a Sabbath of solemn rest, holy to the LORD. Whoever does any work on the Sabbath day shall surely be put to death.
16 Aisraeli onse komanso zidzukulu zawo mʼtsogolo azidzasunga tsiku la Sabata ngati pangano lamuyaya.
Therefore the children of Israel shall keep the Sabbath, to observe the Sabbath throughout their generations, for a perpetual covenant.
17 Tsiku la Sabata lidzakhala chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi Aisraeli chosonyeza kuti Yehova analenga za kumwamba ndi dziko lapansi kwa masiku asanu ndi limodzi ndi kuti pa tsiku lachisanu ndi chiwiri analeka kugwira ntchito napumula.”
It is a sign between me and the children of Israel forever; for in six days the LORD made heaven and earth, and on the seventh day he rested, and was refreshed.'"
18 Yehova atamaliza kuyankhula ndi Mose pa phiri la Sinai, anamupatsa Mose miyala iwiri yaumboni, imene Mulungu analembapo ndi chala chake.
He gave to Moses, when he finished speaking with him on Mount Sinai, the two tablets of the testimony, stone tablets, written by the finger of God.

< Eksodo 31 >