< Eksodo 30 >

1 Upange guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani.
ועשית מזבח מקטר קטרת עצי שטים תעשה אתו
2 Likhale lofanana mbali zonse. Mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91. Nyanga zake zipangidwe kumodzi ndi guwalo.
אמה ארכו ואמה רחבו רבוע יהיה ואמתים קמתו ממנו קרנתיו
3 Ukute guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse zinayi, pamodzi ndi nyanga zake. Ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira guwalo.
וצפית אתו זהב טהור את גגו ואת קירתיו סביב--ואת קרנתיו ועשית לו זר זהב סביב
4 Upange mphete ziwiri zagolide ndipo uzilumikize ku guwa mʼmunsi mwa mkombero, mphete ziwiri ku mbali zonse ziwiri zoyangʼanana. Mphetozo zizigwira nsichi zonyamulira guwalo.
ושתי טבעת זהב תעשה לו מתחת לזרו על שתי צלעתיו--תעשה על שני צדיו והיה לבתים לבדים לשאת אתו בהמה
5 Upange mizati yamtengo wa mkesha ndipo uyikute ndi golide.
ועשית את הבדים עצי שטים וצפית אתם זהב
6 Uyike guwalo patsogolo pa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano. Apa ndi pamene ndizidzakumana nawe.
ונתתה אתו לפני הפרכת אשר על ארן העדת--לפני הכפרת אשר על העדת אשר אועד לך שמה
7 “Aaroni ayenera kumafukiza lubani wonunkhira pa guwalo mmawa uliwonse. Pamene akukonza nyale zija afukizenso lubani.
והקטיר עליו אהרן קטרת סמים בבקר בבקר בהיטיבו את הנרת--יקטירנה
8 Aaroni ayenera kufukizanso lubani pamene ayatsa nyale madzulo kuti lubani akhale akuyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova kwa mibado imene ikubwera.
ובהעלת אהרן את הנרת בין הערבים יקטירנה--קטרת תמיד לפני יהוה לדרתיכם
9 Pa guwapo usafukize lubani wachilendo kapena kuperekapo nsembe yopsereza kapena nsembe yaufa. Usathire pa guwapo ngakhale nsembe yachakumwa.
לא תעלו עליו קטרת זרה ועלה ומנחה ונסך לא תסכו עליו
10 Aaroni azidzapereka nsembe yopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Mwambowu uzidzachitika pogwiritsa ntchito magazi a nsembe yopepesera machimo, ndipo zizidzachitika mʼmibado yanu yonse. Choncho guwa lansembelo lidzakhala loyera ndi loperekedwa kwa Yehova.”
וכפר אהרן על קרנתיו אחת בשנה מדם חטאת הכפרים אחת בשנה יכפר עליו לדרתיכם--קדש קדשים הוא ליהוה
11 Ndipo Yehova anati kwa Mose,
וידבר יהוה אל משה לאמר
12 “Pamene ukuchita kalembera wa Aisraeli, munthu aliyense ayenera kupereka kwa Yehova chowombolera moyo wake pamene akuwerengedwa. Motero mliri sudzabwera pa iwo pamene ukuwawerenga.
כי תשא את ראש בני ישראל לפקדיהם ונתנו איש כפר נפשו ליהוה בפקד אתם ולא יהיה בהם נגף בפקד אתם
13 Izi ndi zimene aliyense wolembedwa mu kawundula ayenera kupereka: theka la sekeli, kutanthauza ndalama zolemera magalamu asanu ndi limodzi malingana ndi kawerengedwe ka ndalama za ku Nyumba ya Mulungu. Paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi awiri. Theka la sekeli chidzakhala chopereka cha kwa Yehova.
זה יתנו כל העבר על הפקדים--מחצית השקל בשקל הקדש עשרים גרה השקל--מחצית השקל תרומה ליהוה
14 Aliyense wolembedwa mu kawundula amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira ayenera kupereka chopereka kwa Yehova.
כל העבר על הפקדים מבן עשרים שנה ומעלה--יתן תרומת יהוה
15 Anthu olemera asapereke koposa theka la sekeli ndipo osauka asapereke kuchepera theka la sekeli pamene mukupereka nsembe kwa Yehova yowombolera miyoyo yanu.
העשיר לא ירבה והדל לא ימעיט ממחצית השקל--לתת את תרומת יהוה לכפר על נפשתיכם
16 Ulandire ndalama zopepeserazo kuchokera kwa Aisraeli ndipo zigwiritsidwe ntchito ya ku tenti ya msonkhano. Zoperekazi zidzakhala chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova, ndiponso zowombolera miyoyo yanu.”
ולקחת את כסף הכפרים מאת בני ישראל ונתת אתו על עבדת אהל מועד והיה לבני ישראל לזכרון לפני יהוה לכפר על נפשתיכם
17 Ndipo Yehova anati kwa Mose,
וידבר יהוה אל משה לאמר
18 “Upange beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso. Uliyike pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uthiremo madzi.
ועשית כיור נחשת וכנו נחשת--לרחצה ונתת אתו בין אהל מועד ובין המזבח ונתת שמה מים
19 Aaroni ndi ana ake azisamba mʼmanja ndi kutsuka mapazi awo ndi madzi amenewo.
ורחצו אהרן ובניו ממנו את ידיהם ואת רגליהם
20 Pamene akulowa mu tenti ya msonkhano, iwo asambe madziwa kuti asafe. Ndiponso pamene akupita kukatumikira ku guwa lansembe ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Yehova,
בבאם אל אהל מועד ירחצו מים--ולא ימתו או בגשתם אל המזבח לשרת להקטיר אשה ליהוה
21 azisamba mʼmanja mwawo ndi kutsuka mapazi kuti asadzafe. Limeneli ndi lamulo limene Aaroni, pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake mʼtsogolomo ayenera kumadzalitsatira mpaka muyaya.”
ורחצו ידיהם ורגליהם ולא ימתו והיתה להם חק עולם לו ולזרעו לדרתם
22 Ndipo Yehova anati kwa Mose,
וידבר יהוה אל משה לאמר
23 “Utenge zonunkhira bwino kwambiri izi: makilogalamu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogalamu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa sinamoni, makilogalamu atatu a nzimbe yonunkhira bwino kwambiri,
ואתה קח לך בשמים ראש מר דרור חמש מאות וקנמן בשם מחציתו חמשים ומאתים וקנה בשם חמשים ומאתים
24 makilogalamu asanu ndi limodzi a mkesha. Zonsezi zikhale malingana ndi muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu. Pakhalenso malita anayi a mafuta a olivi.
וקדה חמש מאות בשקל הקדש ושמן זית הין
25 Ugwiritse ntchito zinthu zimenezi kupanga mafuta opatulika odzozera, mafuta onunkhira, apangidwe ndi mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa. Awa adzakhala mafuta opatulika odzozera.
ועשית אתו שמן משחת קדש--רקח מרקחת מעשה רקח שמן משחת קדש יהיה
26 Tsono uwagwiritse ntchito podzoza tenti ya msonkhano, Bokosi la Chipangano,
ומשחת בו את אהל מועד ואת ארון העדת
27 tebulo, ndi ziwiya zake zonse, choyikapo nyale ndi zipangizo zake, guwa lofukizirapo lubani,
ואת השלחן ואת כל כליו ואת המנרה ואת כליה ואת מזבח הקטרת
28 guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso beseni pamodzi ndi nsichi yake.
ואת מזבח העלה ואת כל כליו ואת הכיר ואת כנו
29 Zonsezi uzipatule kuti zidzakhale zopatulika, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza zimenezi chidzakhala chopatulika.
וקדשת אתם והיו קדש קדשים כל הנגע בהם יקדש
30 “Udzoze Aaroni ndi ana ake aamuna ndi kuwapatula kuti akhale ansembe onditumikira.
ואת אהרן ואת בניו תמשח וקדשת אתם לכהן לי
31 Tsono awuze a Israeli kuti, mafuta wodzozera awa adzakhala wopatulika mpaka muyaya.
ואל בני ישראל תדבר לאמר שמן משחת קדש יהיה זה לי--לדרתיכם
32 Musadzadzozere munthu wamba mafuta amenewa, ndipo musadzapange mafuta wofanana ndi amenewa. Mafutawa ndi wopatulika ndipo akhale woyera kwa inu.
על בשר אדם לא ייסך ובמתכנתו לא תעשו כמהו קדש הוא קדש יהיה לכם
33 Wina aliyense amene adzapanga mafuta wonunkhira wofanana nawo kapena kudzozera mafutawa munthu wamba osati wansembe ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.”
איש אשר ירקח כמהו ואשר יתן ממנו על זר--ונכרת מעמיו
34 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tenga muyeso wofanana wa zinthu zonunkhira izi: sitakate, onika, galibanumu pamodzi ndi lubani weniweni.
ויאמר יהוה אל משה קח לך סמים נטף ושחלת וחלבנה סמים ולבנה זכה בד בבד יהיה
35 Uziphatikize pamodzi zonsezi ndi kupanga lubani monga amachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Athire mchere ndipo akhale woyera ndi wopatulika.
ועשית אתה קטרת רקח מעשה רוקח ממלח טהור קדש
36 Upere gawo lina mosalala kwambiri ndipo utapepo pangʼono ndi kuyika patsogolo pa Bokosi la Chipangano mu tenti ya msonkhano, kumene ine ndidzakumane nawe. Lubani ameneyu kwa inu adzakhala wopatulika kwambiri.
ושחקת ממנה הדק ונתתה ממנה לפני העדת באהל מועד אשר אועד לך שמה קדש קדשים תהיה לכם
37 Musapange lubani wanu potsatira njira iyi. Lubani yense wopangidwa mwa njira iyi akhale wopatulika, woperekedwa kwa Yehova.
והקטרת אשר תעשה--במתכנתה לא תעשו לכם קדש תהיה לך ליהוה
38 Aliyense amene adzapanga wofanana naye kuti asangalale ndi fungo lake ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.”
איש אשר יעשה כמוה להריח בה--ונכרת מעמיו

< Eksodo 30 >