1“Aaroni mʼbale wako ndi ana ake aamuna, Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara uwapatule pakati pa Aisraeli. Abwere kwa iwe kuti anditumikire monga ansembe.
3Uwawuze anthu onse aluso amene Ine ndawapatsa nzeru pa ntchito yosoka kuti apange zovala za Aaroni za pa mwambo womupatula, kuti iye anditumikire monga wansembe.
4Zovala zoti apange ndi izi: chovala chapachifuwa, efodi, mkanjo, mwinjiro wolukidwa, nduwira ndi lamba. Apangire mʼbale wako Aaroni ndi ana ake aamuna zovala zopatulikazi kuti iwo anditumikire monga ansembe.
5Iwo agwiritse ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira ndi yosalala yofewa.
6“Apange efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yolukidwa mwaluso.
7Efodiyo ikhale ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga.
8Lamba womangira efodi akhale wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Akhale wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala.
9“Utenge miyala iwiri ya onikisi ndipo uzokotepo mayina a ana a Israeli.
10Mayina asanu ndi limodzi akhale pa mwala umodzi, ndipo mayina asanu ndi limodzi pa mwala winawo motsata mabadwidwe awo.
11Mayina a ana a Israeli uwazokote pa miyala iwiriyo, monga momwe amachitira mmisiri wozokota miyala. Ndipo uyike miyalayo mu zoyikamo zake zagolide.
12Umangirire miyala iwiriyi pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli. Aaroni azinyamula mayinawo mʼmapewa ake kuti akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.
17Uyikepo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba ukhale ndi miyala ya rubi, topazi ndi berili.
18Mzere wachiwiri pakhale miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi;
19mzere wachitatu pakhale miyala ya opera, agate ndi ametisiti.
20Mzere wachinayi pakhale miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi uyiike mu zoyikamo zagolide.
21Miyalayo ikhalepo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse uzokotedwe ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli.
22“Upange timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe.
23Upangenso mphete ziwiri zagolide ndipo uzimangirire pa ngodya ziwiri za pa chovala chapachifuwa.
24Umangirire timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho.
25Ndipo mbali ina ya timaunyoloto umangirire pa zoyikapo zake ziwiri zija ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi.
26Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija.
27Upangenso mphete zina ziwiri zagolide ndipo uzilumikize kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi.
28Tsono umangirire mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi.
29“Pamene Aaroni akulowa kumalo opatulika azivala chovala chapachifuwa cha zoweruzira chija chimene chalembedwa mayina a ana a Israeli kuti Yehova awakumbukire nthawi zonse.
30Ndiponso uyike Urimu ndi Tumimu mu chovala chapachifuwa cha zoweruziracho, kuti zikhale pamtima pa Aaroni. Choncho Aaroniyo adzakhala akutenga nthawi zonse zida zomuthandizira kuweruza ana a Israeli pamene adzafika pamaso pa Yehova.
32Mkanjowo ukhala ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo pakhale chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike.
33Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, upange mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira zokhala ndi maberu agolide pakati pake.
37Ulimange ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira ya Aaroni, ndipo duwalo likhale kutsogolo kwa nduwirayo.
38Lidzakhala pa mphumi ya Aaroni, motero iye adzasenza cholakwa chilichonse cha pa zopereka zilizonse zimene Aisraeli amazipatulira Yehova. Aaroni azivala chikwangwanichi pa mphumi pake nthawi zonse kuti Yehova alandire zopereka za anthu ake.
39“Uluke mwinjiro wa nsalu yofewa yosalala ndiponso upange nduwira ya nsalu yofewa yosalala. Lamba wake akhale wolukidwa bwino ndi munthu waluso.
40Upangirenso ana a Aaroni mwinjiro, malamba ndi nduwira kuti azioneka mwaulemu ndi molemekezeka.
41Zovala zimenezi umuveke Aaroni, mʼbale wako ndi ana ake. Kenaka uwadzoze, uwapatse udindo ndi kuwapatula kuti anditumikire ngati ansembe anga.
43Aaroni ndi ana ake ayenera kuvala akabudulawo pamene akulowa mu tenti ya msonkhano kapena pamene akupita ku guwa lansembe kukatumikira malo oyera kuopa kuti angachimwe ndi kufa. “Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aaroni ndi zidzukulu zake.”