4Panga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo.
5Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana.
20Ndipo mbali yakumpoto ya chihemacho upangenso maferemu makumi awiri.
21Upangenso matsinde 40 asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse.
22Upange maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo.
23Ndipo upangenso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti.
24Pa ngodya ziwirizi pakhale maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba ndipo alumikizidwe pa ngowe imodzi. Maferemu onse akhale ofanana.
25Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse.
26“Upange mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha: mitanda isanu ikhale ya maferemu a mbali imodzi ya chihema,
27mitanda isanu inanso ikhale ya maferemu a mbali inayo. Pakhalenso mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema.
28Mtanda wapakati pa maferemuwo uchokere pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso.
29Maferemuwo uwakute ndi golide ndiponso upange mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso uyikute ndi golide.
30“Upange chihema mofanana ndi momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.
31“Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi.
32Nsaluyo uyikoloweke pa nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide zomwe zili ndi ngowe zagolide, zomwe zayima pa matsinde asiliva anayi.
33Ukoloweke kataniyo ku ngowe ndipo uyike Bokosi la Chipangano mʼkatimo. Kataniyo idzalekanitse malo wopatulika ndi malo wopatulika kwambiri.
34Uyike chivundikiro pa bokosi laumboni ku malo wopatulika kwambiri.
35Uyike tebulo kunja kwa katani yotchinga cha kumpoto kwa chihema ndipo uyike choyikapo nyale chija kummwera moyangʼanana ndi tebulolo.
36“Pa chipata cholowera mu chihema, uyikepo nsalu yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira, yomwe ndi yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso.
37Upange ngowe zagolide za nsaluyo ndi nsanamira zisanu zamtengo wa mkesha ndipo uzikute ndi golide. Upangenso matsinde asanu amkuwa a nsanamirazo.”