< Eksodo 26 >
1 “Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.
"Moreover you shall make the tabernacle with ten curtains; of fine twined linen, and blue, and purple, and scarlet, with cherubim. The work of the skillful workman you shall make them.
2 Nsalu zonse zikhale zofanana. Mulitali mwake zikhale mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri.
The length of each curtain shall be forty-one feet four inches, and the breadth of each curtain five feet eleven inches: all the curtains shall have one measure.
3 Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi. Uchite chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo.
Five curtains shall be coupled together one to another; and the other five curtains shall be coupled one to another.
4 Panga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo.
You shall make loops of blue on the edge of the one curtain from the edge in the coupling; and likewise you shall make in the edge of the curtain that is outmost in the second coupling.
5 Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana.
You shall make fifty loops in the one curtain, and you shall make fifty loops in the edge of the curtain that is in the second coupling. The loops shall be opposite one to another.
6 Kenaka upange ngowe zagolide makumi asanu zolumikizira nsalu ziwirizo kuti zipange chihema chimodzi.
You shall make fifty clasps of gold, and couple the curtains one to another with the clasps: and the tabernacle shall be a unit.
7 “Upange nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zikhale khumi ndi imodzi.
"You shall make curtains of goats' hair for a covering over the tabernacle. You shall make them eleven curtains.
8 Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri.
The length of each curtain shall be forthy-four feet four inches, and the breadth of each curtain five feet eleven inches: the eleven curtains shall have one measure.
9 Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri.
You shall couple five curtains by themselves, and six curtains by themselves, and shall double over the sixth curtain in the forefront of the tent.
10 Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija.
You shall make fifty loops on the edge of the one curtain that is outmost in the coupling, and fifty loops on the edge of the curtain which is outmost in the second coupling.
11 Kenaka upange ngowe 50 zamkuwa ndipo uzilowetse mu zokolowekazo. Ndiye uphatikize nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi.
You shall make fifty clasps of bronze, and put the clasps into the loops, and couple the tent together, that it may be one.
12 Theka lotsalira la nsaluyo lidzalendewera kumbuyo kwa chihemacho.
The overhanging part that remains of the curtains of the tent, the half curtain that remains, shall hang over the back of the tabernacle.
13 Nsalu yotsalira ya masentimita 46 mulitali mwake mʼmbali zonse ziwiri idzalendewere kuphimba mbali ziwirizo.
Eighteen inches on the one side, and eighteen inches on the other side, of that which remains in the length of the curtains of the tent, shall hang over the sides of the tabernacle on this side and on that side, to cover it.
14 Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.
You shall make a covering for the tent of rams' skins dyed red, and a covering of sea cow hides above.
15 “Upange maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho.
"You shall make the boards for the tabernacle of acacia wood, standing up.
16 Feremu iliyonse ikhale yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake mukhale masentimita 69.
Seventeen feet three inches shall be the length of a board, and two feet three inches the breadth of each board.
17 Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri. Upange maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere.
There shall be two tenons in each board, joined to one another: thus you shall make for all the boards of the tabernacle.
18 Upange maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho.
You shall make the boards for the tabernacle, twenty boards for the south side southward.
19 Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija.
You shall make forty sockets of silver under the twenty boards; two sockets under one board for its two tenons, and two sockets under another board for its two tenons.
20 Ndipo mbali yakumpoto ya chihemacho upangenso maferemu makumi awiri.
For the second side of the tabernacle, on the north side, twenty boards,
21 Upangenso matsinde 40 asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse.
and their forty sockets of silver; two sockets under one board, and two sockets under another board.
22 Upange maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo.
For the far part of the tabernacle westward you shall make six boards.
23 Ndipo upangenso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti.
You shall make two boards for the corners of the tabernacle in the far part.
24 Pa ngodya ziwirizi pakhale maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba ndipo alumikizidwe pa ngowe imodzi. Maferemu onse akhale ofanana.
They shall be double beneath, and in like manner they shall be entire to its top to one ring: thus shall it be for them both; they shall be for the two corners.
25 Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse.
There shall be eight boards, and their sockets of silver, sixteen sockets; two sockets under one board, and two sockets under another board.
26 “Upange mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha: mitanda isanu ikhale ya maferemu a mbali imodzi ya chihema,
"You shall make bars of acacia wood: five for the boards of the one side of the tabernacle,
27 mitanda isanu inanso ikhale ya maferemu a mbali inayo. Pakhalenso mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema.
and five bars for the boards of the other side of the tabernacle, and five bars for the boards of the side of the tabernacle, for the far part westward.
28 Mtanda wapakati pa maferemuwo uchokere pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso.
The middle bar in the midst of the boards shall pass through from end to end.
29 Maferemuwo uwakute ndi golide ndiponso upange mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso uyikute ndi golide.
You shall overlay the boards with gold, and make their rings of gold for places for the bars: and you shall overlay the bars with gold.
30 “Upange chihema mofanana ndi momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.
You shall set up the tabernacle according to the way that it was shown to you on the mountain.
31 “Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi.
"You shall make a veil of blue, and purple, and scarlet, and fine twined linen, with cherubim. The work of the skillful workman shall it be made.
32 Nsaluyo uyikoloweke pa nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide zomwe zili ndi ngowe zagolide, zomwe zayima pa matsinde asiliva anayi.
You shall hang it on four pillars of acacia overlaid with gold; their hooks shall be of gold, on four sockets of silver.
33 Ukoloweke kataniyo ku ngowe ndipo uyike Bokosi la Chipangano mʼkatimo. Kataniyo idzalekanitse malo wopatulika ndi malo wopatulika kwambiri.
You shall hang up the veil under the clasps, and shall bring the ark of the testimony in there within the veil: and the veil shall separate the holy place from the most holy for you.
34 Uyike chivundikiro pa bokosi laumboni ku malo wopatulika kwambiri.
You shall put the mercy seat on the ark of the testimony in the most holy place.
35 Uyike tebulo kunja kwa katani yotchinga cha kumpoto kwa chihema ndipo uyike choyikapo nyale chija kummwera moyangʼanana ndi tebulolo.
You shall set the table outside the veil, and the lampstand over against the table on the side of the tabernacle toward the south: and you shall put the table on the north side.
36 “Pa chipata cholowera mu chihema, uyikepo nsalu yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira, yomwe ndi yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso.
"You shall make a screen for the door of the Tent, of blue, and purple, and scarlet, and fine twined linen, the work of the embroiderer.
37 Upange ngowe zagolide za nsaluyo ndi nsanamira zisanu zamtengo wa mkesha ndipo uzikute ndi golide. Upangenso matsinde asanu amkuwa a nsanamirazo.”
You shall make for the screen five pillars of acacia, and overlay them with gold: their hooks shall be of gold: and you shall cast five sockets of bronze for them.