< Eksodo 25 >

1 Yehova ananena kwa Mose kuti,
Locutusque est Dominus ad Moysen, dicens:
2 “Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake.
Loquere filiis Israël, ut tollant mihi primitias: ab omni homine qui offeret ultroneus, accipietis eas.
3 Zopereka zimene ulandire kwa anthuwo ndi izi: Golide, siliva ndi mkuwa.
Hæc sunt autem quæ accipere debeatis: aurum, et argentum, et æs,
4 Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi;
hyacinthum et purpuram, coccumque bis tinctum, et byssum, pilos caprarum,
5 zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha;
et pelles arietum rubricatas, pellesque janthinas, et ligna setim:
6 mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira;
oleum ad luminaria concinnanda: aromata in unguentum, et thymiamata boni odoris:
7 miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.
lapides onychinos, et gemmas ad ornandum ephod, ac rationale.
8 “Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo.
Facientque mihi sanctuarium, et habitabo in medio eorum:
9 Umange chihema ndiponso ziwiya zamʼkatimo monga momwe Ine ndidzakuonetsere.
juxta omnem similitudinem tabernaculi quod ostendam tibi, et omnium vasorum in cultum ejus. Sicque facietis illud:
10 “Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69.
arcam de lignis setim compingite, cujus longitudo habeat duos et semis cubitos: latitudo, cubitum et dimidium: altitudo, cubitum similiter ac semissem.
11 Bokosilo ulikute ndi golide wabwino kwambiri, mʼkati mwake ndi kunja komwe, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira bokosilo.
Et deaurabis eam auro mundissimo intus et foris: faciesque supra, coronam auream per circuitum:
12 Upange mphete zinayi zagolide ndipo uzimangirire ku miyendo yake inayi ya bokosilo, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri.
et quatuor circulos aureos, quos pones per quatuor arcæ angulos: duo circuli sint in latere uno, et duo in altero.
13 Kenaka upange mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide.
Facies quoque vectes de lignis setim, et operies eos auro.
14 Ndipo ulowetse nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira.
Inducesque per circulos qui sunt in arcæ lateribus, ut portetur in eis:
15 Nsichizo zizikhala mʼmphete za bokosilo nthawi zonse, zisamachotsedwe.
qui semper erunt in circulis, nec umquam extrahentur ab eis.
16 Ndipo udzayike mʼbokosilo miyala iwiri yolembedwapo malamulo imene Ine ndidzakupatse.
Ponesque in arca testificationem quam dabo tibi.
17 “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69.
Facies et propitiatorium de auro mundissimo: duos cubitos et dimidium tenebit longitudo ejus, et cubitum ac semissem latitudo.
18 Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho,
Duos quoque cherubim aureos et productiles facies, ex utraque parte oraculi.
19 kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa uwapangire limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo.
Cherub unus sit in latere uno, et alter in altero.
20 Mapiko a Akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo adzakhale choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho.
Utrumque latus propitiatorii tegant expandentes alas, et operientes oraculum, respiciantque se mutuo versis vultibus in propitiatorium quo operienda est arca,
21 Uyike chivundikirocho pamwamba pa bokosi ndipo mʼbokosilo uyikemo miyala ya malamulo, imene ndidzakupatse.
in qua pones testimonium quod dabo tibi.
22 Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli.
Inde præcipiam, et loquar ad te supra propitiatorium, ac de medio duorum cherubim, qui erunt super arcam testimonii, cuncta quæ mandabo per te filiis Israël.
23 “Upange tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69.
Facies et mensam de lignis setim, habentem duos cubitos longitudinis, et in latitudine cubitum, et in altitudine cubitum et semissem.
24 Tebulolo ulikute ndi golide wabwino kwambiri ndipo upange mkombero wagolide mʼmbali mwake.
Et inaurabis eam auro purissimo: faciesque illi labium aureum per circuitum,
25 Upange feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo uyike mkombero wagolide kuzungulira feremuyo.
et ipsi labio coronam interrasilem altam quatuor digitis: et super illam, alteram coronam aureolam.
26 Upange mphete zinayi zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zake zinayi, kumene kuli miyendo yake inayi.
Quatuor quoque circulos aureos præparabis, et pones eis in quatuor angulis ejusdem mensæ per singulos pedes.
27 Mphetezo uziyike kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo.
Subter coronam erunt circuli aurei, ut mittantur vectes per eos, et possit mensa portari.
28 Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide kuti azinyamulira tebulolo.
Ipsos quoque vectes facies de lignis setim, et circumdabis auro ad subvehendam mensam.
29 Upange mbale ndi zipande zagolide wabwino, pamodzinso ndi mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe.
Parabis et acetabula, ac phialas, thuribula, et cyathos, in quibus offerenda sunt libamina, ex auro purissimo.
30 Pa tebulopo uyikepo buledi woperekedwa kosalekeza, kuti azikhala pamaso panga nthawi zonse.
Et pones super mensam panes propositionis in conspectu meo semper.
31 “Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi.
Facies et candelabrum ductile de auro mundissimo, hastile ejus, et calamos, scyphos, et sphærulas, ac lilia ex ipso procedentia.
32 Mʼmbali mwake mukhale mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse.
Sex calami egredientur de lateribus, tres ex uno latere, et tres ex altero.
33 Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zikhale pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri pakhalenso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zikhale chimodzimodzi ndipo zituluke mʼchoyikapo nyalecho.
Tres scyphi quasi in nucis modum per calamos singulos, sphærulaque simul, et lilium: et tres similiter scyphi instar nucis in calamo altero, sphærulaque simul et lilium. Hoc erit opus sex calamorum, qui producendi sunt de hastili:
34 Pa choyikapo nyalecho pakhale zikho zinayi zopangidwa ngati maluwa amtowo ali ndi mphukira ndi maluwa.
in ipso autem candelabro erunt quatuor scyphi in nucis modum, sphærulæque per singulos, et lilia.
35 Mphukira yoyamba ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Ndipo mphukira yachitatu ikhale mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zikhale nthambi zisanu ndi imodzi
Sphærulæ sub duobus calamis per tria loca, qui simul sex fiunt procedentes de hastili uno.
36 Mphukira ndi nthambi zonse zisulidwe kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri.
Et sphærulæ igitur et calami ex ipso erunt, universa ductilia de auro purissimo.
37 “Ndipo upange nyale zisanu ndi ziwiri ndi kuziyika pa choyikapo nyalecho kuti ziwunikire kutsogolo.
Facies et lucernas septem, et pones eas super candelabrum, ut luceant ex adverso.
38 Mbaniro ndi zowolera phulusa zikhale zagolide wabwino kwambiri.
Emunctoria quoque, et ubi quæ emuncta sunt extinguantur, fiant de auro purissimo.
39 Choyikapo nyale ndi zipangizo zonse zipangidwe ndi golide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34.
Omne pondus candelabri cum universis vasis suis habebit talentum auri purissimi.
40 Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.”
Inspice, et fac secundum exemplar quod tibi in monte monstratum est.

< Eksodo 25 >