7Upewe zabodza ndipo usaphetse munthu wosalakwa ndi wolungama, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.
8“Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa.
9“Usamuzunze mlendo, pakuti inu nomwe mukudziwa mmene amamvera mlendo chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Igupto.
10“Muzidzala mbewu zanu mʼmunda ndi kumakolola mbewuzo kwa zaka zisanu ndi chimodzi.
11Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi.
12“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri musagwire ntchito kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu apume ndiponso kuti kapolo wobadwira mʼnyumba yanu ndi mlendo yemwe apezenso mphamvu.
13“Samalani pochita zonse zimene ine ndanena. Musamapemphere kwa milungu ina ndipo mayina awo musamawatchule.
14“Muzichita zikondwerero zolemekeza Ine katatu pa chaka.
15“Muzichita Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi mwezi wa Abibu pa nthawi yomwe ndayika, pakuti mʼmwezi umenewu munatuluka mʼdziko la Igupto. “Pasapezeke munthu wobwera pamaso panga wopanda kanthu mʼmanja.
16“Muzichita Chikondwerero cha Masika pogwiritsa ntchito zipatso zoyambirira kucha zimene munadzala mʼmunda. “Muzichitanso Chikondwerero cha Zokolola pakutha pa chaka, pamene mukututa zokolola zanu mʼmunda.
17“Amuna onse azionekera pamaso pa Ambuye Yehova katatu pa chaka.
18“Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti. “Ndipo musasunge mafuta anyama yansembe ya pa chikondwerero mpaka mmawa.
19“Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku Nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.
20“Taona Ine ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu kuti akutetezeni mʼnjiramo ndi kukakufikitsani ku malo amene ndakonza.
21Muzimumvera ndi kumvetsetsa zimene akunena. Musamuwukire chifukwa sadzakhululuka kuwukira kwanu, pakuti akuchita zimenezi mʼdzina langa.
22Ngati mudzamvera iyeyu ndi kuchita zonse zimene Ine ndikunena, Ine ndidzakhala mdani wa adani anu ndipo ndidzatsutsana ndi onse otsutsana nanu.
23Mngelo wanga adzakhala patsogolo panu ndipo adzakufikitsani mʼdziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanaani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawapheratu onsewo.
24Musagwadire milungu yawo kapena kuyipembedza. Ndipo musatsatire zinthu zomwe amachita. Koma inu mukawononge milungu yawo ndi kuphwasula malo amene amapembedzerapo.
25Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu.
30Ndidzawathamangitsa pangʼonopangʼono mpaka inu mutachuluka kokwanira mwakuti nʼkutenga dzikolo.
31“Malire a dziko lanu adzakhala kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku nyanja ya Afilisti, ndiponso kuyambira ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Anthu onse okhala mʼdziko limeneli ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo mudzawathamangitsa.
32Musachite pangano ndi iwo kapena ndi milungu yawo.
33Asadzakhale mʼdziko lanu chifukwa angadzakuchimwitseni ndi kuyamba kupembedza milungu yawo. Mukadzatero ndiye kuti mwakodwa mu msampha.”