< Eksodo 23 >

1 “Usafalitse mbiri yabodza. Usathandize munthu wolakwa pomuchitira umboni wonama.
لَا تَنْقُلْ أَخْبَاراً كَاذِبَةً، وَلا تَتَعَاوَنْ مَعَ المُنَافِقِ فِي شَهَادَةِ زُورٍ.١
2 “Usatsate gulu la anthu ndi kuchita choyipa. Pamene ukupereka umboni mʼbwalo lamilandu, usakhotetse mlandu chifukwa chofuna kukondweretsa anthu ambiri.
لَا تَتْبَعِ الأَغْلَبِيَّةَ لاِرْتِكَابِ الشَّرِّ، وَلا تُحَرِّفْ شَهَادَتَكَ فِي دَعْوَى انْجِرَافاً مَعَ الأَكْثَرِيَّةِ،٢
3 Ndipo poweruza mlandu wa munthu wosauka usamukondere.
وَلا تَتَحَيَّزْ لِلْفَقِيرِ فِي دَعْوَاهُ لِمُجَرَّدِ كَوْنِهِ فَقِيراً فَقَطْ.٣
4 “Ngati ukumana ndi ngʼombe kapena bulu wa mdani wako zitasochera, uwonetsetse kuti wazitenga kupita nazo kwa mwini wakeyo.
إِذَا صَادَفْتَ ثَوْرَ عَدُوِّكَ أَوْ حِمَارَهُ شَارِداً، فَرُدَّهُ إِلَيْهِ.٤
5 Ngati uwona bulu wa munthu wina amene amakuda atagwa ndi katundu, usamusiye pomwepo, uwonetsetse kuti wamuthandiza.
وَإذَا عَايَنْتَ حِمَارَ مُبْغِضِكَ وَاقِعاً تَحْتَ حِمْلِهِ، فَلا تَتَجَاوَزْهُ حَتَّى تُسْعِفَ عَدُوَّكَ فِي حَلِّ ثِقْلِ حِمَارِهِ.٥
6 “Usakhotetse milandu ya anthu osauka.
لَا تَتَهَاوَنْ فِي حَقِّ فَقِيرِكَ فِي دَعْوَاهُ لِكَوْنِهِ فَقِيراً.٦
7 Upewe zabodza ndipo usaphetse munthu wosalakwa ndi wolungama, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.
اجْتَنِبْ الاتِّهَامَ الْكَاذِبَ وَلا تَقْتُلِ الْبَرِيءَ وَالصَّالِحَ، لأَنَّنِي لَا أُبْرِىءُ المُذْنِبَ.٧
8 “Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa.
لَا تَقْبَلْ رِشْوَةً لأَنَّ الرِّشْوَةَ تُعْمِي الْمُبْصِرِينَ وَتُحَرِّفُ أَقْوَالَ الصَّالِحِينَ.٨
9 “Usamuzunze mlendo, pakuti inu nomwe mukudziwa mmene amamvera mlendo chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Igupto.
لَا تُضَايِقْ غَرِيباً لأَنَّكُمْ تَعْلَمُونَ مَشَاعِرَ الغَرِيبِ، فَقَدْ كُنْتُمْ غُرَبَاءَ فِي دِيَارِ مِصْرَ.٩
10 “Muzidzala mbewu zanu mʼmunda ndi kumakolola mbewuzo kwa zaka zisanu ndi chimodzi.
ازْرَعْ أَرْضَكَ وَاحْصُدْ غَلَّتَهَا سِتَّ سِنِينَ،١٠
11 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi.
ثُمَّ أَرِحْهَا فِي السَّنَةِ السَّابِعَةِ وَاتْرُكْهَا لِيَأْكُلَ مِنْهَا فُقَرَاءُ شَعْبِكَ. وَمَا فَضَلَ عَنْهُمْ تَقْتَاتُهُ وُحُوشُ الْبَرِّيَّةِ. وَهَكَذَا تَفْعَلُ أَيْضاً بِكَرْمِكَ وَزَيْتُونِكَ.١١
12 “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri musagwire ntchito kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu apume ndiponso kuti kapolo wobadwira mʼnyumba yanu ndi mlendo yemwe apezenso mphamvu.
اعْمَلْ سِتَّةَ أَيَّامٍ فَقَطْ، وَفِي الْيَوْمِ السَّابِعِ تَسْتَرِيحُ لِكَيْ يَسْتَرِيحَ أَيْضاً ثَوْرُكَ وَحِمَارُكَ، وَيَنْتَعِشَ ابْنُ أَمَتِكَ وَالغَرِيبُ.١٢
13 “Samalani pochita zonse zimene ine ndanena. Musamapemphere kwa milungu ina ndipo mayina awo musamawatchule.
أَطِيعُوا كُلَّ مَا أَوْصَيْتُكُمْ بِهِ، وَلا تَذْكُرُوا اسْمَ آلِهَةٍ أُخْرَى، وَلا يَتَلَفَّظْ بِهِ فَمُكَ.١٣
14 “Muzichita zikondwerero zolemekeza Ine katatu pa chaka.
ثَلاثَ مَرَّاتٍ تَحْتَفِلُ لِي فِي السَّنَةِ:١٤
15 “Muzichita Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi mwezi wa Abibu pa nthawi yomwe ndayika, pakuti mʼmwezi umenewu munatuluka mʼdziko la Igupto. “Pasapezeke munthu wobwera pamaso panga wopanda kanthu mʼmanja.
تَحْتَفِلُ بِعِيدِ الْفَطِيرِ فَتَأْكُلُ كَمَا أَمَرْتُكَ فَطِيراً، مُدَّةَ سَبْعَةِ أَيَّامٍ، فِي الْوَقْتِ الْمُعَيَّنِ مِنْ شَهْرِ أَبِيبَ (أَيْ شَهْرِ آذَارَ – مَارِسَ)، لأَنَّهُ فِيهِ خَرَجْتَ مِنْ مِصْرَ. وَلا يَمْثُلُ أَحَدٌ أَمَامِي بِيَدَيْنِ فَارِغَتَيْنِ.١٥
16 “Muzichita Chikondwerero cha Masika pogwiritsa ntchito zipatso zoyambirira kucha zimene munadzala mʼmunda. “Muzichitanso Chikondwerero cha Zokolola pakutha pa chaka, pamene mukututa zokolola zanu mʼmunda.
وَتَحْتَفِلُ أَيْضاً بِعِيدِ الْحَصَادِ، حَيْثُ تُقَدِّمُ بَاكُورَةَ غَلّاتِكَ الَّتِي زَرَعْتَهَا فِي الْحَقْلِ، ثُمَّ عِيدِ الْجَمْعِ فِي نِهَايَةِ مَوْسِمِ الْحَصَادِ عِنْدَمَا تَجْمَعُ غَلّاتِكَ مِنَ الْحَقْلِ.١٦
17 “Amuna onse azionekera pamaso pa Ambuye Yehova katatu pa chaka.
ثَلاثَ مَرَّاتٍ يَمْثُلُ جَمِيعُ الرِّجَالِ أَمَامَ السَّيِّدِ الرَّبِّ.١٧
18 “Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti. “Ndipo musasunge mafuta anyama yansembe ya pa chikondwerero mpaka mmawa.
لَا تُقَرِّبْ لِي دَمَ ذَبِيحَةٍ مَعَ خُبْزٍ مُخْتَمِرٍ، وَلا يَبِتْ شَحْمُ ذَبَائِحِ عِيدِي إِلَى صَبَاحِ الْغَدِ.١٨
19 “Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku Nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.
أَحْضِرْ أَجْوَدَ بَاكُورَةِ أَرْضِكَ إِلَى بَيْتِ إِلَهِكَ. وَلا تَطْبُخْ جَدْياً فِي لَبَنِ أُمِّهِ.١٩
20 “Taona Ine ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu kuti akutetezeni mʼnjiramo ndi kukakufikitsani ku malo amene ndakonza.
هَا أَنَا مُرْسِلٌ مَلاكِي أَمَامَكَ لِيَحْرُسَكَ طَوَالَ الطَّرِيقِ، وَيَقُودَكَ إِلَى الأَرْضِ الَّتِي أَعْدَدْتُهَا لَكَ.٢٠
21 Muzimumvera ndi kumvetsetsa zimene akunena. Musamuwukire chifukwa sadzakhululuka kuwukira kwanu, pakuti akuchita zimenezi mʼdzina langa.
فَأصْغِ إِلَيْهِ وَامْتَثِلْ لَهُ وَلا تَعْصَهُ لأَنَّهُ لَا يَصْفَحُ عَنْ ذُنُوبِكُمْ إِذْ أَنَّ اسْمِي فِيهِ.٢١
22 Ngati mudzamvera iyeyu ndi kuchita zonse zimene Ine ndikunena, Ine ndidzakhala mdani wa adani anu ndipo ndidzatsutsana ndi onse otsutsana nanu.
إِنْ حَرِصْتَ عَلَى الاسْتِمَاعِ إِلَى أَقْوَالِهِ وَفَعَلْتَ كُلَّ مَا قُلْتُهُ، أُعَادِي مَنْ يُعَادِيكَ، وَأُقَاوِمُ مُقَاوِمِيكَ،٢٢
23 Mngelo wanga adzakhala patsogolo panu ndipo adzakufikitsani mʼdziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanaani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawapheratu onsewo.
إِذْ يَسِيرُ مَلاكِي أَمَامَكَ حَتَّى يُدْخِلَكَ بِلادَ الأَمُورِيِّينَ وَالْحِثِّيِّينَ وَالْفَرِزِّيِّينَ وَالْكَنْعَانِيِّينَ وَالْحِوِّيِّينَ وَالْيَبُوسِيِّينَ الَّذِينَ أُبِيدُهُمْ.٢٣
24 Musagwadire milungu yawo kapena kuyipembedza. Ndipo musatsatire zinthu zomwe amachita. Koma inu mukawononge milungu yawo ndi kuphwasula malo amene amapembedzerapo.
إِيَّاكَ أَنْ تَسْجُدَ لِآلِهَتِهِمْ، وَلا تَعْبُدْهَا، وَلا تَعْمَلْ أَعْمَالَهُمْ، بَلْ تُبِيدُهُمْ وَتُحَطِّمُ أَصْنَامَهُمْ.٢٤
25 Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu.
إِنَّمَا تَعْبُدُونَنِي أَنَا الرَّبَّ إِلَهَكُمْ فَأُبَارِكُ طَعَامَكَ وَشَرَابَكَ وَأُزِيلُ الأَمْرَاضَ مِنْ بَيْنِكُمْ٢٥
26 Palibe mkazi amene adzapite padera kapena kukhala wosabereka mʼdziko mwanu. Ndidzakupatsani moyo wautali.
فَلا تَكُونُ مُجْهِضَةٌ وَلا عَاقِرٌ فِي أَرْضِكَ. وَأُمَتِّعُكَ بِكَامِلِ عُمْرِكَ.٢٦
27 “Ine ndidzawachititsa mantha ndi kusokoneza anthu onse amene adzalimbana ndi inu ndipo adani anu onse adzakuthawani.
وَأَجْعَلُ هَيْبَتِي تَتَقَدَّمُكَ، أُزْعِجُ كُلَّ أُمَّةٍ تَقِفُ فِي وَجْهِكَ، وَأَجْعَلُ أَعْدَاءَكَ يُوَلُّونَ الأَدْبَارَ أَمَامَكَ.٢٧
28 Ahivi, Akanaani ndi Ahiti adzathawa ngati kuti ndawatumizira mavu.
وَأَبْعَثُ الزَّنَابِيرَ أَمَامَكَ، فَتَطْرُدُ الْحِوِّيِّينَ وَالْكَنْعَانِيِّينَ وَالْحِثِّيِّينَ مِنْ قُدَّامِكَ.٢٨
29 Komabe sindidzawachotseratu onse mʼchaka chimodzi chifukwa dziko lingadzakhale lopanda anthu ndipo nyama zakuthengo zidzakuchulukirani.
إِنَّمَا لَنْ أَطْرُدَهُمْ فِي سَنَةٍ وَاحِدَةٍ لِئَلّا تُقْفِرَ الأَرْضُ فَتَتَكَاثَرَ عَلَيْكَ وُحُوشُ الْبَرِّيَّةِ،٢٩
30 Ndidzawathamangitsa pangʼonopangʼono mpaka inu mutachuluka kokwanira mwakuti nʼkutenga dzikolo.
بَلْ أَطْرُدُهُمْ تَدْرِيجِيًّا مِنْ أَمَامِكَ رَيْثَمَا تَنْمُونَ وَتَرِثُونَ الْبِلادَ.٣٠
31 “Malire a dziko lanu adzakhala kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku nyanja ya Afilisti, ndiponso kuyambira ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Anthu onse okhala mʼdziko limeneli ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo mudzawathamangitsa.
وَأَجْعَلُ تُخُومَكَ تَمْتَدُّ مِنَ الْبَحْرِ الأَحْمَرِ إِلَى سَاحِلِ فِلِسْطِينَ، وَمِنَ الْبَرِّيَّةِ حَتَّى نَهْرِ الْفُرَاتِ، وَأُخْضِعُ لَكَ سُكَّانَ الأَرْضِ فَتَطْرُدُهُمْ مِنْ أَمَامِكَ.٣١
32 Musachite pangano ndi iwo kapena ndi milungu yawo.
لَا تَقْطَعْ مَعَهُمْ وَلا مَعْ آلِهَتِهِمْ عَهْداً،٣٢
33 Asadzakhale mʼdziko lanu chifukwa angadzakuchimwitseni ndi kuyamba kupembedza milungu yawo. Mukadzatero ndiye kuti mwakodwa mu msampha.”
وَلا تُسْكِنْهُمْ فِي أَرْضِكَ لِئَلّا يَجْعَلُوكَ تُخْطِئُ إِلَيَّ، لأَنَّكَ إنْ عَبَدْتَ آلِهَتَهُمْ، يَكُونُ ذَلِكَ لَكَ فَخّاً».٣٣

< Eksodo 23 >