1“Ngati munthu aba ngʼombe kapena nkhosa ndi kuyipha kapena kuyigulitsa, iye abweze ngʼombe zisanu pa ngʼombe imodzi ndi nkhosa zinayi pa nkhosa imodzi.
23Ngati muwazunza ndipo iwo nʼkulirira kwa Ine, ndidzamva kulira kwawo.
24Ine ndidzakukwiyirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga. Akazi anu adzakhala amasiye ndiponso ana anu adzakhala wopanda abambo.
25“Ngati mukongoza ndalama kwa mʼbale wanu amene ndi mʼmphawi pakati panu, musadzamuchite monga zimene amachita wokongoza ndalama. Musadzamuyikire chiwongoladzanja.
26Mukatenga chovala cha mnzanu kuti chikhale chikole mumubwezere dzuwa lisanalowe
27chifukwa chovala chimene amadzifundira nacho nʼchomwecho. Nanga usiku adzafunda chiyani? Tsonotu ngati adzandilirira, Ine ndidzamva pakuti ndine wachifundo.
28“Musachite chipongwe Mulungu wanu kapena kutemberera mtsogoleri wa anthu anu.
29“Musachedwe kupereka kwa Ine zokolola zanu zochuluka ndi vinyo wanu wochuluka. “Mundipatse ana anu achisamba aamuna.
30Muchite chimodzimodzi ndi ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwa azikhala ndi amayi ake masiku asanu ndi awiri. Koma pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo muzimupereka kwa Ine.
31“Inu mukhale anthu anga opatulika. Choncho musadye nyama ya chiweto chimene chaphedwa ndi zirombo. Nyamayo muwaponyere agalu.”