< Eksodo 2 >

1 Ndipo munthu wina wa fuko la Levi anakwatira mkazi wa fuko lomwelo.
After this there went a man of the house of Levi; and took a wife of his own kindred.
2 Mkaziyo anatenga pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo anali wokongola, anamubisa kwa miyezi itatu.
And she conceived, and bore a son; and seeing him a goodly child hid him three months.
3 Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sakanathanso kubisidwa, amayi ake anatenga kadengu kopangidwa ndi bango nakamata phula. Kenaka anayika mwanayo mʼmenemo ndi kukamuyika pa mabango mu mtsinje wa Nailo.
And when she could hide him no longer, she took a basket made of bulrushes, and daubed it with slime and pitch: and put the little babe therein, and laid him in the sedges by the river’s brink,
4 Mlongo wake wa mwanayo anayima pataliko kuti aone chimene chidzamuchitikira mwanayo.
His sister standing afar off, and taking notice what would be done.
5 Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge.
And behold the daughter of Pharao came down to wash herself in the river: and her maids walked by the river’s brink. And when she saw the basket in the sedges, she sent one of her maids for it: and when it was brought,
6 Iye atavundukula anaona mwana wamwamuna akungolira. Iye anamva naye chisoni mwana uja, nati, “Ameneyu ndi mmodzi mwa ana a Chihebri.”
She opened it and seeing within it an infant crying, having compassion on it she said: This is one of the babes of the Hebrews.
7 Kenaka mlongo wake wa mwanayo anafunsa mwana wa Farao kuti, “Ndingapite kukakupezerani mmodzi mwa amayi a Chihebri kuti azikakulererani mwanayu?”
And the child’s sister said to her Shall I go and call to thee a Hebrew woman, to nurse the babe?
8 Iye anayankha kuti, “Inde, pita.” Ndipo mtsikanayo anapita nakayitana amayi a mwanayo.
She answered: Go. The maid went and called her mother.
9 Mwana wa Farao anati, “Tengani mwanayu mukandilerere, ndidzakulipirani.” Mayiyo anatenga mwanayo kukamulera.
And Pharao’s daughter said to her. Take this child and nurse him for me: I will give thee thy wages. The woman took, and nursed the child: and when he was grown up, she delivered him to Pharao’s daughter.
10 Mwanayo atakula anakamupereka kwa mwana wa Farao ndipo anakhala mwana wake. Iye anamutcha dzina lake Mose, popeza anati, “Ndinamuvuwula mʼmadzi.”
And she adopted him for a son, and called him Moses, saying: Because I took him out of the water.
11 Tsiku lina, Mose atakula, anapita kumene kunali anthu a mtundu wake ndipo anawaona akugwira ntchito yowawa. Iye anaona Mwigupto akumenya Mhebri, mmodzi mwa anthu a mtundu wake.
In those days after Moses was grown up, he went out to his brethren: and saw their affliction, and an Egyptian striking one of the Hebrews his brethren.
12 Atayangʼana uku ndi uku, naona kuti panalibe wina aliyense, Mose anamupha Mwiguptoyo ndipo anamukwirira mu mchenga.
And when he had looked about this way and that way, and saw no one there, he slew the Egyptian and hid him in the sand.
13 Mmawa mwake Mose anapita ndipo anaona anthu awiri a Chihebri akumenyana. Iye anafunsa amene anali wolakwa kuti, “Chifukwa chiyani ukumenya Mhebri mnzako?”
And going out the next day, he saw two Hebrews quarrelling: and he said to him that did the wrong: Why strikest thou thy neighbour?
14 Munthu uja anati, “Kodi ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza? Kodi ukufuna kundipha monga momwe unaphera Mwigupto uja?” Mose anachita mantha ndipo anati mu mtima mwake, “Chimene ndinachita chija chadziwika.”
But he answered: Who hath appointed thee prince and judge over us? Wilt thou kill me, as thou didst yesterday kill the Egyptian? Moses feared, and said: How is this come to be known?
15 Farao atamva zimenezi anafuna kuti aphe Mose, koma Mose anathawa ndipo anapita kukakhala ku Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina anakhala pansi pafupi ndi chitsime.
And Pharao heard of this word and sought to kill Moses: but he fled from his sight, and abode in the land of Madian, and he sat down by a well.
16 Wansembe wa ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi awiri. Iwowa anabwera kudzatunga madzi ndi kudzaza mu zomwera kuti amwetse nkhosa za abambo awo.
And the priest of Madian had seven daughters, who came to draw water: and when the troughs were filled, desired to water their father’s flocks.
17 Koma kunabwera abusa ena amene anathamangitsa atsikana aja. Ndiye Mose anayimirira nawathandiza atsikana aja ndi kumwetsa nkhosa zawo.
And the shepherds came and drove them away: and Moses arose, and defending the maids, watered their sheep.
18 Atsikana aja atabwerera kwa abambo awo Reueli, iye anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero mwabwera msanga?”
And when they returned to Raguel their father, he said to them: Why are ye come sooner than usual?
19 Atsikanawo anayankha kuti, “Mwigupto wina ndiye watilanditsa kwa abusa. Ndiponso anatitungira madzi ndi kumwetsa ziweto zathu.”
They answered: A man of Egypt delivered us from the hands of the shepherds: and he drew water also with us, and gave the sheep to drink.
20 Tsono Reueli anafunsa ana ake kuti, “Ndiye ali kuti munthuyo? Chifukwa chiyani mwamusiya? Kamuyitaneni kuti adzadye.”
But he said: Where is he? why have you let the man go? call him that he may eat bread.
21 Mose anavomera kukhala ndi Reueli, ndipo anamupatsa Zipora kuti akhale mkazi wake.
And Moses swore that he would dwell with him. And he took Sephora his daughter to wife:
22 Zipora anabereka mwana wa mwamuna amene Mose anamutcha Geresomu, popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko la eni.”
And she bore him a son, whom he called Gersam, saying: I have been a stranger in a foreign country. And she bore another, whom he called Eliezer, saying: For the God of my father, my helper hath delivered me out of the hand of Pharao.
23 Nthawi yonseyo nʼkuti ana a Israeli akulira chifukwa cha ukapolo wawo uja. Iwo anafuwula kupempha thandizo, ndipo kulira kwawoko kunafika kwa Mulungu.
Now after a long time the king of Egypt died: and the children of Israel groaning, cried out because of the works: and their cry went up unto God from the works.
24 Mulungu anamva kubuwula kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
And he heard their groaning, and remembered the covenant which he made with Abraham, Isaac, and Jacob.
25 Mulungu ataona Aisraeli aja ndi masautso awo, Iye anawamvera chifundo.
And the Lord looked upon the children of Israel, and he knew them.

< Eksodo 2 >