< Eksodo 19 >
1 Ana a Israeli aja anafika ku chipululu cha Sinai pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere mʼdziko la Igupto.
2 Atachoka ku Refidimu, anafika ku Sinai, ndipo Aisraeli anamangako misasa yawo moyangʼanana ndi phirilo.
3 Mose anakwera ku phiri kukakumana ndi Mulungu ndipo Yehova anamuyitana nati, “Ukawuze zidzukulu za Yakobo, ana onse a Israeli kuti,
4 ‘Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine.
5 Tsopano, ngati mumveradi mawu anga ndi kusunga pangano langa, mudzakhala chuma changa chapamtima pakati pa mitundu yonse. Ngakhale kuti dziko lonse lapansi ndi langa,
6 inu mudzakhala ansembe achifumu ndi mtundu woyera mtima. Awa ndi mawu amene uyenera kuwawuza Aisraeli.”
7 Ndipo Mose anabwerera ndi kuyitanitsa akuluakulu. Atabwera anawafotokozera mawu amene Yehova anamulamulira kuti adzanene.
8 Anthu onse anayankha pamodzi kuti, “Ife tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Choncho Mose anabweza yankho lawo kwa Yehova.
9 Yehova anati kwa Mose, “Ine ndibwera kwa iwe mu mtambo wakuda kuti anthu adzandimve ndikuyankhula ndi iwe. Choncho adzakukhulupirira nthawi zonse.” Kenaka Mose anawuza Yehova zimene anthu ananena.
10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa anthu onse ndi kuwayeretsa lero ndi mawa. Achape zovala zawo
11 ndipo akhale atakonzeka pofika tsiku lachitatu, chifukwa tsiku limenelo Yehova adzatsika pa phiri la Sinai anthu onse akuona.
12 Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, ‘Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu.
13 Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndi miyala kapena kumulasa ndi mivi. Palibe amene adzamukhudze. Palibe munthu amene adzaloledwa kukhala ndi moyo ngakhale nyama. Iwo adzayenera kuphedwa.’ Koma anthu adzapita ku phirilo akadzamva kulira kwa lipenga la nyanga yankhosa.”
14 Tsono Mose anatsika phiri lija nafika kwa anthu aja ndi kuwayeretsa. Iwo anachapa zovala zawo.
15 Kenaka iye anati kwa anthu, “Konzekerani tsiku lachitatu, musagone pamodzi ndi mkazi.”
16 Mʼmamawa wa tsiku lachitatu kunali mabingu, ziphaliwali ndi mtambo wakuda umene unaphimba phiri, ndiponso lipenga lolira kwambiri. Aliyense ku misasa kuja ananjenjemera ndi mantha.
17 Ndipo Mose anatsogolera anthu kutuluka mʼmisasa kukakumana ndi Mulungu, ndipo anayima mʼmunsi mwa phiri.
18 Phiri la Sinai linakutidwa ndi utsi, chifukwa Yehova anatsika ndi moto pa phiripo. Utsi unakwera ngati wochokera mʼngʼanjo yamoto ndipo phiri lonse linagwedezeka kwambiri.
19 Liwu la lipenga linkakulirakulira. Tsono Mose anayankhula ndipo Yehova anamuyankha ndi mabingu.
20 Yehova anatsika nafika pamwamba pa phiri la Sinai, ndipo anayitana Mose kuti apite pa phiripo. Choncho Mose anakwera,
21 ndipo Yehova anati kwa iye, “Tsika ukawachenjeze anthu kuti asayesere kudutsa malire kuti adzandione chifukwa ambiri a iwo adzafa.
22 Ngakhale ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova ayenera kudziyeretsa kuopa kuti ndingadzawalange.”
23 Mose anati kwa Yehova, “Anthu sangakwere phiri la Sinai chifukwa inu munatichenjeza. Lembani malire kuzungulira phiri ndipo mulipatule kuti likhale loyera.”
24 Yehova anayankha, “Tsika ukamutenge Aaroni. Koma ansembe ndi anthu asayesere kubzola malire kuti abwere kwa Yehova chifukwa Iye adzawalanga.”
25 Ndipo Mose anatsika ndi kukawawuza anthuwo.