< Eksodo 13 >

1 Yehova anati kwa Mose,
И рече Господь к Моисею глаголя:
2 “Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.”
освяти Ми всякаго первенца перворожденнаго, разверзающаго всякая ложесна в сынех Израилевых от человека до скота, яко Мне есть.
3 Ndipo Mose anati kwa anthu, “Muzikumbukira tsiku lino, tsiku limene munatuluka mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo chifukwa Yehova anakutulutsani ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye kalikonse kamene kali ndi yisiti.
Рече же Моисей к людем: помните день сей, в оньже изыдосте от земли Египетския, из дому работы: рукою бо крепкою изведе вас Господь отсюду: и не ядите квасна,
4 Pa tsiku la lero mwezi uno wa Abibu, mukutuluka mʼdziko la Igupto.
понеже в днешний день исходите в месяце плодов новых:
5 Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanaani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi, muzikachita mwambo uwu mwezi uno.
и будет, егда введет тя Господь Бог твой в землю Хананейску и Хеттейску, и Аморрейску и Евейску, и Иевусейску и Гергесейску и Ферезейску, еюже клятся ко отцем твоим, дати тебе землю точащую млеко и мед, и сотвориши службу сию сего месяца:
6 Muzidzadya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri ndipo tsiku lachisanu ndi chiwirilo muzichita chikondwerero cha Yehova.
шесть дний ядите опресноки, в седмый же день праздник Господу,
7 Mudye buledi wopanda yisiti masiku asanu ndi awiri. Pasapezeke chinthu chilichonse chokhala ndi yisiti pakati panu, kapena paliponse mʼdziko lanu.
опресноки ядите седмь дний: да не явится тебе квасное, ниже будет тебе квас во всех пределех твоих,
8 Tsiku limenelo muzidzawuza ana anu kuti, ‘Ine ndimachita zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira pamene ndimatuluka mʼdziko la Igupto.’
и возвестиши сыну твоему в день он, глаголя: сего ради сотворил Господь Бог мне, егда исхождах из Египта:
9 Lamulo ili lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi chikumbutso choyikidwa pamphumi panu kuti malamulo a Yehova asachoke pakamwa panu. Pakuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.
и будет тебе знамение на руце твоей, и воспоминание пред очима твоима, яко да будет закон Господнь во устех твоих, рукою бо крепкою изведе тя Господь Бог из Египта:
10 Muzichita mwambo uwu pa nthawi yake chaka ndi chaka.
и сохраните закон сей по временом уставленым, от дний до дний,
11 “Yehova akadzakulowetsani ndi kukupatsani dziko la Kanaani monga analonjezera kwa inu ndi makolo anu,
и будет егда введет тя Господь Бог твой в землю Хананейску, якоже кляся отцем твоим, и даст ю тебе:
12 muzikapereka kwa Ambuye ana onse oyamba kubadwa. Ziweto zonse zazimuna zoyamba kubadwa ndi za Ambuye.
и отлучиши всякое разверзающее ложесна, мужеск пол Господу: всякое разверзающее ложесна от стад или от скот твоих, елика будут тебе, мужеск пол освятиши Господу:
13 Koma mwana woyamba kubadwa wa bulu muzikamuwombola ndi mwana wankhosa, koma ngati simukamuwombola, muzikamuthyola khosi. Mwana wamwamuna woyamba kubadwa muzikamuwombola.
всякое разверзающее утробу ослю премениши овцею: аще же не премениши, искупиши е: и всякаго первенца человеча сынов твоих да искупиши:
14 “Mʼtsogolomo mwana wanu akakafunsa kuti, ‘Zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mukamuwuze kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo ndi dzanja lamphamvu.
аще же вопросит тя сын твой по сих, глаголя: что сие? И речеши ему: яко рукою крепкою изведе нас Господь из земли Египетския, из дому работы,
15 Farao atakanitsitsa kuti asatitulutse, Yehova anapha aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira ana a anthu ndi ziweto zomwe. Nʼchifukwa chake ine ndimapereka nsembe kwa Yehova, chachimuna chilichonse choyamba kubadwa ndipo mwana wamwamuna woyamba kubadwa ndimamuwombola.’
егда бо ожесточися фараон отпустити нас, изби Господь всякаго первенца в земли Египетстей, от первенца человеча до первенца скотия: сего ради аз в жертву приношу всякое разверзающее ложесна, мужеск пол Господу, и всякаго первенца сынов моих искуплю,
16 Ndipo chidzakhala kwa inu ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi pamphumi panu kuonetsa kuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.”
и будет в знамение на руце твоей, и непоколебимо пред очесы твоими: рукою бо крепкою изведе тя Господь из Египта.
17 Farao atalola anthu aja kuti atuluke, Mulungu sanawadzeretse njira yodutsa dziko la Afilisti, ngakhale kuti inali yachidule popeza Mulungu anati, “Ngati anthuwa atadzakumana ndi nkhondo angadzakhumudwe ndi kubwerera ku Igupto.”
Егда же отпусти фараон люди, не поведе их Бог путем земли Филистимския, яко близ бяше, ибо рече Бог: да не когда раскаются людие, видевше рать, и возвратятся во Египет.
18 Choncho Mulungu anawadzeretsa anthuwo njira yozungulira ya mʼchipululu kulowera ku Nyanja Yofiira. Komabe Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto atakonzekera nkhondo.
И обведе Бог люди путем, иже в пустыню к Чермному морю. Пятаго же рода изыдоша сынове Израилевы от земли Египетския.
19 Mose ananyamula mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe anawalumbiritsa ana a Israeli. Iye anawawuza kuti, “Mulungu adzabwera ndithu kudzakuthandizani, ndipo mudzanyamule mafupa anga pochoka ku malo ano.”
И взя Моисей кости Иосифовы с собою: клятвою бо закля Иосиф сыны Израилевы, глаголя: присещением присетит вас Господь, и изнесете отсюду кости моя с собою.
20 Atachoka ku Sukoti anakagona ku Etamu mʼmphepete mwa chipululu.
Воздвигшеся же сынове Израилевы от Сокхофа, ополчишася во Офоме при пустыни.
21 Nthawi yamasana Yehova amakhala patsogolo pa anthu kuwatsogolera njira ndi chipilala cha mtambo, ndipo usiku Yehova ankawatsogolera ndi chipilala cha moto, kuwawunikira njira kuti athe kuyenda masana ndi usiku.
Бог же вождаше их, в день убо столпом облачным, показати им путь, нощию же столпом огненным, светити им:
22 Usana, chipilala cha mtambo ndi usiku, chipilala cha moto zinali patsogolo kuwatsogolera anthu aja.
и не оскуде столп облачный во дни и столп огненный нощию пред всеми людьми.

< Eksodo 13 >