< Estere 9 >
1 Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo.
Now in the twelfth month, which is the month of Adar, on the thirteenth day, when the king's law and decree were about to be carried out, on the day when the enemies of the Jews hoped to gain power over them, it was reversed. The Jews gained power over those who hated them.
2 Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha.
The Jews assembled in their cities throughout all the provinces of King Ahasuerus, to lay hands on those who tried to bring disaster on them. No one could stand against them, for the fear of them had fallen on all the peoples.
3 Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai.
All the officials of the provinces, the provincial governors, the governors, and the king's administrators, helped the Jews because the fear of Mordecai had fallen on them.
4 Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe.
For Mordecai was great in the king's house, and his fame spread throughout all the provinces, for the man Mordecai was becoming great.
5 Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo.
The Jews attacked their enemies with the sword, killing and destroying them, and did as they pleased to those who hated them.
6 Ku likulu la mzinda wa Susa, Ayuda anapha ndi kuwononga anthu 500.
In the fortress of Susa itself the Jews killed and destroyed five hundred men.
7 Ayuda anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata,
They killed Parshandatha, Dalphon, Aspatha,
8 Porata, Adaliya, Aridata,
Poratha, Adalia, Aridatha,
9 Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata,
Parmashta, Arisai, Aridai, Vaizatha,
10 ana khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande katundu wawo.
and the ten sons of Haman son of Hammedatha, the enemy of the Jews. But they did not take any plunder.
11 Tsiku lomwelo anawuza mfumu chiwerengero cha anthu amene anaphedwa mu likulu la mzinda wa Susa.
That day the number of those killed in the fortress of Susa, was reported to the king.
12 Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.”
The king said to Queen Esther, “The Jews have killed five hundred men in the fortress of Susa, including the ten sons of Haman. What then have they done in the rest of the king's provinces? Now what is your petition? It will be granted you. What is your request? It will be granted to you.”
13 Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni mfumu, apatseni chilolezo Ayuda okhala mu Susa kuti achitenso zimene achita lerozi mawa, potsata lamulo ndipo mulole kuti ana khumi a Hamani aja mitembo yawo ipachikidwe pa mtanda.”
Esther said, “If it pleases the king, let the Jews who are in Susa be permitted to carry out this day's decree tomorrow also, and let the bodies of Haman's ten sons be hanged on gallows.”
14 Choncho mfumu inalamula kuti izi zichitike. Anapereka lamulo mu Susa ndipo mitembo ya ana khumi a Hamani anayipachika pa mtanda.
So the king commanded that this be done. A decree was issued in Susa, and they hanged the ten sons of Haman.
15 Ayuda a mu mzinda wa Susa anasonkhana pamodzi pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndipo anapha anthu 300 mu Susa, koma sanatenge katundu wawo.
The Jews who were in Susa came together on the fourteenth day of the month of Adar, and killed three hundred more men in Susa, but laid no hands on the plunder.
16 Tsono Ayuda ena onse amene anali mu zigawo za mfumu anasonkhananso kudziteteza ndipo sanasautsidwenso ndi adani popeza anapha anthu 75,000 koma sanalande zofunkha zawo.
The rest of the Jews who were in the king's provinces came together to defend their lives, and they got relief from their enemies and killed seventy-five thousand of those who hated them, but they did not lay their hands on the valuables of those they killed.
17 Zonsezi zinachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara ndipo pa tsiku la 14 anapumula ndi kupanga tsikuli kuti likhale la madyerero ndi chikondwerero.
This happened on the thirteenth day of the month of Adar. On the fourteenth day they rested and made that a day of feasting and gladness.
18 Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero.
But the Jews who were in Susa assembled together on the thirteenth and the fourteenth days. On the fifteenth day they rested and made it a day of feasting and gladness.
19 Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso.
That is why the Jews of the villages, who make their homes in the rural towns, observe the fourteenth day of the month of Adar as a day of gladness and feasting, and as a day on which they send gifts of food to one another.
20 Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali:
Mordecai recorded these things and sent letters to all the Jews who were in all the provinces of King Ahasuerus, both near and far,
21 Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara,
obligating them to keep the fourteenth and the fifteenth day of Adar every year.
22 ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka.
These were the days when the Jews got relief from their enemies, and the month when their sorrow turned to joy, and mourning into a day of celebration. They were to make them days of feasting and gladness, and of sending gifts of food to one another, and gifts to the poor.
23 Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai.
So the Jews continued the celebration they had begun, doing what Mordecai had written to them.
24 Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, mdani wa Ayuda onse, anakonza chiwembu chakupha ndi kuwononga Ayuda ndipo anachita maere otchedwa Purimu kuti awaphe ndi kuwawononga.
At that time Haman son of Hammedatha the Agagite, the enemy of all the Jews, had plotted against the Jews to destroy them, and he threw Pur (that is, he threw lots), to crush and destroy them.
25 Koma mfumu itazindikira za chiwembuchi, inalamula kuti zilembedwe mʼmakalata kuti chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda chigwere pa iye mwini, ndi kuti iye pamodzi ndi ana ake apachikidwe pa mtanda.
But when the matter came before the king, he gave orders by letters that the wicked plan Haman developed against the Jews should come back on his own head, and that he and his sons should be hanged on the gallows.
26 Ndi chifukwa chake masiku amenewa amatchedwa masiku a Purimu potsata dzina lakuti Purimu. Chifukwa cha kalata ya Mordekai ndiponso chifukwa cha zimene anaziona ndi kuwachitikira,
Therefore they called these days Purim, after the name of Pur. Because of everything that was written in this letter, and everything that they had seen and that had happened to them,
27 Ayuda onse anagwirizana kukhazikitsa lamulo lokhudza iwo, zidzukulu zawo ndi onse amene adzapanga nawo ubale kuti asalephere kusunga masiku awiri amenewa chaka chilichonse monga zinalembedweramo ndiponso potsata nthawi imene anayika.
the Jews accepted a new custom and duty. This custom would be for themselves, their descendants, and everyone who joined them. It would be that they would celebrate these two days every year. They would celebrate them in a certain way and at the same time each year.
28 Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira.
These days were to be celebrated and observed in every generation, every family, every province, and every city. These Jews and their descendants would never cease to faithfully observe these days of Purim, so that they should never forget them.
29 Choncho mfumukazi Estere, mwana wa mkazi wa Abihaili, pamodzi ndi Mordekai Myuda analemba ndi ulamuliro onse kutsimikizira kalata iyi yachiwiri yokhudza Purimu.
Queen Esther daughter of Abihail and Mordecai the Jew wrote with full authority and confirmed this second letter about Purim.
30 Ndipo Mordekai anatumiza makalata kwa Ayuda onse ku zigawo 127 za ufumu wa Ahasiwero. Kalatayi inali ya mawu a mtendere ndiponso a kukhulupirika
Letters were sent to all the Jews in the 127 provinces of the kingdom of Ahasuerus, wishing the Jews safety and truth.
31 kuti azisunga masiku a Purimu pa nyengo imene inavomerezeka monga mmene Mordekai Myuda ndi mfumukazi Estere anawalamulira ndiponso monga anadziyikira eni okha ndi zidzukulu zawo zonena za nthawi zawo za kusala zakudya ndi kulira.
These letters confirmed the days of Purim at their appointed times, as Mordecai the Jew and Queen Esther obligated the Jews. The Jews accepted this obligation for themselves and their descendants, just as also they accepted times of fasting and lamenting.
32 Lamulo la Estere linakhazikitsa mwambo wa Purimuwu ndipo zinalembedwa mʼmabuku.
The command of Esther confirmed these regulations regarding Purim, and it was written in the book.