< Aefeso 5 >
1 Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu.
2 Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.
3 Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu.
4 Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika.
5 Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.
6 Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera.
7 Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere.
8 Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika
9 (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi).
10 Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye.
11 Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse.
12 Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri.
13 Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala.
14 Nʼchifukwa chake Malemba akuti, “Dzuka, wamtulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuwalira.”
15 Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru.
16 Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa.
17 Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite.
18 Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.
19 Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu.
20 Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
21 Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu.
22 Inu akazi, muzigonjera amuna anu, monga mumagonjera kwa Ambuye.
23 Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake.
24 Tsono monga mpingo umagonjera Khristu, momwemonso akazi akuyenera kugonjera amuna awo mu zonse.
25 Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo
26 kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake.
27 Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro.
28 Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha.
29 Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake
30 pakuti ndife ziwalo za thupi lake.
31 “Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”
32 Ichi ndi chinsinsi chozama, koma ine ndikunena za Khristu ndi mpingo.
33 Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.