< Aefeso 3 >
1 Nʼchifukwa chake ine Paulo, ndili wamʼndende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu anthu a mitundu ina.
For this cause I, Paul, am the prisoner of Christ Jesus on behalf of you Gentiles,
2 Ndithudi, inu munamva za ntchito yachisomo cha Mulungu imene anandipatsa chifukwa cha inu,
if it is so that you have heard of the administration of that grace of God which was given me toward you,
3 ndicho chinsinsi chimene chinawululidwa kwa ine mwa vumbulutso, monga ndinakulemberani kale mwachidule.
how that by revelation the mystery was made known to me, as I wrote before in few words,
4 Pamene mukuwerenga izi, inu mudzazindikira za chidziwitso changa pa chinsinsi cha Khristu,
by which, when you read, you can perceive my understanding in the mystery of Christ,
5 chimene sichinawululidwe kwa anthu amibado ina monga momwe tsopano chawululidwa ndi Mzimu wa Mulungu mwa atumwi oyera ndi aneneri.
which in other generations was not made known to the children of men, as it has now been revealed to his holy apostles and prophets in the Spirit,
6 Chinsinsicho nʼchakuti, kudzera mu Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina ndi olowamʼmalo pamodzi ndi Aisraeli, ndi ziwalo za thupi limodzi, ndi olandira nawo pamodzi malonjezo a mwa Khristu Yesu.
that the Gentiles are fellow heirs and fellow members of the body, and fellow partakers of his promise in Christ Jesus through the Good News,
7 Mwachisomo cha Mulungu ndi mphamvu zake, ine ndinasanduka mtumiki wa Uthenga Wabwinowu.
of which I was made a servant according to the gift of that grace of God which was given me according to the working of his power.
8 Ngakhale ndili wamngʼono kwambiri pakati pa anthu onse a Mulungu, anandipatsa chisomo chimenechi cholalikira kwa anthu a mitundu ina chuma chopanda malire cha Khristu.
To me, the very least of all saints, was this grace given, to preach to the Gentiles the unsearchable riches of Christ,
9 Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse. (aiōn )
and to make all men see what is the administration of the mystery which for ages has been hidden in God, who created all things through Jesus Christ, (aiōn )
10 Cholinga chake tsopano nʼchakuti, kudzera mwa mpingo, mafumu ndi a ulamuliro onse a kumwamba adziwe nzeru zochuluka za Mulungu.
to the intent that now through the assembly the manifold wisdom of God might be made known to the principalities and the powers in the heavenly places,
11 Chimenechi chinali chikonzero chamuyaya cha Mulungu, chimene chinachitika kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye athu. (aiōn )
according to the eternal purpose which he accomplished in Christ Jesus our Lord. (aiōn )
12 Mwa Khristu ndi mwa chikhulupiriro chathu mwa Iye, timayandikira kwa Mulungu momasuka ndi molimbika mtima.
In him we have boldness and access in confidence through our faith in him.
13 Choncho, ine ndikukupemphani kuti musakhumudwe popeza ndikusautsidwa chifukwa cha inu pakuti masautso angawa ndi ulemerero wanu.
Therefore I ask that you may not lose heart at my troubles for you, which are your glory.
14 Nʼchifukwa chake ine ndikugwada pamaso pa Atate,
For this cause, I bow my knees to the Father of our Lord Jesus Christ,
15 amene banja lililonse kumwamba ndi pa dziko lapansi limatchulidwa ndi dzina lawo.
from whom every family in heaven and on earth is named,
16 Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake,
that he would grant you, according to the riches of his glory, that you may be strengthened with power through his Spirit in the inner person,
17 kuti Khristu akhazikike mʼmitima mwanu mwachikhulupiriro. Ndipo ndikukupemphererani kuti muzikike ndi kukhazikika mʼchikondi
that Christ may dwell in your hearts through faith, to the end that you, being rooted and grounded in love,
18 kuti mukhale ndi mphamvu, kuti pamodzi ndi anthu oyera mtima onse muthe kuzindikira kupingasa, kutalika ndi kukwera komanso kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu.
may be strengthened to comprehend with all the saints what is the width and length and height and depth,
19 Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.
and to know Christ’s love which surpasses knowledge, that you may be filled with all the fullness of God.
20 Tsopano kwa Iye amene angathe kuchita zochuluka kuposa zimene tingapemphe, kapena kuganiza molingana ndi mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwa ife,
Now to him who is able to do exceedingly abundantly above all that we ask or think, according to the power that works in us,
21 Iyeyo akhale ndi ulemu mu mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibado yonse mpaka muyaya. Ameni. (aiōn )
to him be the glory in the assembly and in Christ Jesus to all generations, forever and ever. Amen. (aiōn )