< Aefeso 2 >

1 Kunena za inu, kale munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu,
І вас, що мертві були через ваші провини й гріхи,
2 mmene inu munkakhalamo pamene munkatsatira njira za dziko lapansi ndi za ulamuliro waufumu wa mlengalenga, mzimu umene ukugwira ntchito tsopano mwa amene samvera. (aiōn g165)
в яких ви колись проживали за звича́єм віку цього́, за волею князя, що панує в повітрі, духа, що працює тепер у неслухня́них, (aiōn g165)
3 Nthawi ina tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, tinkachitanso zilizonse zimene matupi ndi maganizo athu ankafuna. Mwachibadwa chathu, tinali oyenera chilango monga anthu ena onse.
між якими й усі ми проживали колись у пожадливостях нашого тіла, як чинили волю тіла й думо́к, і з природи були дітьми́ гніву, як і інші, -
4 Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo,
Бог же, багатий на милосердя, через Свою превелику любов, що нею Він нас полюбив,
5 anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo.
і нас, що мертві були через прогріхи, оживив ра́зом із Христом, — спасені ви благода́ттю, -
6 Ndipo Mulungu anatiukitsa pamodzi ndi Khristu ndi kutikhazika pamodzi ndi Iye mmwamba mwa Khristu Yesu,
і ра́зом із Ним воскресив, і ра́зом із Ним посадив на небесних місцях у Христі Ісусі,
7 ndi cholinga chakuti mʼnthawi imene ikubwera, Iyeyo adzaonetse chuma choposa cha chisomo chake, choonetsedwa mwa kukoma mtima kwake kwa ife mwa Khristu Yesu. (aiōn g165)
щоб у наступних віках показати безмірне багатство благода́ті Своєї в до́брості до нас у Христі Ісусі. (aiōn g165)
8 Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu,
Бо спасені ви благода́ттю через віру, а це не від вас, то дар Божий,
9 osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire.
не від діл, щоб ніхто не хвалився.
10 Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.
Бо ми — Його тво́риво, ство́рені в Христі Ісусі на добрі діла, які Бог наперед приготува́в, щоб ми в них перебува́ли.
11 Chifukwa chake kumbukirani kuti poyamba inu amene munali anthu a mitundu ina mwachibadwa ndipo munkatchedwa “osachita mdulidwe” ndi amene amadzitcha okha “a mdulidwe” (zimene zinachitika mʼthupi ndi manja a anthu).
Отож, пам'ятайте, що ви, колись тілом погани, що вас так звані рукотворно „обрізані“на тілі звуть „необрізаними“,
12 Kumbukirani kuti nthawi imene inu munali wopanda Khristu, simunkawerengedwa ngati nzika za Israeli ndipo munali alendo pa pangano la lonjezo, wopanda chiyembekezo ndi opanda Mulungu mʼdziko lapansi.
що ви того ча́су були́ без Христа, відлучені від громади ізра́їльської, і чужі заповітам обі́тниці, не мавши надії й без Бога на світі.
13 Koma tsopano mwa Khristu Yesu, inu amene nthawi ina munali kutali, mwabweretsedwa pafupi kudzera mʼmagazi a Khristu.
А тепер у Христі Ісусі ви, що колись далекі були́, стали близькі́ Христовою кров'ю.
14 Pakuti Iye mwini ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti awiri akhale mmodzi ndipo anagumula chotchinga, khoma la udani lotilekanitsa,
Він бо наш мир, що вчинив із двох одне й зруйнував середи́нну перегороду, ворожнечу, Своїм тілом, -
15 pothetsa mʼthupi lake lamulo pamodzi ndi zolamulira zake ndi malangizo. Cholinga chake chinali chakuti alenge mwa Iye mwini, munthu mmodzi watsopano kuchokera kwa abwino, motero nʼkupanga mtendere,
Він Своєю наукою знищив Зако́на заповідей, щоб з обох збудувати Собою одно́го ново́го чоловіка, мир чинивши,
16 ndi kuyanjanitsa onse awiriwa mʼthupi lake kwa Mulungu, kudzera pa mtanda, umene Iye anaphapo udani wawo.
і хрестом примирити із Богом обох в однім тілі, ворожнечу на ньому забивши.
17 Iye anabwera ndipo analalikira mtendere kwa inu amene munali kutali ndi mtendere ndiponso kwa iwonso amene anali pafupi.
І, прийшовши, „Він благовісти́в мир вам, далеким, і мир близьки́м“,
18 Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi.
бо обоє Ним маємо при́ступ у Дусі однім до Отця.
19 Kotero kuti, inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso a mʼbanja la Mulungu.
Отже, ви вже не чужі й не прихо́дьки, а співгорожа́ни святим, і домашні для Бога,
20 Ndinu okhazikika pa maziko a atumwi ndi a aneneri, pamodzi ndi Khristu Yesu mwini ngati mwala wa pa ngodya.
збудовані на основі апо́столів і пророків, де наріжним каменем є Сам Ісус Христос,
21 Mwa Iyeyo, nyumba yonse yalumikizidwa pamodzi ndipo yakwezedwa kukhala Nyumba yoyera mwa Ambuye.
що на ньому вся буді́вля, улад побудована, росте в святий храм у Господі,
22 Ndipo mwa Iye, inunso mukamangidwa pamodzi ndi ena onse kukhala nyumba yokhalamo imene Mulungu amakhala mwa Mzimu wake.
що на ньому і ви ра́зом будуєтеся Духом на оселю Божу.

< Aefeso 2 >