< Mlaliki 7 >
1 Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino, ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
2 Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro kusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero: Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense; anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo.
3 Chisoni nʼchabwino kusiyana ndi kuseka, pakuti nkhope yakugwa ndi yabwino chifukwa imakonza mtima.
4 Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa, koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo.
5 Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru.
6 Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mʼphika, izinso ndi zopandapake.
7 Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru, ndipo chiphuphu chimawononga mtima.
8 Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake, ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza.
9 Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako, pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.
10 Usamafunse kuti, “Nʼchifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?” pakuti si chinthu chanzeru kufunsa mafunso oterewa.
11 Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwino ndipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.
12 Nzeru ndi chitetezo, monganso ndalama zili chitetezo, koma phindu la chidziwitso ndi ili: kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.
13 Taganizirani zimene Mulungu wazichita: ndani angathe kuwongola chinthu chimene Iye anachipanga chokhota?
14 Pamene zinthu zili bwino, sangalala; koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino: Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo, ndiponso nthawi imene si yabwinoyo. Choncho munthu sangathe kuzindikira chilichonse cha mʼtsogolo mwake.
15 Pa moyo wanga wopanda phinduwu ndaona zinthu ziwiri izi: munthu wolungama akuwonongeka mʼchilungamo chake, ndipo munthu woyipa akukhala moyo wautali mʼzoyipa zake.
16 Usakhale wolungama kwambiri kapena wanzeru kwambiri, udziwonongerenji wekha?
17 Usakhale woyipa kwambiri, ndipo usakhale chitsiru, uferenji nthawi yako isanakwane?
18 Nʼkwabwino kuti utsate njira imodzi, ndipo usataye njira inayo. Munthu amene amaopa Mulungu adzapewa zinthu ziwiri zonsezi.
19 Nzeru zimapereka mphamvu zambiri kwa munthu wanzeru kupambana olamulira khumi a mu mzinda.
20 Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.
21 Usamamvetsere mawu onse amene anthu amayankhula, mwina udzamva wantchito wako akukutukwana,
22 pakuti iwe ukudziwa mu mtima mwako kuti nthawi zambiri iwenso unatukwanapo ena.
23 Zonsezi ndinaziyesa ndi nzeru zanga ndipo ndinati, “Ine ndatsimikiza mu mtima mwanga kuti ndikhale wanzeru,” koma nzeruyo inanditalikira.
24 Nzeru zimene zilipo, zili kutali ndipo ndi zozama kwambiri, ndani angathe kuzidziwa?
25 Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalira ndipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa misala.
26 Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa, mkazi amene ali ngati khoka, amene mtima wake uli ngati khwekhwe, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo, koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.
27 Mlaliki akunena kuti, “Taonani, chimene ndinachipeza ndi ichi: “Kuwonjezera chinthu china pa china kuti ndidziwe mmene zinthu zimachitikira,
28 pamene ine ndinali kufufuzabe koma osapeza kanthu, ndinapeza munthu mmodzi wolungama pakati pa anthu 1,000, koma pakati pawo panalibepo mkazi mmodzi wolungama.
29 Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi: Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama, koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”