< Mlaliki 6 >

1 Ine ndinaona choyipa china pansi pano, ndipo chimasautsa anthu kwambiri:
我観るに日の下に一件の患あり是は人の間に恒なる者なり
2 Mulungu amapereka chuma, zinthu ndi ulemu kwa munthu, kotero kuti munthuyo sasowa kanthu kalikonse kamene akukalakalaka, koma Mulungu samulola kuti adyerere zinthuzo, ndipo mʼmalo mwake amadyerera ndi mlendo. Izi ndi zopandapake, ndi zoyipa kwambiri.
すなはち神富と財と貴を人にあたへて その心に慕ふ者を一件もこれに欠ることなからしめたまひながらも 神またその人に之を食ふことを得せしめたまはずして 他人のこれを食ことあり 是空なり惡き疾なり
3 Ngakhale munthu atabereka ana 100 ndi kukhala ndi moyo zaka zambiri; komatu ngakhale atakhala zaka zambiri chotani, ngati iye sangadyerere chuma chake ndi kuyikidwa mʼmanda mwaulemu, ine ndikuti mtayo umamuposa iyeyo.
仮令人百人の子を挙けまた長壽してその年齢の日多からんも 若その心景福に満足せざるか又は葬らるることを得ざるあれば 我言ふ流産の子はその人にまさるたり
4 Mtayo umangopita pachabe ndipo umapita mu mdima, ndipo mu mdimamo dzina lake limayiwalika.
夫流産の子はその來ること空しくして黒暗の中に去ゆきその名は黒暗の中にかくるるなり
5 Ngakhale kuti mtayowo sunaone dzuwa kapena kudziwa kanthu kalikonse, koma umapumula kuposa munthu uja,
又是は日を見ることなく物を知ることなければ彼よりも安泰なり
6 ngakhale munthuyo atakhala ndi moyo zaka 2,000, koma ndi kulephera kudyerera chuma chake. Kodi onsewa sapita malo amodzi?
人の壽命千年に倍するとも福祉を蒙れるにはあらず 皆一所に往くにあらずや
7 Ntchito yonse ya munthu imathera pakamwa pake, komatu iye sakhutitsidwa ndi pangʼono pomwe.
人の労苦は皆その口のためなり その心はなほも飽ざるところ有り
8 Kodi munthu wanzeru amaposa motani chitsiru? Kodi munthu wosauka amapindula chiyani podziwa kukhala bwino pamaso pa anthu ena?
賢者なんぞ愚者に勝るところあらんや また世人の前に歩行ことを知ところの貧者も何の勝るところ有んや
9 Kuli bwino kumangoona zinthu ndi maso kusiyana ndi kumangozilakalaka mu mtima. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
目に観る事物は心のさまよひ歩くに愈るなり 是また空にして風を捕ふるがごとし
10 Chilichonse chimene chilipo anachitchula kale dzina, za mmene munthu alili nʼzodziwika; sangathe kutsutsana ndi munthu amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.
嘗て在し者は久しき前にすでにその名を命られたり 即ち是は人なりと知る 然ば是はかの自己よりも力強き者と争ふことを得ざるなり
11 Mawu akachuluka zopandapake zimachulukanso, nanga munthu zimamupindulira chiyani?
衆多の言論ありて虚浮き事を増す然ど人に何の益あらんや
12 Pakuti ndani amene amadziwa chomwe ndi chabwino pa moyo wa munthu, pakuti moyo wake ndi wa masiku ochepa ndi opandapake, umangopitira ngati mthunzi. Ndani amene angamufotokozere zimene zidzachitika pansi pano iye atapita?
人はその虚空き生命の日を影のごとくに送るなり 誰かこの世において如何なる事か人のために善き者なるやを知ん 誰かその身の後に日の下にあらんところの事を人に告うる者あらんや

< Mlaliki 6 >