< Mlaliki 5 >
1 Uzisamala mayendedwe ako pamene ukupita ku nyumba ya Mulungu. Upite pafupi kuti ukamvetsere mʼmalo mopereka nsembe ya zitsiru zimene sizizindikira kuti zikuchita zolakwa.
2 Usamafulumire kuyankhula, usafulumire mu mtima mwako kunena chilichonse pamaso pa Mulungu. Mulungu ali kumwamba ndipo iwe uli pa dziko lapansi, choncho mawu ako akhale ochepa.
3 Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oyipa, ndipo kuchuluka kwa mawu kumadzetsa uchitsiru.
4 Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako.
5 Kuli bwino kusalumbira kusiyana ndi kulumbira koma osakwaniritsa lumbirolo.
6 Pakamwa pako pasakuchimwitse. Ndipo usanene kwa mthenga wa mʼNyumba ya Mulungu kuti, “Ndinalakwitsa polumbira.” Chifukwa chiyani ukufuna Mulungu akwiye ndi mawu ako ndiponso ntchito ya manja ako?
7 Maloto ochuluka ndi mawu ochuluka ndi zinthu zopandapake. Kotero lemekeza Mulungu.
8 Ngati uwona anthu osauka akuzunzika mʼdziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzawo ndi kuwalanda ufulu wawo, usadabwe ndi zinthu zimenezi; pakuti woyangʼanira ali naye wina womuyangʼanira wamkulu, ndipo pamwamba pa awiriwa pali ena akuluakulu owaposa.
9 Anthu onse amatengako zokolola za mʼminda: koma ndi mfumu yokha imene imapeza phindu la mindayi.
10 Aliyense amene amakonda ndalama sakhutitsidwa ndi ndalamazo; aliyense amene amakonda chuma sakhutitsidwa ndi zimene amapeza. Izinso ndi zopandapake.
11 Chuma chikachuluka akudya nawo chumacho amachulukanso. Nanga mwini wake amapindulapo chiyani kuposa kumangochiyangʼana ndi maso ake?
12 Wantchito amagona tulo tabwino ngakhale adye pangʼono kapena kudya kwambiri, koma munthu wolemera, chuma sichimulola kuti agone.
13 Ine ndinaona choyipa chomvetsa chisoni pansi pano: chuma chokundikidwa chikupweteka mwini wake yemwe,
14 kapena chuma chowonongedwa pa nthawi yatsoka, kotero kuti pamene wabereka mwana alibe kanthu koti amusiyire.
15 Munthu anabadwa wamaliseche kuchokera mʼmimba mwa amayi ake, ndipo monga iye anabadwira, adzapitanso choncho. Pa zonse zimene iye anakhetsera thukuta palibe nʼchimodzi chomwe chimene adzatenge mʼmanja mwake.
16 Izinso ndi zoyipa kwambiri: munthu adzapita monga momwe anabwerera, ndipo iye amapindula chiyani, pakuti amagwira ntchito yolemetsa yopanda phindu?
17 Masiku ake onse ndi odzaza ndi mdima, kukhumudwa kwakukulu, masautso ndi nkhawa.
18 Tsono ndinazindikira kuti nʼchabwino ndi choyenera kuti munthu azidya ndi kumwa, ndi kukhutitsidwa ndi ntchito yake yolemetsa imene amayigwira pansi pano pa nthawi yake yochepa imene Mulungu amamupatsa, poti ichi ndiye chake.
19 Komatu pamene Mulungu apereka chuma kwa munthu aliyense ndi zinthu zina, ndi kulola kuti akondwere ndi chumacho, munthuyo alandire chumacho ndi kusangalala ndi ntchito yake, imene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.
20 Munthu wotereyu saganizirapo za masiku a moyo wake, chifukwa Mulungu amamutanganidwitsa ndi chisangalalo cha mu mtima mwake.