< Mlaliki 4 >
1 Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano: ndinaona misozi ya anthu opsinjika, ndipo iwo alibe owatonthoza; mphamvu zinali ndi anthu owapsinjawo ndipo iwonso analibe owatonthoza.
Then I returned and saw all the oppressions that are done under the sun: and behold, the tears of such as were oppressed, and they had no comforter; and on the side of their oppressors there was power, but they had no comforter.
2 Ndipo ndinanena kuti akufa, amene anafa kale, ndi osangalala kuposa amoyo, amene akanalibe ndi moyo.
Wherefore I praised the dead which are already dead more than the living which are yet alive;
3 Koma wopambana onsewa ndi amene sanabadwe, amene sanaone zoyipa zimene chimachitika pansi pano.
yea, better than them both [did I esteem] him which hath not yet been, who hath not seen the evil work that is done under the sun.
4 Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
Then I saw all labour and every skilful work, that for this a man is envied of his neighbour. This also is vanity and a striving after wind.
5 Chitsiru chimangoti manja ake lobodo ndi kudzipha chokha ndi njala.
The fool foldeth his hands together, and eateth his own flesh.
6 Nʼkwabwino kukhala ndi dzanja limodzi lodzaza uli pa mtendere, kuposa kukhala ndi manja awiri odzaza uli pa mavuto, ndipo uku nʼkungodzivuta chabe.
Better is an handful with quietness, than two handfuls with labour and striving after wind.
7 Ndinaonanso chinthu china chopanda phindu pansi pano:
Then I returned and saw vanity under the sun.
8 Panali munthu amene anali yekhayekha; analibe mwana kapena mʼbale. Ntchito yake yolemetsa sinkatha, ndipo maso ake sankakhutitsidwa ndi chuma chake. Iye anadzifunsa kuti, “Kodi ntchito yosautsayi ndikuyigwirira yani? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikudzimana chisangalalo?” Izinso ndi zopandapake, zosasangalatsa!
There is one that is alone, and he hath not a second; yea, he hath neither son nor brother; yet is there no end of all his labour, neither are his eyes satisfied with riches. For whom then, [saith he], do I labour, and deprive my soul of good? This also is vanity, yea, it is a sore travail.
9 Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:
Two are better than one; because they have a good reward for their labour.
10 Ngati winayo agwa, mnzakeyo adzamudzutsa. Koma tsoka kwa munthu amene agwa ndipo alibe wina woti amudzutse!
For if they fall, the one will lift up his fellow: but woe to him that is alone when he falleth, and hath not another to lift him up.
11 Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana. Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?
Again, if two lie together, then they have warmth: but how can one be warm [alone]?
12 Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa, koma anthu awiri akhoza kudziteteza. Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.
And if a man prevail against him that is alone, two shall withstand him; and a threefold cord is not quickly broken.
13 Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo.
Better is a poor and wise youth than an old and foolish king, who knoweth not how to receive admonition any more.
14 Wachinyamatayo angathe kuchokera ku ndende ndi kudzakhala mfumu, kapena angathe kubadwa wosauka mʼdziko la mfumuyo.
For out of prison he came forth to be king; yea, even in his kingdom he was born poor.
15 Ndipo ndinaona kuti iwo onse amene anakhala ndi moyo ndi kuyenda pansi pano anatsatira wachinyamatayo, amene anatenga malo a mfumu.
I saw all the living which walk under the sun, that they were with the youth, the second, that stood up in his stead.
16 Mfumu ikhoza kulamulira anthu osawerengeka, komabe itamwalira, palibe amene adzayamikire zomwe mfumuyo inachita. Izinso ndi zopandapake, nʼkungozivuta chabe.
There was no end of all the people, even of all them over whom he was: yet they that come after shall not rejoice in him. Surely this also is vanity and a striving after wind.