< Mlaliki 3 >
1 Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake, ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:
2 Nthawi yobadwa ndi nthawi yomwalira, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola.
3 Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa, nthawi yogwetsa ndi nthawi yomanga.
4 Nthawi yomva chisoni ndi nthawi yosangalala, nthawi yolira maliro ndi nthawi yovina.
5 Nthawi yotaya miyala ndi nthawi yokundika miyala, nthawi yokumbatirana ndi nthawi yoleka kukumbatirana.
6 Nthawi yofunafuna ndi nthawi yoleka kufunafuna, nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.
7 Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka, nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyankhula.
8 Nthawi yokondana ndi nthawi yodana, nthawi ya nkhondo ndi nthawi ya mtendere.
9 Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa?
10 Ine ndinaona chipsinjo chimene Mulungu anayika pa anthu.
11 Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro.
12 Ine ndikudziwa kuti palibenso kanthu kabwino kwa anthu kopambana kusangalala ndi kuchita zabwino pamene ali ndi moyo.
13 Ndi mphatso ya Mulungu kwa munthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ndi ntchito zake zolemetsa.
14 Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.
15 Chilichonse chimene chilipo chinalipo kale, ndipo chimene chidzakhalapo chinalipo poyamba; Mulungu amabwezanso zakale zimene zinapita kuti zichitikenso.
16 Ndipo ndinaona chinthu chinanso pansi pano: ku malo achiweruzo, kuyipa mtima kuli komweko, ku malo achilungamo, kuyipa mtima kuli komweko.
17 Ndinalingalira mu mtima mwanga kuti; “Mulungu adzaweruza olungama pamodzi ndi oyipa omwe, pakuti anayika nthawi yochitikira chinthu chilichonse, nthawi ya ntchito iliyonse.”
18 Ndinalingaliranso kuti, “Kunena za anthu, Mulungu amawayesa ndi cholinga choti awaonetse kuti iwo ali ngati nyama.
19 Zimene zimachitikira munthu, zomwezonso zimachitikira nyama; chinthu chimodzi chomwecho chimachitikira onse: Monga munthu amafa momwemonso nyama imafa. Zonsezi zimapuma mpweya umodzimodzi omwewo; munthu saposa nyama. Zonsezi ndi zopandapake.
20 Zonse zimapita kumodzimodzi; zonsezi zimachokera ku fumbi, ndipo zimabwereranso ku fumbi komweko.
21 Kodi ndani amene amadziwa ngati mzimu wa munthu umakwera kumwamba, ndipo mzimu wa nyama umatsikira kunsi kwa dziko?”
22 Kotero ndinaona kuti palibe chinthu chabwino kwa munthu kuposa kuti munthu azisangalala ndi ntchito yake, pakuti ichi ndiye chake chenicheni. Pakuti ndani amene angamubweretse kuti adzaone zimene zidzamuchitikira iye akadzamwalira?