< Mlaliki 11 >

1 Ponya chakudya chako pa madzi, udzachipezanso patapita masiku ambiri.
Cast your bread on the waters; for you shall find it after many days.
2 Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu, pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.
Give a portion to seven, yes, even to eight; for you do not know what evil will be on the earth.
3 Ngati mitambo yadzaza ndi madzi, imagwetsa mvula pa dziko lapansi. Mtengo ukagwera cha kummwera kapena cha kumpoto, ndiye kuti udzagonera kumene wagwerako.
If the clouds are full of rain, they empty themselves on the earth; and if a tree falls toward the south, or toward the north, in the place where the tree falls, there shall it be.
4 Amene amayangʼana mphepo sadzadzala; amene amayangʼana mitambo sadzakolola.
He who observes the wind won't sow; and he who regards the clouds won't reap.
5 Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo, kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi, momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu, Mlengi wa zinthu zonse.
As you do not know what is the way of the wind, nor how the bones grow in the womb of her who is with child; even so you do not know the work of God who does all.
6 Dzala mbewu zako mmawa ndipo madzulo usamangoti manja lobodo, pakuti sudziwa chimene chidzapindula, mwina ichi kapena icho, kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.
In the morning sow your seed, and in the evening do not withhold your hand; for you do not know which will prosper, whether this or that, or whether they will both be equally good.
7 Kuwala nʼkwabwino, ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.
Truly the light is sweet, and a pleasant thing it is for the eyes to see the sun.
8 Munthu akakhala wa zaka zambiri, mulekeni akondwerere zaka zonsezo, koma iye azikumbukira masiku a mdima, pakuti adzakhala ochuluka. Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.
Yes, if a man lives many years, let him rejoice in them all; but let him remember the days of darkness, for they shall be many. All that comes is vanity.
9 Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono, ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako. Tsatira zimene mtima wako ukufuna, ndiponso zimene maso ako akuona, koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo Mulungu adzakuweruza.
Rejoice, young man, in your youth, and let your heart cheer you in the days of your youth, and walk in the ways of your heart, and in the sight of your eyes; but know that for all these things God will bring you into judgment.
10 Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako, upewe zokupweteka mʼthupi mwako, pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.
Therefore remove sorrow from your heart, and put away evil from your flesh; for youth and the dawn of life are vanity.

< Mlaliki 11 >