< Mlaliki 1 >

1 Mawu a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu:
דברי קהלת בן דוד מלך בירושלם
2 “Zopandapake! Zopandapake!” atero Mlaliki. “Zopandapake kotheratu! Zopandapake.”
הבל הבלים אמר קהלת הבל הבלים הכל הבל
3 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zake zonse zimene amasautsidwa nazo pansi pano?
מה יתרון לאדם בכל עמלו--שיעמל תחת השמש
4 Mibado imabwera ndipo mibado imapita, koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse.
דור הלך ודור בא והארץ לעולם עמדת
5 Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa ndipo limapita mwamsanga kumene limatulukira.
וזרח השמש ובא השמש ואל מקומו--שואף זורח הוא שם
6 Mphepo imawombera cha kummwera ndi kukhotera cha kumpoto; imawomba mozungulirazungulira, kumangobwererabwerera komwe yachokera.
הולך אל דרום וסובב אל צפון סובב סבב הולך הרוח ועל סביבתיו שב הרוח
7 Mitsinje yonse imakathira ku nyanja, koma nyanjayo sidzaza; kumene madziwo amachokera, amabwereranso komweko.
כל הנחלים הלכים אל הים והים איננו מלא אל מקום שהנחלים הלכים--שם הם שבים ללכת
8 Zinthu zonse ndi zotopetsa, kutopetsa kwake ndi kosaneneka. Maso satopa ndi kuona kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.
כל הדברים יגעים לא יוכל איש לדבר לא תשבע עין לראות ולא תמלא אזן משמע
9 Zomwe zinalipo kale zidzakhalaponso, zomwe zinachitika kale zidzachitikanso. Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
מה שהיה הוא שיהיה ומה שנעשה הוא שיעשה ואין כל חדש תחת השמש
10 Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti, “Taona! Ichi ndiye chatsopano?” Chinalipo kale, kalekale; chinalipo ife kulibe.
יש דבר שיאמר ראה זה חדש הוא כבר היה לעלמים אשר היה מלפננו
11 Anthu akale sakumbukiridwa, ngakhale amene adzabwera mʼtsogolomu sadzakumbukiridwa ndi iwo amene adzabwere pambuyo pawo.
אין זכרון לראשנים וגם לאחרנים שיהיו לא יהיה להם זכרון--עם שיהיו לאחרנה
12 Ine, Mlalikine, ndinali mfumu ya Israeli mu Yerusalemu.
אני קהלת הייתי מלך על ישראל--בירושלם
13 Ndinayika mtima wanga pophunzira ndi kufunafuna mwa nzeru zinthu zonse zimene zimachitika pansi pa thambo. Ndi ntchito yolemetsa ndithu imene Mulungu anayipereka kwa anthu!
ונתתי את לבי לדרוש ולתור בחכמה על כל אשר נעשה תחת השמים הוא ענין רע נתן אלהים לבני האדם--לענות בו
14 Ine ndaona zinthu zonse zochitika pansi pano; zinthu zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
ראיתי את כל המעשים שנעשו תחת השמש והנה הכל הבל ורעות רוח
15 Chinthu chokhota sichingathe kuwongoledwa; chimene palibe sichingathe kuwerengedwa.
מעות לא יוכל לתקן וחסרון לא יוכל להמנות
16 Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Taona, ine ndakula ndi kukhala wa nzeru zochuluka kupambana aliyense amene analamulirapo Yerusalemu ndisanabadwe; ndaphunzira nzeru zochuluka ndi luntha.”
דברתי אני עם לבי לאמר--אני הנה הגדלתי והוספתי חכמה על כל אשר היה לפני על ירושלם ולבי ראה הרבה חכמה ודעת
17 Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.
ואתנה לבי לדעת חכמה ודעת הוללת ושכלות ידעתי שגם זה הוא רעיון רוח
18 Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso: chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.
כי ברב חכמה רב כעס ויוסיף דעת יוסיף מכאוב

< Mlaliki 1 >