< Deuteronomo 9 >

1 Mvera Israeli. Watsala pangʼono kuwoloka Yorodani ndi kukathamangitsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iweyo, imene mizinda yake ndi ikuluikulu yokhala ndi makoma ofika mpaka kumwamba.
שמע ישראל אתה עבר היום את הירדן לבא לרשת גוים גדלים ועצמים ממך ערים גדלת ובצרת בשמים׃
2 Anthuwo ndi ataliatali, Aanaki! Ukudziwa za iwo ndipo unamvapo zikunenedwa kuti, “Ndani amene angalimbane ndi Aanaki?”
עם גדול ורם בני ענקים אשר אתה ידעת ואתה שמעת מי יתיצב לפני בני ענק׃
3 Koma khulupirira lero kuti Yehova Mulungu wako amene ali patsogolo pako ali ngati moto wonyeketsa. Adzawononga iwowo ndipo adzawagonjetsa iweyo ukuona. Pamenepo udzawathamangitsa ndi kuwakantha mwamsanga, monga momwe Yehova wakulonjezera.
וידעת היום כי יהוה אלהיך הוא העבר לפניך אש אכלה הוא ישמידם והוא יכניעם לפניך והורשתם והאבדתם מהר כאשר דבר יהוה לך׃
4 Yehova Mulungu wako akadzawapirikitsa pamaso pako, usadzanene mu mtima mwako kuti, “Yehova wandibweretsa kuno kudzalanda dziko lino chifukwa cha kulungama kwanga.” Ayi, koma ndi chifukwa cha kuyipa kwa anthu amene Yehova ati awapirikitse pamaso pako.
אל תאמר בלבבך בהדף יהוה אלהיך אתם מלפניך לאמר בצדקתי הביאני יהוה לרשת את הארץ הזאת וברשעת הגוים האלה יהוה מורישם מפניך׃
5 Sukalowa ndi kutenga dziko lawolo chifukwa cha kulungama kwako kapena kukhulupirika kwako koma chifukwa cha kuyipa kwa anthuwo. Yehova Mulungu wako awapirikitsa pamaso pako kuti akwaniritse zimene analumbira kwa makolo ako Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
לא בצדקתך ובישר לבבך אתה בא לרשת את ארצם כי ברשעת הגוים האלה יהוה אלהיך מורישם מפניך ולמען הקים את הדבר אשר נשבע יהוה לאבתיך לאברהם ליצחק וליעקב׃
6 Tsono zindikira kuti si chifukwa cha kulungama kwako kuti Yehova Mulungu wako akukupatsa dziko labwinoli kuti ulitenge popeza ndiwe wokanika.
וידעת כי לא בצדקתך יהוה אלהיך נתן לך את הארץ הטובה הזאת לרשתה כי עם קשה ערף אתה׃
7 Kumbukirani izi ndipo musayiwale mmene munaputira mkwiyo wa Yehova Mulungu mʼchipululu muja. Kuyambira tsiku limene munatuluka mu Igupto mpaka pamene munafika kuno, mwakhala owukira Yehova.
זכר אל תשכח את אשר הקצפת את יהוה אלהיך במדבר למן היום אשר יצאת מארץ מצרים עד באכם עד המקום הזה ממרים הייתם עם יהוה׃
8 Ku Horebu munaputa mkwiyo wa Yehova, kotero kuti anakwiya kwambiri nafuna kukuwonongani.
ובחרב הקצפתם את יהוה ויתאנף יהוה בכם להשמיד אתכם׃
9 Nditakwera ku phiri kuti ndikalandire miyala iwiri ya malamulo, ya pangano limene Yehova anachita ndi inu, ndinakhala ku phiriko kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana, sindinadye buledi kapena kumwa madzi.
בעלתי ההרה לקחת לוחת האבנים לוחת הברית אשר כרת יהוה עמכם ואשב בהר ארבעים יום וארבעים לילה לחם לא אכלתי ומים לא שתיתי׃
10 Yehova anandipatsa miyala iwiri yolembedwa ndi chala chake. Pa miyalapo panali malamulo onse amene Yehova analengeza kwa inu pa phiri kuchokera mʼmoto pa tsiku la msonkhano.
ויתן יהוה אלי את שני לוחת האבנים כתבים באצבע אלהים ועליהם ככל הדברים אשר דבר יהוה עמכם בהר מתוך האש ביום הקהל׃
11 Pakutha pa masiku makumi anayi usiku ndi usana, Yehova anandipatsa miyala iwiri, miyala ya pangano.
ויהי מקץ ארבעים יום וארבעים לילה נתן יהוה אלי את שני לחת האבנים לחות הברית׃
12 Tsono Yehova anandiwuza, “Tsikako kuno msanga, chifukwa anthu ako aja unawatulutsa ku Iguptowa adziyipitsa. Iwo apatukapo mofulumira pa zimene ndinawalamulira ndipo adzipangira fano lachitsulo.”
ויאמר יהוה אלי קום רד מהר מזה כי שחת עמך אשר הוצאת ממצרים סרו מהר מן הדרך אשר צויתם עשו להם מסכה׃
13 Ndipo Yehova anati kwa ine, “Anthu awa ndawaona ndipo ndi anthu okanikadi!
ויאמר יהוה אלי לאמר ראיתי את העם הזה והנה עם קשה ערף הוא׃
14 Ndilekeni ndiwawononge ndi kufafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi wochuluka kuposa iwo.”
הרף ממני ואשמידם ואמחה את שמם מתחת השמים ואעשה אותך לגוי עצום ורב ממנו׃
15 Choncho ndinatembenuka ndi kutsika phiri moto ukanayakabe. Ndipo miyala iwiri ya pangano inali mʼmanja mwanga.
ואפן וארד מן ההר וההר בער באש ושני לחת הברית על שתי ידי׃
16 Ine poyangʼana ndinaona kuti inu munachimwira Yehova Mulungu wanu. Munadzipangira fano lowumbidwa ngati mwana wangʼombe. Inuyo munapatuka msanga kuchoka pa njira imene Yehova anakulamulirani.
וארא והנה חטאתם ליהוה אלהיכם עשיתם לכם עגל מסכה סרתם מהר מן הדרך אשר צוה יהוה אתכם׃
17 Motero ine ndinaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwanga, ndi kuyiphwanya inu mukuona.
ואתפש בשני הלחת ואשלכם מעל שתי ידי ואשברם לעיניכם׃
18 Tsono nthawi yomweyo ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana. Sindinadye buledi kapena kumwa madzi chifukwa cha machimo onse amene munawachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kumukwiyitsa kwambiri.
ואתנפל לפני יהוה כראשנה ארבעים יום וארבעים לילה לחם לא אכלתי ומים לא שתיתי על כל חטאתכם אשר חטאתם לעשות הרע בעיני יהוה להכעיסו׃
19 Ine ndinachita mantha ndi mkwiyo ndi ukali wa Yehova chifukwa anakwiya nanu kokwanira kukuwonongani. Koma Yehova anandimveranso.
כי יגרתי מפני האף והחמה אשר קצף יהוה עליכם להשמיד אתכם וישמע יהוה אלי גם בפעם ההוא׃
20 Ndipo Yehova anakwiya ndi Aaroni ndipo akanamuwononga, koma ine ndinamupemphereranso Aaroniyo.
ובאהרן התאנף יהוה מאד להשמידו ואתפלל גם בעד אהרן בעת ההוא׃
21 Ndiponso ndinatenga chinthu chanu choyipacho, mwana wangʼombe amene munapangayo, ndi kumuwotcha pa moto. Kenaka ndinamuphwanya ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi ndipo ndinawaza fumbilo mu mtsinje umene unkayenda kuchokera mʼphiri.
ואת חטאתכם אשר עשיתם את העגל לקחתי ואשרף אתו באש ואכת אתו טחון היטב עד אשר דק לעפר ואשלך את עפרו אל הנחל הירד מן ההר׃
22 Inu munamukwiyitsanso Yehova ku Tabera, ku Masa ndi ku Kibiroti Hatava.
ובתבערה ובמסה ובקברת התאוה מקצפים הייתם את יהוה׃
23 Ndipo Yehova atakutulutsani ku Kadesi Barinea anati, “Pitani mukatenge dziko limene ndakupatsani.” Koma munawukira ulamuliro wa Yehova Mulungu wanu. Inu simunamukhulupirire kapena kumumvera.
ובשלח יהוה אתכם מקדש ברנע לאמר עלו ורשו את הארץ אשר נתתי לכם ותמרו את פי יהוה אלהיכם ולא האמנתם לו ולא שמעתם בקלו׃
24 Kuyambira pamene ndinakudziwani, mwakhala owukira Yehova.
ממרים הייתם עם יהוה מיום דעתי אתכם׃
25 Ine ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku chifukwa Yehova ananena kuti akuwonongani.
ואתנפל לפני יהוה את ארבעים היום ואת ארבעים הלילה אשר התנפלתי כי אמר יהוה להשמיד אתכם׃
26 Ndinapemphera kwa Ambuye ndi kuti, “Haa Yehova Wamkulukulu, musawawononge anthu anu, chuma chanuchanu chimene munachipulumutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ku Igupto ndi dzanja lanu la mphamvu.
ואתפלל אל יהוה ואמר אדני יהוה אל תשחת עמך ונחלתך אשר פדית בגדלך אשר הוצאת ממצרים ביד חזקה׃
27 Kumbukirani atumiki anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Musatengere kupulupudza, kuyipa ndi kuchimwa kwawo anthuwa.
זכר לעבדיך לאברהם ליצחק וליעקב אל תפן אל קשי העם הזה ואל רשעו ואל חטאתו׃
28 Kupanda kutero, ndiye kuti anthu a ku dziko lija munatitulutsaku adzati, ‘Yehova anawatulutsa kuti akawaphe mʼchipululu popeza sanathe kukawalowetsa mʼdziko limene anawalonjeza ndipo anadana nawo.’
פן יאמרו הארץ אשר הוצאתנו משם מבלי יכלת יהוה להביאם אל הארץ אשר דבר להם ומשנאתו אותם הוציאם להמתם במדבר׃
29 Koma iwowa ndi anthu anu, chuma chanu chimene munachitulutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ndi mkono wanu wotambasuka.”
והם עמך ונחלתך אשר הוצאת בכחך הגדל ובזרעך הנטויה׃

< Deuteronomo 9 >