< Deuteronomo 8 >

1 Samalani potsata lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero, kuti mukhale ndi moyo ndi kuchulukana kuti mulande ndi kulowa mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu.
כל המצוה אשר אנכי מצוך היום--תשמרון לעשות למען תחיון ורביתם ובאתם וירשתם את הארץ אשר נשבע יהוה לאבתיכם
2 Kumbukirani mmene Yehova Mulungu wanu anakutsogolerani njira yonse mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kukutsitsani ndi kukuyesani kuti adziwe chimene chinali mu mtima mwanu ngati mungathe kusunga malamulo ake kapena ayi.
וזכרת את כל הדרך אשר הוליכך יהוה אלהיך זה ארבעים שנה--במדבר למען ענתך לנסתך לדעת את אשר בלבבך התשמר מצותו--אם לא
3 Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.
ויענך וירעבך ויאכלך את המן אשר לא ידעת ולא ידעון אבתיך למען הודיעך כי לא על הלחם לבדו יחיה האדם--כי על כל מוצא פי יהוה יחיה האדם
4 Mʼzaka makumi anayi zimenezi, zovala zanu sizinangʼambike ndipo mapazi anu sanatupe.
שמלתך לא בלתה מעליך ורגלך לא בצקה--זה ארבעים שנה
5 Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani.
וידעת עם לבבך כי כאשר ייסר איש את בנו יהוה אלהיך מיסרך
6 Samalirani malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira yake ndi kumuopa Iye.
ושמרת את מצות יהוה אלהיך ללכת בדרכיו וליראה אתו
7 Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino, dziko lokhala ndi mitsinje ndi mathawale a madzi, akasupe oyenderera mu zigwa ndi mʼmapiri,
כי יהוה אלהיך מביאך אל ארץ טובה ארץ נחלי מים--עינת ותהמת יצאים בבקעה ובהר
8 dziko lokhala ndi tirigu ndi barele, mpesa ndi mitengo ya mkuyu, makangadza, mafuta a olivi ndi uchi;
ארץ חטה ושערה וגפן ותאנה ורמון ארץ זית שמן ודבש
9 dziko limene buledi sadzasowa ndipo simudzasowa chilichonse; dziko limene miyala yake ndi chitsulo ndipo ku mapiri ake mukhoza kukumbako mkuwa.
ארץ אשר לא במסכנת תאכל בה לחם--לא תחסר כל בה ארץ אשר אבניה ברזל ומהרריה תחצב נחשת
10 Mukadya ndi kukhuta, yamikani Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.
ואכלת ושבעת--וברכת את יהוה אלהיך על הארץ הטבה אשר נתן לך
11 Samalani kuopa kuti mungayiwale Yehova Mulungu wanu posasunga malamulo, zikhazikitso ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero,
השמר לך פן תשכח את יהוה אלהיך לבלתי שמר מצותיו ומשפטיו וחקתיו אשר אנכי מצוך היום
12 kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo,
פן תאכל ושבעת ובתים טבים תבנה וישבת
13 ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka,
ובקרך וצאנך ירבין וכסף וזהב ירבה לך וכל אשר לך ירבה
14 mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo.
ורם לבבך ושכחת את יהוה אלהיך המוציאך מארץ מצרים מבית עבדים
15 Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma.
המוליכך במדבר הגדל והנורא נחש שרף ועקרב וצמאון אשר אין מים המוציא לך מים מצור החלמיש
16 Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino.
המאכלך מן במדבר אשר לא ידעון אבתיך למען ענתך ולמען נסתך--להיטבך באחריתך
17 Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, “Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi.”
ואמרת בלבבך כחי ועצם ידי עשה לי את החיל הזה
18 Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.
וזכרת את יהוה אלהיך--כי הוא הנתן לך כח לעשות חיל למען הקים את בריתו אשר נשבע לאבתיך כיום הזה
19 Ine ndine mboni yokutsutsani lero lino, kuti mukayiwala Yehova Mulungu wanu ndi kutsata milungu ina nʼkumayigwadira, mudzawonongeka ndithu.
והיה אם שכח תשכח את יהוה אלהיך והלכת אחרי אלהים אחרים ועבדתם והשתחוית להם--העדתי בכם היום כי אבד תאבדון
20 Monga mitundu ina ya anthu imene Yehova anayiwononga pamaso panu, inunso mudzawonongedwa chifukwa chosamvera Yehova Mulungu wanu.
כגוים אשר יהוה מאביד מפניכם--כן תאבדון עקב לא תשמעון בקול יהוה אלהיכם

< Deuteronomo 8 >