< Deuteronomo 7 >
1 Pamene Yehova Mulungu wanu wakufikitsani mʼdziko limene mukukalowa ndi kulilanda ndi kuthamangitsa pamaso panu mitundu ya anthu iyi: Ahiti, Agirigasi, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi; yomwe ndi mitundu isanu ndi iwiri yayikulu ndi yamphamvu kuposa inu;
2 Yehova Mulungu wanu akadzawapereka mʼmanja mwanu, ndipo inu mukadzawagonjetsa, mudzawawononge kwathunthu. Musadzachite mgwirizano ndi anthuwo ndiponso musadzawachitire chifundo.
3 Musadzakwatirane nawo. Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna kapena kutenga ana anu aamuna ndi kuwapereka kwa ana awo aakazi.
4 Mukadzatero, iwo adzasocheretsa ana anu aamuna kuti asanditsatire ndi kutumikira milungu ina. Motero Yehova adzakukwiyirani ndi kukuwonongani mwachangu.
5 Koma mukachite izi: Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, mukadule mitengo yawo ya Asera, ndi kutentha mafano awo pa moto.
6 Pakuti inu ndinu anthu opatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani pakati pa anthu onse pa dziko lapansi kuti mukhale ake, chuma chake cha mtengo wapatali.
7 Yehova sanakukondeni chifukwa choti munali ochuluka kuposa ena pakuti inuyo ndiye munali ochepetsetsa mwa anthu onse.
8 Koma chifukwa chakuti Yehova anakukondani nasunga lumbiro lake limene analumbira kwa makolo anu. Ndi chifukwa chake anakutulutsani ndi mphamvu yake yopanda malire ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo, kuchoka mʼmanja mwa Farao mfumu ya ku Igupto.
9 Choncho dziwani kuti Yehova Mulungu wanu, ndi Mulungu. Iye ndi Mulungu wokhulupirika, wosunga pangano lake la chikondi chosasinthika ku mibadomibado, kwa iwo amene amamukonda nasunga malamulo ake.
10 Koma iwo amene amamuda adzawabwezera powawononga pamaso pawo; sadzachedwa kuwabwezera iwo amene amadana naye.
11 Choncho muziyesetsa kusunga malamulo, malangizo ndi maphunziro amene ndikukulamulani lero lino kuti muchite.
12 Mukamvera malamulo amenewa, ndi kusamala kuwatsata, ndiye kuti Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano lake la chikondi chosasinthika ndi inu, monga analumbira kwa makolo anu.
13 Iye adzakukondani nakudalitsani ndi kukuchulukitsani. Adzadalitsa chipatso cha mʼmimba mwanu, zokolola za mʼdziko mwanu, tirigu wanu, vinyo wanu ndi mafuta anu, ana angʼombe zanu ndi ana ankhosa zanu mʼdziko limene analumbirira kwa makolo anu kuti akupatseni inu.
14 Inu mudzadalitsika kuposa mtundu wina uliwonse wa anthu ndipo palibe mwamuna kapena mkazi aliyense pakati panu amene adzakhale wosabereka. Ziweto zanu nazonso, sipadzapezeka zosabereka.
15 Yehova adzakupewetsani ku matenda aliwonse. Sadzakugwetserani matenda owopsa aja munawadziwa ku Igupto, koma adzawagwetsera pa odana nanu.
16 Muwononge anthu onse amene Yehova Mulungu wanu awapereka kwa inu. Musawamvere chisoni ndipo musatumikire milungu yawo pakuti umenewo udzakhala msampha kwa inu.
17 Mukhoza kunena kuti, “Anthu awa ndi amphamvu kuposa ifeyo. Nanga tingawapirikitse bwanji?”
18 Koma musachite nawo mantha, kumbukirani bwino zimene Yehova Mulungu wanu anachita ndi Farao pamodzi ndi Igupto yense.
19 Munadzionera nokha ndi maso anu mayesero aakulu, zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, mphamvu yake yopanda malire imene Yehova Mulungu wanu anakutulutsirani. Yehova Mulungu adzachita zimenezo ndi anthu onse amene muwaopa tsopano.
20 Kuwonjezera apo, Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pawo mpaka atamaliza onse amene adzakubisalirani.
21 Musaopsedwe nawo pakuti Yehova Mulungu wanu, amene ali pakati panu, ndi Mulungu wamkulu ndi woopsa.
22 Yehova Mulungu wanu adzapirikitsa anthu a mitundu yonse pamaso panu, pangʼonopangʼono. Sadzakulolani kuti muwathe nthawi imodzi, kuti nyama zakuthengo zingadzaswane mokuzungulirani.
23 Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu, adzawasokoneza kufikira atawonongedwa.
24 Iye adzapereka mafumu awo mʼdzanja lanu, ndipo adzafafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Palibe amene adzalimbana nanu, inu mudzawawononga.
25 Muwawotche pa moto mafano a milungu yawo. Musasirire siliva ndi golide amene ali pa mafanoyo. Musamutenge kuti akhale wanu chifukwa mukatero mudzakodwa naye ngati msampha, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa nazo.
26 Musabweretse chinthu chonyansa mʼnyumba mwanu kuopa kuwonongedwa ngati chonyasacho. Muziyipidwa ndi kunyansidwa nacho kwambiri pakuti chidzawonongedwanso.