< Deuteronomo 6 >

1 Awa ndi malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene Yehova Mulungu wanu anandilamula kuti ndikuphunzitseni kuti mukawatsatire mʼdziko limene mukuwolokera Yorodani kuti mukalitenge,
וזאת המצוה החקים והמשפטים אשר צוה יהוה אלהיכם ללמד אתכם--לעשות בארץ אשר אתם עברים שמה לרשתה
2 kuti inuyo, ana anu, ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo mudzaope Yehova Mulungu wanu moyo wanu wonse posunga malangizo ndi malamulo ake onse amene ndinakupatsani inu kuti musangalale ndi moyo wautali.
למען תירא את יהוה אלהיך לשמר את כל חקתיו ומצותיו אשר אנכי מצוך אתה ובנך ובן בנך כל ימי חייך--ולמען יארכן ימיך
3 Mvera Israeli ndipo usamalitse kuchita malamulowa kuti zinthu zikuyendere bwino mʼdziko ndi kuti muchuluke kwambiri mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.
ושמעת ישראל ושמרת לעשות אשר ייטב לך ואשר תרבון מאד כאשר דבר יהוה אלהי אבתיך לך--ארץ זבת חלב ודבש
4 Tamvani inu Aisraeli, Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi.
שמע ישראל יהוה אלהינו יהוה אחד
5 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.
ואהבת את יהוה אלהיך בכל לבבך ובכל נפשך ובכל מאדך
6 Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu.
והיו הדברים האלה אשר אנכי מצוך היום--על לבבך
7 Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.
ושננתם לבניך ודברת בם בשבתך בביתך ובלכתך בדרך ובשכבך ובקומך
8 Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu.
וקשרתם לאות על ידך והיו לטטפת בין עיניך
9 Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.
וכתבתם על מזזות ביתך ובשעריך
10 Pamene Yehova Mulungu wanu akukulowetsani ndi kukupatsani dziko limene analumbirira makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo, dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu imene inu simunamange,
והיה כי יביאך יהוה אלהיך אל הארץ אשר נשבע לאבתיך לאברהם ליצחק וליעקב--לתת לך ערים גדלת וטבת אשר לא בנית
11 nyumba zodzaza ndi zinthu za mitundu yonse zimene inu simunayikemo, zitsime zimene inu simunakumbe, minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi zimene inuyo simunadzale, tsono mukadya ndi kukhuta,
ובתים מלאים כל טוב אשר לא מלאת וברת חצובים אשר לא חצבת כרמים וזיתים אשר לא נטעת ואכלת ושבעת
12 samalani kuti mungayiwale Yehova amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani mu ukapolo.
השמר לך פן תשכח את יהוה אשר הוציאך מארץ מצרים מבית עבדים
13 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye yekha, ndipo muzilumbira pa dzina lake.
את יהוה אלהיך תירא ואתו תעבד ובשמו תשבע
14 Musamatsatire milungu ina, milungu ya anthu ena okuzungulirani,
לא תלכון אחרי אלהים אחרים--מאלהי העמים אשר סביבותיכם
15 pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu, ndi Mulungu wansanje ndipo adzakukwiyirani kwambiri ndi kukuwonongani, kukufafanizani mʼdziko.
כי אל קנא יהוה אלהיך בקרבך פן יחרה אף יהוה אלהיך בך והשמידך מעל פני האדמה
16 Musamuyese Yehova Mulungu wanu monga munachitira ku Masa.
לא תנסו את יהוה אלהיכם כאשר נסיתם במסה
17 Onetsetsani kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, malangizo ake ndi zikhazikitso zake zimene anakulamulirani.
שמור תשמרון את מצות יהוה אלהיכם ועדתיו וחקיו אשר צוך
18 Chitani zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova, kuti zikuyendereni bwino ndi kuti mukhoza kukalowa ndi kulanda dziko labwinolo limene Yehova analonjeza molumbira kwa makolo anu,
ועשית הישר והטוב בעיני יהוה--למען ייטב לך ובאת וירשת את הארץ הטבה אשר נשבע יהוה לאבתיך
19 kupirikitsiratu adani anu onse, monga Yehova wanenera.
להדף את כל איביך מפניך כאשר דבר יהוה
20 Mʼtsogolo muno, ana anu akadzakufunsani kuti, “Kodi tanthauzo la ndondomeko, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo amene Yehova Mulungu wathu anakulamulani nʼchiyani?”
כי ישאלך בנך מחר לאמר מה העדת והחקים והמשפטים אשר צוה יהוה אלהינו אתכם
21 Inu mudzawawuze kuti, “Ife tinali akapolo a Farao ku Igupto, koma Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lamphamvu.
ואמרת לבנך עבדים היינו לפרעה במצרים ויציאנו יהוה ממצרים ביד חזקה
22 Ifeyo tikuona Yehova anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, zazikulu ndi zoopsa, pa Aigupto ndi Farao pamodzi ndi banja lake lonse.
ויתן יהוה אותת ומפתים גדלים ורעים במצרים בפרעה ובכל ביתו--לעינינו
23 Koma anatitulutsa kumeneko ndi kutilowetsa kuno natipatsa dziko limene analonjeza mwa lumbiro kwa makolo athu.
ואותנו הוציא משם--למען הביא אתנו לתת לנו את הארץ אשר נשבע לאבתינו
24 Yehova anatilamula kuti tizimvera malamulo onsewa, kuti tizimuopa kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu monga momwe zilili leromu.
ויצונו יהוה לעשות את כל החקים האלה ליראה את יהוה אלהינו--לטוב לנו כל הימים לחיתנו כהיום הזה
25 Ndipo ngati tisamala kumvera malamulo onsewa pamaso pa Yehova Mulungu wathu monga momwe anatilamulira ife, chimenecho chidzakhala chilungamo chathu.”
וצדקה תהיה לנו כי נשמר לעשות את כל המצוה הזאת לפני יהוה אלהינו--כאשר צונו

< Deuteronomo 6 >