< Deuteronomo 4 >

1 Mverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuphunzitseni. Muwatsatire kuti mukhale ndi moyo ndi kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani.
ועתה ישראל שמע אל החקים ואל המשפטים אשר אנכי מלמד אתכם לעשות--למען תחיו ובאתם וירשתם את הארץ אשר יהוה אלהי אבתיכם נתן לכם
2 Musawonjezere pa zimene ndikukulamulirani ndipo musachotserepo, koma muwasunge malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.
לא תספו על הדבר אשר אנכי מצוה אתכם ולא תגרעו ממנו--לשמר את מצות יהוה אלהיכם אשר אנכי מצוה אתכם
3 Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita ku Baala-Peori. Yehova Mulungu wanu anawononga aliyense amene anatsata Baala wa ku Peori pakati panu.
עיניכם הראות את אשר עשה יהוה בבעל פעור כי כל האיש אשר הלך אחרי בעל פעור--השמידו יהוה אלהיך מקרבך
4 Koma inu nonse amene munagwiritsitsa Yehova Mulungu wanu mukanali ndi moyo mpaka lero.
ואתם הדבקים ביהוה אלהיכם--חיים כלכם היום
5 Taonani, ndakuphunzitsani malangizo ndi malamulo monga Yehova Mulungu wanga anandilamulira kuti inuyo muwatsatire mʼdziko limene mukulowa ndi kulitengali.
ראה למדתי אתכם חקים ומשפטים כאשר צוני יהוה אלהי לעשות כן--בקרב הארץ אשר אתם באים שמה לרשתה
6 Muwasunge mosamalitsa pakuti zimenezi zidzaonetsa nzeru zanu ndi kuzindikira kwanu kwa anthu a mitundu ina, amene adzamva za malangizo onsewa nati, “Ndithudi, mtundu waukulu uwu ndi wa anthu anzeru ndi ozindikira.”
ושמרתם ועשיתם--כי הוא חכמתכם ובינתכם לעיני העמים אשר ישמעון את כל החקים האלה ואמרו רק עם חכם ונבון הגוי הגדול הזה
7 Mtundu wina wa anthu ndi uti umene uli waukulu chomwechi, woti ukhoza kukhala ndi milungu yawo pafupi monga mmene alili Yehova Mulungu wathu ndi ife nthawi zonse pamene tipemphera kwa Iye?
כי מי גוי גדול אשר לו אלהים קרבים אליו כיהוה אלהינו בכל קראנו אליו
8 Ndipo ndi mtundu uti mwa mitundu ya anthu umene ndi waukulu chotere kuti nʼkukhala ndi malangizo ndi malamulo olungama ngati malamulo amene ndikuyika pamaso panu lero?
ומי גוי גדול אשר לו חקים ומשפטים צדיקם ככל התורה הזאת אשר אנכי נתן לפניכם היום
9 Inu mungosamala ndi kudziyangʼanira kwambiri nokha kuti musayiwale zimene maso anu aona. Musalole kuti zichoke mʼmitima mwanu pa moyo wanu wonse. Zimenezi muziphunzitse kwa ana anu ndi zidzukulu zanu ngakhale mʼtsogolo.
רק השמר לך ושמר נפשך מאד פן תשכח את הדברים אשר ראו עיניך ופן יסורו מלבבך כל ימי חייך והודעתם לבניך ולבני בניך
10 Kumbukirani tsiku limene munayimirira pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebu, pamene anati kwa ine, “Sonkhanitsa anthu pamaso panga kuti amve mawu anga ndi kuti aphunzire kundilemekeza mʼmoyo wawo onse mʼdzikomo ndi kuti ana awo aziwaphunzitsa zimenezi.”
יום אשר עמדת לפני יהוה אלהיך בחרב באמר יהוה אלי הקהל לי את העם ואשמעם את דברי אשר ילמדון ליראה אתי כל הימים אשר הם חיים על האדמה ואת בניהם ילמדון
11 Munabwera pafupi ndi kuyima pa tsinde pa phiri pamene phirilo limayaka moto umene umafika mpaka kumwamba. Panalinso mtambo wakuda ndi mdima wambiri.
ותקרבון ותעמדון תחת ההר וההר בער באש עד לב השמים--חשך ענן וערפל
12 Kenaka Yehova anayankhula nanu kuchokera mʼmotowo. Inu munamva mawu ake okha koma simunamuone pakuti panali mawu chabe.
וידבר יהוה אליכם מתוך האש קול דברים אתם שמעים ותמונה אינכם ראים זולתי קול
13 Iye anakuwuzani Malamulo Khumi omwe ndi pangano lake limene anakulamulirani kuti mutsatire. Ndipo anawalemba malamulowo pa mapale awiri a miyala.
ויגד לכם את בריתו אשר צוה אתכם לעשות--עשרת הדברים ויכתבם על שני לחות אבנים
14 Ndipo Yehova anandilamula nthawi imene ija kuti ndikuphunzitseni malangizo ndi malamulo amene muyenera kutsata mʼdziko limene mutenge mukawoloka Yorodani.
ואתי צוה יהוה בעת ההוא ללמד אתכם חקים ומשפטים לעשתכם אתם--בארץ אשר אתם עברים שמה לרשתה
15 Tsiku limene Yehova anayankhula nanu ku Horebu mʼmoto uja, simunaone thupi lake. Choncho mudziyangʼanire nokha mosamalitsa,
ונשמרתם מאד לנפשתיכם כי לא ראיתם כל תמונה ביום דבר יהוה אליכם בחרב מתוך האש
16 kuti musasokonezeke ndi kudzipangira nokha fano kapena chifanizo cha mtundu uliwonse, kaya chokhala ngati mwamuna kapena ngati mkazi,
פן תשחתון--ועשיתם לכם פסל תמונת כל סמל תבנית זכר או נקבה
17 kaya chokhala ngati nyama iliyonse ya pa dziko lapansi kapena mbalame iliyonse yowuluka mlengalenga.
תבנית כל בהמה אשר בארץ תבנית כל צפור כנף אשר תעוף בשמים
18 Kapena cholengedwa chilichonse choyenda pa nthaka kapena nsomba ya mʼmadzi akuya.
תבנית כל רמש באדמה תבנית כל דגה אשר במים מתחת לארץ
19 Ndipo pamene muyangʼana kumwamba muona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, zonse zakumwambazo musakopeke kuti muzigwadire ndi kumapembedza zinthu zimene Yehova wapereka kwa anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi.
ופן תשא עיניך השמימה וראית את השמש ואת הירח ואת הכוכבים כל צבא השמים ונדחת והשתחוית להם ועבדתם--אשר חלק יהוה אלהיך אתם לכל העמים תחת כל השמים
20 Koma inuyo, Yehova anakutengani ndi kukutulutsani mʼngʼanjo yosungunulira zitsulo, ku Igupto kuti mukhale anthu olandira chuma chake monga mmene mulili tsopano.
ואתכם לקח יהוה ויוצא אתכם מכור הברזל ממצרים להיות לו לעם נחלה כיום הזה
21 Yehova anakwiya nane chifukwa cha inu, ndipo analumbira kwathunthu kuti sindidzawoloka Yorodani ndi kulowa mʼdziko labwinolo limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani inu ngati cholowa chanu.
ויהוה התאנף בי על דבריכם וישבע לבלתי עברי את הירדן ולבלתי בא אל הארץ הטובה אשר יהוה אלהיך נתן לך נחלה
22 Ine ndifera mʼdziko lino, sindiwoloka Yorodani. Koma inu mwatsala pangʼono kuwoloka ndi kukatenga dziko labwinolo.
כי אנכי מת בארץ הזאת אינני עבר את הירדן ואתם עברים וירשתם את הארץ הטובה הזאת
23 Samalani, musayiwale pangano limene Yehova Mulungu wanu anapangana nanu ndipo musadzipangire nokha fano la chinthu chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu waletsa.
השמרו לכם פן תשכחו את ברית יהוה אלהיכם אשר כרת עמכם ועשיתם לכם פסל תמונת כל אשר צוך יהוה אלהיך
24 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wonyeketsa ndipo ndi Mulungu wansanje.
כי יהוה אלהיך אש אכלה הוא אל קנא
25 Mukadzakhala nthawi yayitali mʼdzikomo ndi kubereka ana ndi kukhala ndi zidzukulu ndipo mukadzasokonekera ndi kupanga fano la mtundu uliwonse, nʼkumachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kumukwiyitsa,
כי תוליד בנים ובני בנים ונושנתם בארץ והשחתם ועשיתם פסל תמונת כל ועשיתם הרע בעיני יהוה אלהיך להכעיסו
26 ine ndi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni lero zokutsutsani kuti mudzawonongedwa msanga ndipo mudzachotsedwa mʼdziko limene mutenge mukawoloka Yorodani. Simudzakhalitsa kumeneko koma mudzawonongedwa ndithu.
העידתי בכם היום את השמים ואת הארץ כי אבד תאבדון מהר מעל הארץ אשר אתם עברים את הירדן שמה לרשתה לא תאריכן ימים עליה כי השמד תשמדון
27 Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu ena. Ochepa okha pakati panu ndi amene adzapulumuke pakati pa anthu a mitundu ina kumene Yehova adzakupirikitsireniko.
והפיץ יהוה אתכם בעמים ונשארתם מתי מספר בגוים אשר ינהג יהוה אתכם שמה
28 Kumeneko mudzapembedza milungu ya mitengo ndi miyala yopangidwa ndi anthu, imene singaone kapena kumva kapena kudya kapena kununkhiza.
ועבדתם שם אלהים מעשה ידי אדם עץ ואבן--אשר לא יראון ולא ישמעון ולא יאכלון ולא יריחן
29 Mukanali komweko, ngati mudzamufunafuna Yehova Mulungu wanu mudzamupeza koma ngati mutamufunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
ובקשתם משם את יהוה אלהיך ומצאת כי תדרשנו בכל לבבך ובכל נפשך
30 Mukadzakhala pa chipsinjo ndipo zonsezi zikadzakuchitikirani, ndi pamene pambuyo pake mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera Iye.
בצר לך--ומצאוך כל הדברים האלה באחרית הימים ושבת עד יהוה אלהיך ושמעת בקלו
31 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo, Iye sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuyiwala pangano lake ndi makolo anu, limene analitsimikiza mwa lumbiro.
כי אל רחום יהוה אלהיך לא ירפך ולא ישחיתך ולא ישכח את ברית אבתיך אשר נשבע להם
32 Tsopano tafunsani za masiku a mʼmbuyomu, zakale inu musanabadwe, kuyambira tsiku limene Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani kuyambira kumapeto mpaka mapeto anzake a thambo. Kodi chinachitikako china chachikulu ngati ichi, kapena chinayamba chamvekako chokhala ngati ichi?
כי שאל נא לימים ראשנים אשר היו לפניך למן היום אשר ברא אלהים אדם על הארץ ולמקצה השמים ועד קצה השמים הנהיה כדבר הגדול הזה או הנשמע כמהו
33 Kodi uliponso mtundu wina wa anthu umene unamva mawu a Mulungu akuyankhula kuchokera mʼmoto nʼkukhala ndi moyo monga mwachitira inumu?
השמע עם קול אלהים מדבר מתוך האש כאשר שמעת אתה--ויחי
34 Kodi alipo mulungu amene anayeserapo kudzitengera mtundu wa anthu kuwachotsa mu mtundu unzake mwa mayesero, zizindikiro zozizwitsa, nkhondo, komanso mwa mphamvu zake zopanda malire, kapena mwa zochita zazikulu ndi zochititsa mantha, monga zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Igupto inu mukupenya?
או הנסה אלהים לבוא לקחת לו גוי מקרב גוי במסת באתת ובמופתים ובמלחמה וביד חזקה ובזרוע נטויה ובמוראים גדלים ככל אשר עשה לכם יהוה אלהיכם במצרים--לעיניך
35 Iye anakuonetsani zonsezi kuti inu muzindikire kuti Yehova ndiye Mulungu, palibenso wina wofanana naye.
אתה הראת לדעת כי יהוה הוא האלהים אין עוד מלבדו
36 Kuchokera kumwamba, Iye anafuna kuti inu mumve mawu ake ndi kuti mukhale osunga mwambo. Pa dziko lapansi anakuonetsani moto waukulu, ndipo inu munamva mawu ake kuchokera mʼmotomo.
מן השמים השמיעך את קלו ליסרך ועל הארץ הראך את אשו הגדולה ודבריו שמעת מתוך האש
37 Popeza anakonda makolo anu ndi kusankha adzukulu awo, a pambuyo pawo, anakutulutsani kuchoka ku Igupto ali pakati panu ndi mphamvu yake,
ותחת כי אהב את אבתיך ויבחר בזרעו אחריו ויוצאך בפניו בכחו הגדל ממצרים
38 kuti akupirikitsireni mayiko akuluakulu ndi amphamvu kuposa inu, ndi kukubweretsani inu ku dziko lawo kuti likhale lanu, monga liliri lero.
להוריש גוים גדלים ועצמים ממך--מפניך להביאך לתת לך את ארצם נחלה--כיום הזה
39 Vomerezani lero ndipo dziwani mu mtima mwanu kuti Yehova ndiye Mulungu kumwamba ndi pa dziko lapansi. Palibenso wina.
וידעת היום והשבת אל לבבך כי יהוה הוא האלהים בשמים ממעל ועל הארץ מתחת אין עוד
40 Sungani malangizo ake ndi malamulo ake amene ndikukupatsani lero lino, kuti zikuyendereni bwino inu ndi ana anu kutsogoloko, ndi kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kwa nthawi zonse.
ושמרת את חקיו ואת מצותיו אשר אנכי מצוך היום אשר ייטב לך ולבניך אחריך--ולמען תאריך ימים על האדמה אשר יהוה אלהיך נתן לך כל הימים
41 Kenaka Mose anapatula mizinda itatu cha kummawa kwa Yorodani,
אז יבדיל משה שלש ערים בעבר הירדן מזרחה שמש
42 kumene aliyense amene wapha munthu akhoza kuthawirako ngati wopha munthuyo sanaphe mnzakeyo mwadala ndi maganizo oyipa. Iye akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi napulumutsa moyo wake.
לנס שמה רוצח אשר ירצח את רעהו בבלי דעת והוא לא שנא לו מתמל שלשם ונס אל אחת מן הערים האל--וחי
43 Mizindayo inali iyi: ku fuko la Rubeni, unali mzinda wa Bezeri ku mapiri a ku chipululu; ku fuko la Gadi, unali Ramoti ku Giliyadi; ndipo ku fuko la Manase, unali Golani ku Basani.
את בצר במדבר בארץ המישר לראובני ואת ראמת בגלעד לגדי ואת גולן בבשן למנשי
44 Awa ndi malamulo amene Mose anapereka kwa Aisraeli.
וזאת התורה אשר שם משה לפני בני ישראל
45 Izi ndi ndondomeko, malangizo ndi malamulo amene Mose anawapatsa iwo pamene anatuluka ku Igupto.
אלה העדת והחקים והמשפטים--אשר דבר משה אל בני ישראל בצאתם ממצרים
46 Anali ku chigwa cha kufupi ndi Beti-Peori mbali ya kummawa kwa Yorodani, mʼdziko la Sihoni mfumu ya Aamori amene ankalamulira ku Hesiboni ndipo anagonjetsedwa ndi Mose ndi Aisraeli pamene ankachokera ku Igupto.
בעבר הירדן בגיא מול בית פעור בארץ סיחן מלך האמרי אשר יושב בחשבון--אשר הכה משה ובני ישראל בצאתם ממצרים
47 Iye anamulanda dziko lake ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani. Awa anali mafumu awiri Aamori a kummawa kwa Yorodani.
ויירשו את ארצו ואת ארץ עוג מלך הבשן שני מלכי האמרי אשר בעבר הירדן--מזרח שמש
48 Dziko ili linayambira ku Aroeri cha kumphepete kwa khwawa la Arinoni ku phiri la Siyoni (limeneli ndi phiri la Herimoni),
מערער אשר על שפת נחל ארנן ועד הר שיאן--הוא חרמון
49 ndi kuphatikizapo dziko lonse la Araba cha kummawa kwa Yorodani mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, kumunsi kwa Phiri la Pisiga.
וכל הערבה עבר הירדן מזרחה ועד ים הערבה--תחת אשדת הפסגה

< Deuteronomo 4 >