< Deuteronomo 33 >

1 Awa ndi madalitso amene Mose, munthu wa Mulungu, anawapereka kwa Aisraeli asanafe.
This is the blessing with which Moses the man of God blessed the children of Israel before his death.
2 Iye anati: “Yehova anabwera kuchokera ku Sinai ndipo anatulukira kuchokera ku Seiri; anawala kuchokera pa Phiri la Parani. Iye anabwera ndi chiwunyinji cha angelo kuchokera kummwera, moto woyaka uli mʼdzanja mwake.
He said, “The LORD came from Sinai, and rose from Seir to them. He shone from Mount Paran. He came from the ten thousands of holy ones. At his right hand was a fiery law for them.
3 Ndithu ndinu amene mumakonda anthu anu; opatulika ake onse ali mʼmanja mwake. Onse amagwada pansi pa mapazi anu kuchokera kwa inu amalandira malangizo,
Yes, he loves the people. All his saints are in your hand. They sat down at your feet. Each receives your words.
4 malamulo amene Mose anatipatsa, chuma chopambana cha mtundu wa Yakobo.
Moses commanded us a law, an inheritance for the assembly of Jacob.
5 Iye anali mfumu ya Yesuruni pamene atsogoleri a anthu anasonkhana, pamodzi ndi mafuko a Israeli.
He was king in Jeshurun, when the heads of the people were gathered, all the tribes of Israel together.
6 “Lolani Rubeni akhale ndi moyo ndipo asafe, anthu ake asachepe pa chiwerengero.”
“Let Reuben live, and not die; Nor let his men be few.”
7 Ndipo ponena za Yuda anati: “Inu Yehova, imvani kulira kwa Yuda; mubweretseni kwa anthu ake. Ndi manja ake omwe adziteteze yekha. Inu khalani thandizo lake polimbana ndi adani ake!”
This is for Judah. He said, “Hear, LORD, the voice of Judah. Bring him in to his people. With his hands he contended for himself. You shall be a help against his adversaries.”
8 Za fuko la Alevi anati: “Tumimu wanu ndi Urimu ndi za mtumiki wanu wokhulupirika. Munamuyesa ku Masa; munalimbana naye ku madzi a ku Meriba.
About Levi he said, “Your Thummim and your Urim are with your godly one, whom you proved at Massah, with whom you contended at the waters of Meribah.
9 Iye ananena za abambo ake ndi amayi ake kuti, ‘Sindilabadira za iwo.’ Sanasamale za abale ake kapena ana ake, koma anayangʼanira mawu anu ndipo anateteza pangano lanu.
He said of his father, and of his mother, ‘I have not seen him.’ He didn’t acknowledge his brothers, nor did he know his own children; for they have observed your word, and keep your covenant.
10 Iye amaphunzitsa Yakobo malangizo anu ndi malamulo anu kwa Israeli. Amafukiza lubani pamaso panu ndiponso amapereka nsembe zanu zonse zopsereza pa guwa lanu.
They shall teach Jacob your ordinances, and Israel your law. They shall put incense before you, and whole burnt offering on your altar.
11 Inu Yehova, dalitsani luso lake lonse ndipo mukondwere ndi ntchito za manja ake. Menyani adani awo mʼchiwuno kanthani amene amuwukira kuti asadzukenso.”
LORD, bless his skills. Accept the work of his hands. Strike through the hips of those who rise up against him, of those who hate him, that they not rise again.”
12 Za fuko la Benjamini anati: “Wokondedwa wa Yehova akhale mwamtendere mwa Iye, pakuti amamuteteza tsiku lonse, ndipo amene Yehova amamukonda amawusa pa mapewa ake.”
About Benjamin he said, “The beloved of the LORD will dwell in safety by him. He covers him all day long. He dwells between his shoulders.”
13 Za fuko la Yosefe anati: “Yehova adalitse dziko lake ndi mame ambiri ochokera kumwamba ndiponso madzi ambiri ochokera pansi pa nthaka;
About Joseph he said, “His land is blessed by the LORD, for the precious things of the heavens, for the dew, for the deep that couches beneath,
14 ndi zinthu zambiri zimene zimacha ndi dzuwa ndiponso ndi zokolola zabwino kwambiri zimene zimacha ndi mwezi uliwonse;
for the precious things of the fruits of the sun, for the precious things that the moon can yield,
15 ndi zipatso zabwino kwambiri zochokera mʼmapiri amakedzanawa ndiponso zokolola zochuluka zochokera ku zitunda zakalekale;
for the best things of the ancient mountains, for the precious things of the everlasting hills,
16 ndi mphatso zabwino kwambiri zochokera pa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndiponso kukoma mtima kwa Iye amene amakhala mʼchitsamba choyaka moto. Madalitso onsewa akhale pa mutu pa Yosefe, wapaderadera pakati pa abale ake.
for the precious things of the earth and its fullness, the good will of him who lived in the bush. Let this come on the head of Joseph, on the crown of the head of him who was separated from his brothers.
17 Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa; nyanga zake zili ngati za njati. Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina, ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi. Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu; nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”
Majesty belongs to the firstborn of his herd. His horns are the horns of the wild ox. With them he will push all the peoples to the ends of the earth. They are the ten thousands of Ephraim. They are the thousands of Manasseh.”
18 Za fuko la Zebuloni anati: “Kondwera Zebuloni, pamene ukutuluka, ndipo iwe, Isakara, kondwera mʼmatenti ako.
About Zebulun he said, “Rejoice, Zebulun, in your going out; and Issachar, in your tents.
19 Adzayitanira mitundu ya anthu kumapiri, kumeneko adzaperekako nsembe zachilungamo; kumeneko adzadyerera zinthu zochuluka zochokera ku nyanja, chuma chobisika mu mchenga.”
They will call the peoples to the mountain. There they will offer sacrifices of righteousness, for they will draw out the abundance of the seas, the hidden treasures of the sand.”
20 Za fuko la Gadi anati: “Wodala amene amakulitsa malire a Gadi! Gadi amakhala kumeneko ngati mkango, kukhadzula mkono kapena mutu.
About Gad he said, “He who enlarges Gad is blessed. He dwells as a lioness, and tears the arm and the crown of the head.
21 Iye anadzisankhira dziko labwino kwambiri; gawo la mtsogoleri anasungira iye. Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana, anachita chifuniro cha Yehova molungama, ndiponso malamulo onena za Israeli.”
He provided the first part for himself, for the lawgiver’s portion was reserved for him. He came with the heads of the people. He executed the righteousness of the LORD, His ordinances with Israel.”
22 Za fuko la Dani anati: “Dani ndi mwana wamkango, amene akutuluka ku Basani.”
About Dan he said, “Dan is a lion’s cub that leaps out of Bashan.”
23 Za fuko la Nafutali anati: “Nafutali wadzaza ndi kukoma mtima kwa Yehova ndipo ndi wodzaza ndi madalitso ake; cholowa chake chidzakhala mbali ya kummwera kwa nyanja.”
About Naphtali he said, “Naphtali, satisfied with favor, full of the LORD’s blessing, Possess the west and the south.”
24 Za fuko la Aseri anati: “Mwana wodalitsika kwambiri ndi Aseri; abale ake amukomere mtima, ndipo asambe mapazi ake mʼmafuta.
About Asher he said, “Asher is blessed with children. Let him be acceptable to his brothers. Let him dip his foot in oil.
25 Zotsekera za zipata zako zidzakhala za chitsulo ndi za mkuwa, ndi mphamvu zako zidzakhala ngati masiku a moyo wako.
Your bars will be iron and bronze. As your days, so your strength will be.
26 “Palibe wina wofanana ndi Mulungu wa Yesuruni, amene amakwera pa thambo kukuthandizani ndiponso pa mitambo ya ulemerero wake.
“There is no one like God, Jeshurun, who rides on the heavens for your help, in his excellency on the skies.
27 Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu, ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu, adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’
The eternal God is your dwelling place. Underneath are the everlasting arms. He thrust out the enemy from before you, and said, ‘Destroy!’
28 Motero Israeli adzakhala yekha mwamtendere; zidzukulu za Yakobo zili pa mtendere mʼdziko la tirigu ndi vinyo watsopano, kumene thambo limagwetsa mame.
Israel dwells in safety, the fountain of Jacob alone, In a land of grain and new wine. Yes, his heavens drop down dew.
29 Iwe Israeli, ndiwe wodala! Wofanana nanu ndani anthu opulumutsidwa ndi Yehova? Iye ndiye chishango ndi mthandizi wanu ndi lupanga lanu la ulemerero. Adani ako adzakugonjera, ndipo iwe udzapondereza pansi malo awo achipembedzo.”
You are happy, Israel! Who is like you, a people saved by the LORD, the shield of your help, the sword of your excellency? Your enemies will submit themselves to you. You will tread on their high places.”

< Deuteronomo 33 >