< Deuteronomo 32 >
1 Mverani, inu mayiko a mmwamba ndipo ine ndidzayankhula; imva, iwe dziko lapansi, mawu a pakamwa panga.
2 Chiphunzitso changa chigwe ngati mvula ndipo mawu anga atsike ngati mame, ngati mvumbi pa udzu watsopano, ngati mvula yochuluka pa zomera zanthete.
3 Ndidzalalikira dzina la Yehova. Aa, tamandani ukulu wa Mulungu wathu!
4 Iye ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika amene salakwitsa, Iye ndiye wolungama ndi wosalakwa.
5 Koma iwo achita mosakhulupirika pamaso pake, iwo si ana akenso, koma iwo ndi mʼbado wachinyengo ndi wokhotakhota.
6 Kodi mukumubwezera Yehova chotere, inu anthu opusa ndi opanda nzeru? Kodi Iye si Atate anu, Mlengi wanu, amene anakupangani ndi kukuwumbani?
7 Kumbukirani masiku amakedzana; ganizirani za mibado yakalekale. Funsa abambo ako ndipo adzakuwuza, akuluakulu ako, ndipo adzakufotokozera.
8 Pamene Wammwambamwamba anapereka mayiko kwa anthu a mitundu ina kukhala cholowa chawo, pamene analekanitsa anthu onse, anayikira malire anthu onse molingana ndi chiwerengero cha ana a Israeli.
9 Pakuti gawo la Yehova ndi anthu ake, Yakobo ndiye cholowa chake.
10 Anamupeza mʼchipululu, ku malo owuma ndi kopanda kanthu. Anamuteteza ndi kumusamalira; anamutchinjiriza ngati mwanadiso wake,
11 ngati chiwombankhanga chimene chimasasula chisa chake nʼkumazungulira pamwamba pa ana ake, chimene chimatambalalitsa mapiko ake kuti chigwire anawo ndi kuwanyamula pa mapiko ake otambalalawo.
12 Yehova yekha ndiye anamutsogolera; popanda thandizo la mulungu wachilendo.
13 Anamuyendetsa pamwamba pa mapiri a mʼdziko ndi kumudyetsa zipatso za mʼminda. Anamudyetsa uchi wofula pa thanthwe, ndiponso mafuta ochokera mʼnthaka ya miyala,
14 pamodzi ndi chambiko ndi mkaka wochokera ku ngʼombe ndi nkhosa, ndiponso ana ankhosa onenepa ndi mbuzi, pamodzinso ndi nkhosa zazimuna zabwino za ku Basani ndiponso tirigu wabwino kwambiri. Munamwa vinyo wa thovu lofiira.
15 Yesuruni ananenepa ndi kuyamba kuwukira; atakhuta, ananenepa ndi kukula thupi. Anasiya Mulungu amene anamulenga ndipo anakana Thanthwe ndi Mpulumutsi wake.
16 Anamuchititsa nsanje ndi milungu yawo yachilendo ndiponso anamukwiyitsa ndi mafano awo onyansa.
17 Anapereka nsembe kwa ziwanda zimene si Mulungu, milungu imene sankayidziwa nʼkale lomwe, milungu yongobwera kumene, milungu imene makolo anu sankayiopa.
18 Inu munasiya Thanthwe limene linakulerani; munayiwala Mulungu amene anakubalani.
19 Yehova anaona zimenezi ndipo anawakana chifukwa ana ake aamuna ndi aakazi anamukwiyitsa.
20 Iye anati, “Ndidzawabisira nkhope yanga, ndi kuona kuti mathero awo adzakhala otani; pakuti ndi mʼbado wopotoka, ana amene ndi osakhulupirika.
21 Anandichititsa kukhala wansanje pamene ankapembedza chimene si mulungu ndi kundikwiyitsa chifukwa cha mafano awo achabechabe. Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake; ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.
22 Pakuti mkwiyo wanga wayaka ngati moto, umene umayaka mpaka ku dziko la anthu akufa. Motowo udzanyeketsa dziko lapansi ndi zokolola zake ndipo udzapsereza maziko a mapiri. (Sheol )
23 “Ndidzawawunjikira masautso ndipo mivi yanga yonse idzathera pa iwo.
24 Ndidzawatumizira njala yoopsa, malungo woopsa ndi nthenda zofa nazo; ndidzawatumizira zirombo zakuthengo zowavuta, ululu wa njoka ya mʼphiri imene imakwawa pa fumbi.
25 Mʼmisewu lupanga lidzawasandutsa kukhala wopanda ana; mantha adzalamulira nyumba zawo. Anyamata ndi atsikana adzafa, ngakhalenso makanda ndi okalamba.
26 Ine ndinanena kuti ndidzawamwaza ndi kuwafafaniza kuti anthu asawakumbukirenso,
27 koma sindinafune kuti adani anga adzandinyoze, mwina adani anga sadzandimvetsetsa ndipo adzanena kuti, ‘Tagonjetsa anthuwa ndife; Yehova sanachite zonsezi.’”
28 Iwo ndi mtundu wopanda maganizo, iwo alibe nzeru nʼpangʼono pomwe.
29 Ngati iwo akanakhala anzeru akanamvetsetsa izi ndi kuzindikira kuti mathero awo adzakhala otani!
30 Kodi munthu mmodzi akanathamangitsa bwanji anthu 1,000 kapena anthu awiri kuthamangitsa anthu 10,000, kuti awagonjetse, Thanthwe lawo likanapanda kuwagulitsa, Yehova akanapanda kuwataya?
31 Pakuti thanthwe lawo silofanana ndi Thanthwe lathu, ngakhale adani athu amavomereza zimenezi.
32 Mpesa wawo umachokera ku mpesa wa ku Sodomu ndiponso ku minda ya ku Gomora. Mphesa zawo zili ndi ululu wakupha ndipo maphava ake ndi owawa.
33 Vinyo wawo ndi wa ululu wa njoka, ululu woopsa wa mphiri.
34 “Kodi zimenezi sindinazisunge ndi kuzitsekera mʼkatikati mwa chuma changa?
35 Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine. Pa nthawi yake phazi lawo lidzaterera; tsiku lawo la masautso layandikira ndipo chiwonongeko chawo chikubwera pa iwo mofulumira.”
36 Yehova adzaweruza anthu ake ndipo adzachitira atumiki ake chifundo pamene adzaona kuti mphamvu zawo zatha ndipo kuti palibe amene watsala, kapolo kapena mfulu.
37 Iye adzanena kuti, “Nanga ili kuti milungu yawo, thanthwe limene ankabisalamo,
38 milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawo ndi kumwa vinyo wa chopereka chawo cha chakumwa?” Iwuzeni ibwere kuti idzakuthandizeni! Ibwere kuti idzakutetezenitu!
39 “Onani tsopano kuti Ine ndine Iyeyo! Palibe mulungu wina koma Ine ndekha. Ine ndimapha ndiponso kupereka moyo, ndavulaza ndipo ndidzachiritsa, ndipo palibe angathe kupulumutsa munthu mʼmanja mwanga.
40 Ndikweza dzanja langa kumwamba ndi kulumbira kuti, ‘Pali Ine wamoyo wamuyaya,
41 pamene ndidzanola lupanga langa lonyezimira ndipo dzanja liligwira pakubweretsa chiweruzo, ndidzabwezera chilango adani anga ndi kulanga onse odana nane.
42 Mivi yanga idzakhuta magazi awo pamene lupanga langa lidzawononga mnofu: magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa ukapolo, mitu ya atsogoleri a adani.’”
43 Kondwerani, inu mitundu yonse ya anthu pamodzi ndi anthu ake, pakuti Iye adzabwezera chilango anthu amene anapha atumiki ake; adzabwezera chilango adani ake ndipo adzakhululukira dziko lake ndi la anthu ake.
44 Mose anabwera ndi Yoswa mwana wa Nuni ndipo anayankhula mawu onsewa mʼnyimbo anthu akumva.
45 Mose atatsiriza kunena mawu onsewa pamtima kwa Aisraeli,
46 iye anawawuza kuti, “Muwasunge bwino mu mtima mwanu, mawu onse amene lero lino ndikukuwuzani kuti mudzawuze ana anu, kuti adzamvere mosamalitsa mawu onse a malamulo amenewa.
47 Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani.”
48 Tsiku lomwelo Yehova anawuza Mose kuti,
49 “Pita ku mapiri a ku Abarimu ukakwere pa Phiri la Nebo ku Mowabu, moyangʼanana ndi Yeriko, ndipo ukaone dziko la Kanaani, dziko limene ndikulipereka kwa Aisraeli kukhala lawo.
50 Iwe udzafera pa phiri limenelo ndipo udzapita kumene makolo ako anapita, monga mʼbale wako Aaroni anafera pa phiri la Hori ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.
51 Chifukwa chake nʼchakuti inu nonse awiri simunakhulupirike kwa Ine pamaso pa Aisraeli pa madzi a Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini chifukwa simunandilemekeze kokwanira pakati pa Aisraeli.
52 Choncho udzalionera kutali dziko limene ndikupereka kwa Aisraeli. Sudzalowa mʼdziko limene ndi kulipereka kwa Aisraeli.”