< Deuteronomo 30 >

1 Madalitso ndi matemberero awa onse amene ndawayika pamaso panu akadzafika pa inu, inu nʼkukumbukira kulikonse kumene Yehova Mulungu wanu wakubalalitsirani pakati pa mitundu ya anthu,
והיה כי יבאו עליך כל הדברים האלה הברכה והקללה אשר נתתי לפניך והשבת אל לבבך בכל הגוים אשר הדיחך יהוה אלהיך שמה׃
2 ndipo inu pamodzi ndi ana anu nʼkudzatembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse molingana ndi chilichonse chimene ndakulamulani lero lino,
ושבת עד יהוה אלהיך ושמעת בקלו ככל אשר אנכי מצוך היום אתה ובניך בכל לבבך ובכל נפשך׃
3 pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakukhalitsani monga kale ndi kukuchitirani chifundo, ndipo adzakusonkhanitsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu kumene anakubalalitsirani.
ושב יהוה אלהיך את שבותך ורחמך ושב וקבצך מכל העמים אשר הפיצך יהוה אלהיך שמה׃
4 Ngakhale atakupirikitsirani ku malekezero a dziko lapansi, adzakusonkhanitsani kuchokera kumeneko ndi kukubweretsaninso.
אם יהיה נדחך בקצה השמים משם יקבצך יהוה אלהיך ומשם יקחך׃
5 Adzakubweretsani ku dziko limene linali la makolo anu, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzakulemeretsani ndi kukuchulukitsani kupambana makolo anu.
והביאך יהוה אלהיך אל הארץ אשר ירשו אבתיך וירשתה והיטבך והרבך מאבתיך׃
6 Yehova Mulungu wanu adzasintha mitima yanu pamodzi ndi mitima ya zidzukulu zanu, kotero kuti mudzamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo mudzakhala ndi moyo.
ומל יהוה אלהיך את לבבך ואת לבב זרעך לאהבה את יהוה אלהיך בכל לבבך ובכל נפשך למען חייך׃
7 Yehova Mulungu wanu adzayika matemberero awa onse pa adani anu amene amadana nanu ndi kukuzunzani.
ונתן יהוה אלהיך את כל האלות האלה על איביך ועל שנאיך אשר רדפוך׃
8 Inu mudzamveranso Yehova ndi kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino.
ואתה תשוב ושמעת בקול יהוה ועשית את כל מצותיו אשר אנכי מצוך היום׃
9 Pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakulemeretsani pa zochita zanu zonse ndipo adzakupatsani ana ambiri, zoweta zambiri, ndiponso mudzakhala ndi zokolola zambiri za mʼdziko lanu. Yehova adzakondwera nanunso ndi kukulemeretsani monga momwe anakondwera ndi makolo anu,
והותירך יהוה אלהיך בכל מעשה ידך בפרי בטנך ובפרי בהמתך ובפרי אדמתך לטובה כי ישוב יהוה לשוש עליך לטוב כאשר שש על אבתיך׃
10 ngati mudzamvera Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ake ndi mawu ake amene alembedwa Mʼbuku ili la Malamulo ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
כי תשמע בקול יהוה אלהיך לשמר מצותיו וחקתיו הכתובה בספר התורה הזה כי תשוב אל יהוה אלהיך בכל לבבך ובכל נפשך׃
11 Tsopano zimene ndikukulamulirani leroli sizovuta kapena zapatali.
כי המצוה הזאת אשר אנכי מצוך היום לא נפלאת הוא ממך ולא רחקה הוא׃
12 Sizili kumwamba, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene akwere kumwamba kuti akazitenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?”
לא בשמים הוא לאמר מי יעלה לנו השמימה ויקחה לנו וישמענו אתה ונעשנה׃
13 Komanso sizili pa tsidya la nyanja, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene adzawoloke nyanja kuti akatenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?”
ולא מעבר לים הוא לאמר מי יעבר לנו אל עבר הים ויקחה לנו וישמענו אתה ונעשנה׃
14 Ayi, mawu ali pafupi ndi inu; ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu kuti muwamvere.
כי קרוב אליך הדבר מאד בפיך ובלבבך לעשתו׃
15 Taonani, lero ine ndayika pamaso panu moyo ndi zokoma, imfa ndi chiwonongeko.
ראה נתתי לפניך היום את החיים ואת הטוב ואת המות ואת הרע׃
16 Pakuti lero ndikukulamulani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kuti muyende mʼnjira zake, ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake. Mukatero mudzakhala ndi moyo ndi kuchulukana, ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukulowa kukakhalamo.
אשר אנכי מצוך היום לאהבה את יהוה אלהיך ללכת בדרכיו ולשמר מצותיו וחקתיו ומשפטיו וחיית ורבית וברכך יהוה אלהיך בארץ אשר אתה בא שמה לרשתה׃
17 Koma ngati mtima wanu udzatembenuka, inu nʼkukhala osandimvera, ndipo ngati mudzatengeka ndi kupita kukagwadira milungu ina ndi kuyipembedza,
ואם יפנה לבבך ולא תשמע ונדחת והשתחוית לאלהים אחרים ועבדתם׃
18 lero ndikulengeza kwa inu kuti mudzawonongeka ndithu. Simudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukulowamo pamene mukuwoloka Yorodani kuti mulitenge.
הגדתי לכם היום כי אבד תאבדון לא תאריכן ימים על האדמה אשר אתה עבר את הירדן לבא שמה לרשתה׃
19 Lero kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zodzakutsutsani pakuti ndayika pamaso panu moyo ndi imfa, madalitso ndi matemberero. Tsopano sankhani moyo kuti inu ndi ana anu mukhale ndi moyo.
העידתי בכם היום את השמים ואת הארץ החיים והמות נתתי לפניך הברכה והקללה ובחרת בחיים למען תחיה אתה וזרעך׃
20 Ndi kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kukhulupirika kwa Iye. Pakuti Yehova ndiye moyo wanu, ndipo mudzakhala zaka zambiri mʼdziko limene analumbira kulipereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
לאהבה את יהוה אלהיך לשמע בקלו ולדבקה בו כי הוא חייך וארך ימיך לשבת על האדמה אשר נשבע יהוה לאבתיך לאברהם ליצחק וליעקב לתת להם׃

< Deuteronomo 30 >