< Deuteronomo 28 >

1 Ngati mumvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamalitsa malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, Yehova Mulungu wanu adzakukwezani pamwamba pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
וְהָיָה אִם־שָׁמוֹעַ תִּשְׁמַע בְּקוֹל יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ לִשְׁמֹר לַעֲשׂוֹת אֶת־כׇּל־מִצְוֺתָיו אֲשֶׁר אָנֹכִי מְצַוְּךָ הַיּוֹם וּנְתָנְךָ יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ עֶלְיוֹן עַל כׇּל־גּוֹיֵי הָאָֽרֶץ׃
2 Madalitso awa adzabwera kwa inu ndi kuyenda nanu ngati mumvera Yehova Mulungu wanu:
וּבָאוּ עָלֶיךָ כׇּל־הַבְּרָכוֹת הָאֵלֶּה וְהִשִּׂיגֻךָ כִּי תִשְׁמַע בְּקוֹל יְהֹוָה אֱלֹהֶֽיךָ׃
3 Mudzadalitsika mʼmizinda yanu ndi kudalitsika mʼdzikolo.
בָּרוּךְ אַתָּה בָּעִיר וּבָרוּךְ אַתָּה בַּשָּׂדֶֽה׃
4 Yehova adzadalitsa ana anu, zokolola za mʼdziko lanu, ngʼombe zanu pamodzi ndi ziweto zanu zonse.
בָּרוּךְ פְּרִֽי־בִטְנְךָ וּפְרִי אַדְמָתְךָ וּפְרִי בְהֶמְתֶּךָ שְׁגַר אֲלָפֶיךָ וְעַשְׁתְּרוֹת צֹאנֶֽךָ׃
5 Dengu lanu ndi chiwaya chanu cha buledi zidzadalitsika.
בָּרוּךְ טַנְאֲךָ וּמִשְׁאַרְתֶּֽךָ׃
6 Mudzadalitsika pa kulowa kwanu ndi pa kutuluka kwanu.
בָּרוּךְ אַתָּה בְּבֹאֶךָ וּבָרוּךְ אַתָּה בְּצֵאתֶֽךָ׃
7 Yehova adzaonetsetsa kuti adani anu amene adzakuwukirani agonjetsedwe pamaso panu. Iwo adzabwera kwa inu kuchokera mbali imodzi koma adzakuthawani ku mbali zisanu ndi ziwiri.
יִתֵּן יְהֹוָה אֶת־אֹיְבֶיךָ הַקָּמִים עָלֶיךָ נִגָּפִים לְפָנֶיךָ בְּדֶרֶךְ אֶחָד יֵצְאוּ אֵלֶיךָ וּבְשִׁבְעָה דְרָכִים יָנוּסוּ לְפָנֶֽיךָ׃
8 Yehova adzatumiza madalitso pa nkhokwe zanu ndi pa chilichonse chimene muchikhudza. Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene akukupatsani.
יְצַו יְהֹוָה אִתְּךָ אֶת־הַבְּרָכָה בַּאֲסָמֶיךָ וּבְכֹל מִשְׁלַח יָדֶךָ וּבֵרַכְךָ בָּאָרֶץ אֲשֶׁר־יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ נֹתֵן לָֽךְ׃
9 Yehova Mulungu wanu adzachititsa kuti mukhale anthu ake opatulika, monga momwe analonjezera pa malumbiro ake, ngati musunga malamulo ake ndi kuyenda mʼnjira zake.
יְקִֽימְךָ יְהֹוָה לוֹ לְעַם קָדוֹשׁ כַּאֲשֶׁר נִֽשְׁבַּֽע־לָךְ כִּי תִשְׁמֹר אֶת־מִצְוֺת יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ וְהָלַכְתָּ בִּדְרָכָֽיו׃
10 Pamenepo anthu onse a dziko lapansi adzaona kuti mumadziwika ndi dzina la Yehova ndipo adzakuopani.
וְרָאוּ כׇּל־עַמֵּי הָאָרֶץ כִּי שֵׁם יְהֹוָה נִקְרָא עָלֶיךָ וְיָֽרְאוּ מִמֶּֽךָּ׃
11 Yehova adzakupambanitsani kwambiri ndipo adzakupatsani ana ambiri, ziweto zambiri, ndi zokolola zochuluka, mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani.
וְהוֹתִרְךָ יְהֹוָה לְטוֹבָה בִּפְרִי בִטְנְךָ וּבִפְרִי בְהֶמְתְּךָ וּבִפְרִי אַדְמָתֶךָ עַל הָאֲדָמָה אֲשֶׁר נִשְׁבַּע יְהֹוָה לַאֲבֹתֶיךָ לָתֶת לָֽךְ׃
12 Yehova adzatsekula kumwamba kumene amasungirako chuma chake, kutumiza mvula mʼdziko lanu pa nthawi yake ndi kudalitsa ntchito yonse ya manja anu. Mudzakongoza mitundu yambiri koma inu simudzakongola kwa aliyense.
יִפְתַּח יְהֹוָה ׀ לְךָ אֶת־אוֹצָרוֹ הַטּוֹב אֶת־הַשָּׁמַיִם לָתֵת מְטַֽר־אַרְצְךָ בְּעִתּוֹ וּלְבָרֵךְ אֵת כׇּל־מַעֲשֵׂה יָדֶךָ וְהִלְוִיתָ גּוֹיִם רַבִּים וְאַתָּה לֹא תִלְוֶֽה׃
13 Yehova adzakuthandizani kukhala mutu osati mchira. Mukakhala ndi chidwi ndi malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero lino ndi kuwatsata mosamalitsa, inu mudzakhala apamwamba nthawi zonse osati apansi.
וּנְתָֽנְךָ יְהֹוָה לְרֹאשׁ וְלֹא לְזָנָב וְהָיִיתָ רַק לְמַעְלָה וְלֹא תִהְיֶה לְמָטָּה כִּֽי־תִשְׁמַע אֶל־מִצְוֺת ׀ יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ אֲשֶׁר אָנֹכִי מְצַוְּךָ הַיּוֹם לִשְׁמֹר וְלַעֲשֽׂוֹת׃
14 Musapatukire ku dzanja lamanja kapena lamanzere pa lamulo lina lililonse limene ndikukupatsani lero lino ndi kumatsatira kapena kuyitumikira milungu ina.
וְלֹא תָסוּר מִכׇּל־הַדְּבָרִים אֲשֶׁר אָנֹכִי מְצַוֶּה אֶתְכֶם הַיּוֹם יָמִין וּשְׂמֹאול לָלֶכֶת אַחֲרֵי אֱלֹהִים אֲחֵרִים לְעׇבְדָֽם׃
15 Koma ngati simumvera Yehova Mulungu wanu ndi kusatsata mosamalitsa malamulo ake ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, matemberero awa adzabwera pa inu ndikukugonjetsani:
וְהָיָה אִם־לֹא תִשְׁמַע בְּקוֹל יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ לִשְׁמֹר לַעֲשׂוֹת אֶת־כׇּל־מִצְוֺתָיו וְחֻקֹּתָיו אֲשֶׁר אָנֹכִי מְצַוְּךָ הַיּוֹם וּבָאוּ עָלֶיךָ כׇּל־הַקְּלָלוֹת הָאֵלֶּה וְהִשִּׂיגֽוּךָ׃
16 Mudzatembereredwa mu mzinda ndi kutembereredwa mʼmudzi.
אָרוּר אַתָּה בָּעִיר וְאָרוּר אַתָּה בַּשָּׂדֶֽה׃
17 Dengu lanu ndi chiwaya chanu cha buledi zidzatembereredwa.
אָרוּר טַנְאֲךָ וּמִשְׁאַרְתֶּֽךָ׃
18 Zipatso za mʼmimba mwanu zidzatembereredwa, ndiponso zomera za mʼdziko lanu, ana angʼombe zanu ndi ana ankhosa zanu zidzatembereredwa.
אָרוּר פְּרִֽי־בִטְנְךָ וּפְרִי אַדְמָתֶךָ שְׁגַר אֲלָפֶיךָ וְעַשְׁתְּרֹת צֹאנֶֽךָ׃
19 Mudzatembereredwa pa kulowa kwanu ndi pa kutuluka kwanu.
אָרוּר אַתָּה בְּבֹאֶךָ וְאָרוּר אַתָּה בְּצֵאתֶֽךָ׃
20 Yehova adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndi minyozo pa chilichonse chimene mudzachichita mpaka mudzawonongedwa ndi kukhala bwinja mofulumira chifukwa cha zoyipa zimene mwazichita pa kumutaya Yehova.
יְשַׁלַּח יְהֹוָה ׀ בְּךָ אֶת־הַמְּאֵרָה אֶת־הַמְּהוּמָה וְאֶת־הַמִּגְעֶרֶת בְּכׇל־מִשְׁלַח יָדְךָ אֲשֶׁר תַּעֲשֶׂה עַד הִשָּׁמֶדְךָ וְעַד־אֲבׇדְךָ מַהֵר מִפְּנֵי רֹעַ מַֽעֲלָלֶיךָ אֲשֶׁר עֲזַבְתָּֽנִי׃
21 Yehova adzakugwetserani mliri wa matenda mpaka atakuwonongani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali.
יַדְבֵּק יְהֹוָה בְּךָ אֶת־הַדָּבֶר עַד כַּלֹּתוֹ אֹֽתְךָ מֵעַל הָאֲדָמָה אֲשֶׁר־אַתָּה בָא־שָׁמָּה לְרִשְׁתָּֽהּ׃
22 Yehova adzakukanthani ndi nthenda yowondetsa, ya malungo ndi ya zotupatupa, ndi kutentha kwakukulu ndi chilala, ndi chinsikwi ndi chiwawu zimene zidzakusautsani mpaka mutawonongeka.
יַכְּכָה יְהֹוָה בַּשַּׁחֶפֶת וּבַקַּדַּחַת וּבַדַּלֶּקֶת וּבַֽחַרְחֻר וּבַחֶרֶב וּבַשִּׁדָּפוֹן וּבַיֵּרָקוֹן וּרְדָפוּךָ עַד אׇבְדֶֽךָ׃
23 Mitambo ya pamutu panu idzawuma ngati mkuwa ndipo sidzagwetsa mvula mpaka nthaka yanu idzawuma gwaa ngati chitsulo.
וְהָיוּ שָׁמֶיךָ אֲשֶׁר עַל־רֹאשְׁךָ נְחֹשֶׁת וְהָאָרֶץ אֲשֶׁר־תַּחְתֶּיךָ בַּרְזֶֽל׃
24 Mʼmalo mwa mvula Yehova adzakupatsani fumbi ndi dothi ndipo lidzakugwerani kuchokera kumwamba mpaka mutawonongeka.
יִתֵּן יְהֹוָה אֶת־מְטַר אַרְצְךָ אָבָק וְעָפָר מִן־הַשָּׁמַיִם יֵרֵד עָלֶיךָ עַד הִשָּׁמְדָֽךְ׃
25 Yehova adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Mudzadzera njira imodzi pokalimbana ndi adani anu koma pothawa mudzabalalika mbali zisanu ndi ziwiri. Mudzakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.
יִתֶּנְךָ יְהֹוָה ׀ נִגָּף לִפְנֵי אֹיְבֶיךָ בְּדֶרֶךְ אֶחָד תֵּצֵא אֵלָיו וּבְשִׁבְעָה דְרָכִים תָּנוּס לְפָנָיו וְהָיִיתָ לְזַֽעֲוָה לְכֹל מַמְלְכוֹת הָאָֽרֶץ׃
26 Mitembo yanu idzadyedwa ndi mbalame zamumlengalenga ndi nyama zakutchire, ndipo palibe amene adzaziyingitse.
וְהָיְתָה נִבְלָֽתְךָ לְמַֽאֲכָל לְכׇל־עוֹף הַשָּׁמַיִם וּלְבֶהֱמַת הָאָרֶץ וְאֵין מַחֲרִֽיד׃
27 Yehova adzakusautsani ndi zithupsa za ku Igupto ndi zotupatupa, zipere, ndi mphere zimene simudzachiritsika nazo.
יַכְּכָה יְהֹוָה בִּשְׁחִין מִצְרַיִם (ובעפלים) [וּבַטְּחֹרִים] וּבַגָּרָב וּבֶחָרֶס אֲשֶׁר לֹא־תוּכַל לְהֵרָפֵֽא׃
28 Yehova adzakusautsani inu ndi misala, khungu ndi chisokonekero cha maganizo.
יַכְּכָה יְהֹוָה בְּשִׁגָּעוֹן וּבְעִוָּרוֹן וּבְתִמְהוֹן לֵבָֽב׃
29 Masanasana mudzayenda ngati muli mu mdima, kumafufuzira njira ngati wosaona. Mudzakhala olephera pa chilichonse mungachite. Tsiku ndi tsiku mudzaponderezedwa ndi kuberedwa wopanda wokupulumutsani.
וְהָיִיתָ מְמַשֵּׁשׁ בַּֽצׇּהֳרַיִם כַּאֲשֶׁר יְמַשֵּׁשׁ הַֽעִוֵּר בָּאֲפֵלָה וְלֹא תַצְלִיחַ אֶת־דְּרָכֶיךָ וְהָיִיתָ אַךְ עָשׁוּק וְגָזוּל כׇּל־הַיָּמִים וְאֵין מוֹשִֽׁיעַ׃
30 Mudzachita chinkhoswe ndi mkazi, koma wina adzakulandani ndi kumukwatira. Mudzamanga nyumba koma simudzagonamo. Mudzalima munda wamphesa koma simudzadyako zipatso zake.
אִשָּׁה תְאָרֵשׂ וְאִישׁ אַחֵר (ישגלנה) [יִשְׁכָּבֶנָּה] בַּיִת תִּבְנֶה וְלֹא־תֵשֵׁב בּוֹ כֶּרֶם תִּטַּע וְלֹא תְחַלְּלֶֽנּוּ׃
31 Ngʼombe yanu yamtheno idzaphedwa inu muli pomwepo koma simudzadyako. Bulu wanu adzalandidwa kwa inu mwamakani osabwera nayenso. Nkhosa zanu zidzapatsidwa kwa adani anu, ndipo palibe amene adzazipulumutsa.
שׁוֹרְךָ טָבוּחַ לְעֵינֶיךָ וְלֹא תֹאכַל מִמֶּנּוּ חֲמֹֽרְךָ גָּזוּל מִלְּפָנֶיךָ וְלֹא יָשׁוּב לָךְ צֹֽאנְךָ נְתֻנוֹת לְאֹיְבֶיךָ וְאֵין לְךָ מוֹשִֽׁיעַ׃
32 Ana anu aamuna ndi aakazi adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina ndipo inu mudzafika potopa ndi kulefuka nʼkudikirira tsiku ndi tsiku kuti mwina anawo abwerako.
בָּנֶיךָ וּבְנֹתֶיךָ נְתֻנִים לְעַם אַחֵר וְעֵינֶיךָ רֹאוֹת וְכָלוֹת אֲלֵיהֶם כׇּל־הַיּוֹם וְאֵין לְאֵל יָדֶֽךָ׃
33 Anthu amene simukuwadziwa adzakudyerani zokolola zanu, ndipo mudzakhala mukuponderezedwa mwankhanza masiku onse.
פְּרִי אַדְמָֽתְךָ וְכׇל־יְגִיעֲךָ יֹאכַל עַם אֲשֶׁר לֹא־יָדָעְתָּ וְהָיִיתָ רַק עָשׁוּק וְרָצוּץ כׇּל־הַיָּמִֽים׃
34 Zimene muzidzaziona zidzakusokonezani mitu.
וְהָיִיתָ מְשֻׁגָּע מִמַּרְאֵה עֵינֶיךָ אֲשֶׁר תִּרְאֶֽה׃
35 Yehova adzakusautsani ndi zithupsa zaululu ndi zosachiritsika za mʼmawondo ndi mʼmiyendo ndipo zidzafalikira kuchoka kuphazi mpaka kumutu.
יַכְּכָה יְהֹוָה בִּשְׁחִין רָע עַל־הַבִּרְכַּיִם וְעַל־הַשֹּׁקַיִם אֲשֶׁר לֹא־תוּכַל לְהֵרָפֵא מִכַּף רַגְלְךָ וְעַד קׇדְקֳדֶֽךָ׃
36 Yehova adzakuthamangitsirani, inu ndi mafumu anu amene muwayika, ku dziko losadziwika kwa inu ndi kwa makolo anu. Kumeneko mudzakapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi miyala.
יוֹלֵךְ יְהֹוָה אֹתְךָ וְאֶֽת־מַלְכְּךָ אֲשֶׁר תָּקִים עָלֶיךָ אֶל־גּוֹי אֲשֶׁר לֹא־יָדַעְתָּ אַתָּה וַאֲבֹתֶיךָ וְעָבַדְתָּ שָּׁם אֱלֹהִים אֲחֵרִים עֵץ וָאָֽבֶן׃
37 Inu mudzakhala chinthu chochititsa mantha kuchisunga ndiponso chinthu chotukwanidwa ndi chonyozeka kwa anthu a mitundu yonse kumene Yehova adzakuthamangitsirani.
וְהָיִיתָ לְשַׁמָּה לְמָשָׁל וְלִשְׁנִינָה בְּכֹל הָֽעַמִּים אֲשֶׁר־יְנַהֶגְךָ יְהֹוָה שָֽׁמָּה׃
38 Mudzadzala mbewu zambiri ku munda koma mudzakolola pangʼono, chifukwa dzombe lidzaziwononga.
זֶרַע רַב תּוֹצִיא הַשָּׂדֶה וּמְעַט תֶּאֱסֹף כִּי יַחְסְלֶנּוּ הָאַרְבֶּֽה׃
39 Mudzadzala mpesa ndi kulimirira koma vinyo wake simudzamumwa kapena kukolola mphesazo, chifukwa mphutsi zidzadya mphesazo.
כְּרָמִים תִּטַּע וְעָבָדְתָּ וְיַיִן לֹֽא־תִשְׁתֶּה וְלֹא תֶאֱגֹר כִּי תֹאכְלֶנּוּ הַתֹּלָֽעַת׃
40 Mudzakhala ndi mitengo ya olivi mʼdziko lanu lonse koma simudzagwiritsa ntchito mafuta ake, chifukwa zipatso zake zidzayoyoka.
זֵיתִים יִהְיוּ לְךָ בְּכׇל־גְּבוּלֶךָ וְשֶׁמֶן לֹא תָסוּךְ כִּי יִשַּׁל זֵיתֶֽךָ׃
41 Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi koma sadzakhala anu, chifukwa adzapita ku ukapolo.
בָּנִים וּבָנוֹת תּוֹלִיד וְלֹא־יִהְיוּ לָךְ כִּי יֵלְכוּ בַּשֶּֽׁבִי׃
42 Magulumagulu a dzombe adzawononga mitengo yanu ndi mbewu za mʼdziko lanu.
כׇּל־עֵצְךָ וּפְרִי אַדְמָתֶךָ יְיָרֵשׁ הַצְּלָצַֽל׃
43 Mlendo wokhala pakati panu adzatukuka kuposa inu, koma inuyo mudzaloweralowera pansi.
הַגֵּר אֲשֶׁר בְּקִרְבְּךָ יַעֲלֶה עָלֶיךָ מַעְלָה מָּעְלָה וְאַתָּה תֵרֵד מַטָּה מָּֽטָּה׃
44 Iye adzakubwereketsani, koma inu simudzatha kubwereketsa. Iye adzakhala mutu ndipo inu mudzakhala mchira.
הוּא יַלְוְךָ וְאַתָּה לֹא תַלְוֶנּוּ הוּא יִהְיֶה לְרֹאשׁ וְאַתָּה תִּֽהְיֶה לְזָנָֽב׃
45 Matemberero onsewa adzabwera pa inu. Adzakulondolani ndi kukugonjetsani mpaka mutawonongeka, chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene anakupatsani.
וּבָאוּ עָלֶיךָ כׇּל־הַקְּלָלוֹת הָאֵלֶּה וּרְדָפוּךָ וְהִשִּׂיגוּךָ עַד הִשָּׁמְדָךְ כִּי־לֹא שָׁמַעְתָּ בְּקוֹל יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ לִשְׁמֹר מִצְוֺתָיו וְחֻקֹּתָיו אֲשֶׁר צִוָּֽךְ׃
46 Matemberero amenewa adzakhala chizindikiro ndi chozizwitsa kwa inu ndi zidzukulu zanu mpaka kalekale.
וְהָיוּ בְךָ לְאוֹת וּלְמוֹפֵת וּֽבְזַרְעֲךָ עַד־עוֹלָֽם׃
47 Pakuti inu simunatumikire Yehova Mulungu wanu pa nthawi imene zinthu zinkakuyenderani bwino,
תַּחַת אֲשֶׁר לֹא־עָבַדְתָּ אֶת־יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ בְּשִׂמְחָה וּבְטוּב לֵבָב מֵרֹב כֹּֽל׃
48 chomwecho pa nthawi ya njala ndi ludzu, ya maliseche ndi umphawi woopsa, mudzatumikira adani amene Yehova adzakutumizirani. Iye adzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwanu kufikira atakuwonongani.
וְעָבַדְתָּ אֶת־אֹיְבֶיךָ אֲשֶׁר יְשַׁלְּחֶנּוּ יְהֹוָה בָּךְ בְּרָעָב וּבְצָמָא וּבְעֵירֹם וּבְחֹסֶר כֹּל וְנָתַן עֹל בַּרְזֶל עַל־צַוָּארֶךָ עַד הִשְׁמִידוֹ אֹתָֽךְ׃
49 Yehova adzakutumizirani mtundu wa anthu kuchokera kutali kumapeto kwa dziko lapansi nudzachita ngati mphungu yowulukira pansi, mtundu wa anthu umene chiyankhulo chawo simudzachimva,
יִשָּׂא יְהֹוָה עָלֶיךָ גּוֹי מֵרָחֹק מִקְצֵה הָאָרֶץ כַּאֲשֶׁר יִדְאֶה הַנָּשֶׁר גּוֹי אֲשֶׁר לֹא־תִשְׁמַע לְשֹׁנֽוֹ׃
50 mtundu wooneka wochititsa mantha, wopanda ulemu kwa okalamba kapena chisoni kwa ana.
גּוֹי עַז פָּנִים אֲשֶׁר לֹא־יִשָּׂא פָנִים לְזָקֵן וְנַעַר לֹא יָחֹֽן׃
51 Iwo adzagwira ana a ziweto zanu, natenga zokolola za mʼdziko lanu kufikira mutawonongeka. Iwo sadzakusiyirani tirigu, vinyo watsopano kapena mafuta a olivi, kapena mwana wangʼombe aliyense kapena mwana wankhosa mpaka mutasanduka bwinja.
וְאָכַל פְּרִי בְהֶמְתְּךָ וּפְרִֽי־אַדְמָתְךָ עַד הִשָּׁמְדָךְ אֲשֶׁר לֹא־יַשְׁאִיר לְךָ דָּגָן תִּירוֹשׁ וְיִצְהָר שְׁגַר אֲלָפֶיךָ וְעַשְׁתְּרֹת צֹאנֶךָ עַד הַאֲבִידוֹ אֹתָֽךְ׃
52 Iwo adzathira nkhondo mizinda yonse mʼdziko lanu lonse mpaka malinga anu ataliatali omwe mumadalira aja atagwa. Adzathira nkhondo mizinda yonse ya mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
וְהֵצַר לְךָ בְּכׇל־שְׁעָרֶיךָ עַד רֶדֶת חֹמֹתֶיךָ הַגְּבֹהֹת וְהַבְּצֻרוֹת אֲשֶׁר אַתָּה בֹּטֵחַ בָּהֵן בְּכׇל־אַרְצֶךָ וְהֵצַר לְךָ בְּכׇל־שְׁעָרֶיךָ בְּכׇל־אַרְצְךָ אֲשֶׁר נָתַן יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ לָֽךְ׃
53 Chifukwa cha zosautsa zimene mdani wanu adzabweretsa pa nthawi yokuthirani nkhondo, inu mudzadya ana anu, mnofu wa ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.
וְאָכַלְתָּ פְרִֽי־בִטְנְךָ בְּשַׂר בָּנֶיךָ וּבְנֹתֶיךָ אֲשֶׁר נָתַן־לְךָ יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ בְּמָצוֹר וּבְמָצוֹק אֲשֶׁר־יָצִיק לְךָ אֹיְבֶֽךָ׃
54 Ngakhale munthu woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu sadzakhala ndi chifundo pa mʼbale wake weniweni kapena mkazi wake amene iye amamukonda kapena ana ake otsalawo,
הָאִישׁ הָרַךְ בְּךָ וְהֶעָנֹג מְאֹד תֵּרַע עֵינוֹ בְאָחִיו וּבְאֵשֶׁת חֵיקוֹ וּבְיֶתֶר בָּנָיו אֲשֶׁר יוֹתִֽיר׃
55 ndipo sadzagawirako aliyense wa iwo mnofu wa ana ake amene akudyawo. Kadzakhala kali komweko basi kamene kamutsalira chifukwa cha msautso umene mdani wanu adzagwetsa pa nthawi yothira nkhondo mizinda yanu yonse.
מִתֵּת ׀ לְאַחַד מֵהֶם מִבְּשַׂר בָּנָיו אֲשֶׁר יֹאכֵל מִבְּלִי הִשְׁאִֽיר־לוֹ כֹּל בְּמָצוֹר וּבְמָצוֹק אֲשֶׁר יָצִיק לְךָ אֹיִבְךָ בְּכׇל־שְׁעָרֶֽיךָ׃
56 Mayi woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu, uja woti sangayerekeze kuponda pansi, adzabisira mwamuna wake amene amamukonda ndi ana ake omwe aamuna ndi aakazi
הָרַכָּה בְךָ וְהָעֲנֻגָּה אֲשֶׁר לֹֽא־נִסְּתָה כַף־רַגְלָהּ הַצֵּג עַל־הָאָרֶץ מֵהִתְעַנֵּג וּמֵרֹךְ תֵּרַע עֵינָהּ בְּאִישׁ חֵיקָהּ וּבִבְנָהּ וּבְבִתָּֽהּ׃
57 zotsalira za uchembere zochoka mʼmimba mwake ndi ana amene wabereka. Pakuti adzafuna kuti adye zimenezi yekha mobisa pa nthawi yothiridwa nkhondo chifukwa cha masautso amene mdani wanu adzagwetsa pa inu mʼmizinda yanu.
וּֽבְשִׁלְיָתָהּ הַיּוֹצֵת ׀ מִבֵּין רַגְלֶיהָ וּבְבָנֶיהָ אֲשֶׁר תֵּלֵד כִּֽי־תֹאכְלֵם בְּחֹסֶר־כֹּל בַּסָּתֶר בְּמָצוֹר וּבְמָצוֹק אֲשֶׁר יָצִיק לְךָ אֹיִבְךָ בִּשְׁעָרֶֽיךָ׃
58 Ngati simutsata mosamalitsa mawu onse a malamulo awa amene alembedwa mʼbuku lino, komanso ngati simuopa dzina la ulemerero ndi loopsa, dzina la Yehova Mulungu wanu,
אִם־לֹא תִשְׁמֹר לַעֲשׂוֹת אֶת־כׇּל־דִּבְרֵי הַתּוֹרָה הַזֹּאת הַכְּתֻבִים בַּסֵּפֶר הַזֶּה לְיִרְאָה אֶת־הַשֵּׁם הַנִּכְבָּד וְהַנּוֹרָא הַזֶּה אֵת יְהֹוָה אֱלֹהֶֽיךָ׃
59 Yehova adzatumiza pa inu ndi zidzukulu zanu miliri yoopsa, zosautsa zowawa ndi zokhalitsa, ndi matenda aakulu ndi ovuta kuchiritsika.
וְהִפְלָא יְהֹוָה אֶת־מַכֹּתְךָ וְאֵת מַכּוֹת זַרְעֶךָ מַכּוֹת גְּדֹלֹת וְנֶאֱמָנוֹת וׇחֳלָיִם רָעִים וְנֶאֱמָנִֽים׃
60 Adzakubweretserani matenda onse a ku Igupto aja mumawaopawa ndipo adzakukanirirani.
וְהֵשִׁיב בְּךָ אֵת כׇּל־מַדְוֵה מִצְרַיִם אֲשֶׁר יָגֹרְתָּ מִפְּנֵיהֶם וְדָבְקוּ בָּֽךְ׃
61 Yehova adzakubweretseraninso mtundu uliwonse wa matenda ndi zosautsa zimene sizinalembedwe mʼbuku la malamulo lino, mpaka mutawonongeka.
גַּם כׇּל־חֳלִי וְכׇל־מַכָּה אֲשֶׁר לֹא כָתוּב בְּסֵפֶר הַתּוֹרָה הַזֹּאת יַעְלֵם יְהֹוָה עָלֶיךָ עַד הִשָּׁמְדָֽךְ׃
62 Inu aja munali ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba mudzatsala ochepa chabe chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu.
וְנִשְׁאַרְתֶּם בִּמְתֵי מְעָט תַּחַת אֲשֶׁר הֱיִיתֶם כְּכוֹכְבֵי הַשָּׁמַיִם לָרֹב כִּֽי־לֹא שָׁמַעְתָּ בְּקוֹל יְהֹוָה אֱלֹהֶֽיךָ׃
63 Monga kunamukomera Yehova kukulemeretsani ndi kukuchulukitsani, momwemonso kudzamukondweretsa kukunthani ndi kukuwonongani. Inu mudzazulidwa kukuchotsani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali.
וְהָיָה כַּאֲשֶׁר־שָׂשׂ יְהֹוָה עֲלֵיכֶם לְהֵיטִיב אֶתְכֶם וּלְהַרְבּוֹת אֶתְכֶם כֵּן יָשִׂישׂ יְהֹוָה עֲלֵיכֶם לְהַאֲבִיד אֶתְכֶם וּלְהַשְׁמִיד אֶתְכֶם וְנִסַּחְתֶּם מֵעַל הָאֲדָמָה אֲשֶׁר־אַתָּה בָא־שָׁמָּה לְרִשְׁתָּֽהּ׃
64 Kenaka Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu yonse, kuchokera ku mapeto a dziko kufika ku mapeto ena. Kumeneko mudzapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi ya miyala, imene inu eni kapena makolo anu sanayidziwepo.
וֶהֱפִֽיצְךָ יְהֹוָה בְּכׇל־הָעַמִּים מִקְצֵה הָאָרֶץ וְעַד־קְצֵה הָאָרֶץ וְעָבַדְתָּ שָּׁם אֱלֹהִים אֲחֵרִים אֲשֶׁר לֹא־יָדַעְתָּ אַתָּה וַאֲבֹתֶיךָ עֵץ וָאָֽבֶן׃
65 Pakati pa mitundu ya anthu imeneyi simudzapeza mpata, popanda malo woti nʼkuyikapo phazi. Kumeneko Yehova adzakupatsani moyo wa nkhawa, maso otopa ndi chiyembekezo, ndi mtima wosakhazikika.
וּבַגּוֹיִם הָהֵם לֹא תַרְגִּיעַ וְלֹא־יִהְיֶה מָנוֹחַ לְכַף־רַגְלֶךָ וְנָתַן יְהֹוָה לְךָ שָׁם לֵב רַגָּז וְכִלְיוֹן עֵינַיִם וְדַאֲבוֹן נָֽפֶשׁ׃
66 Inu mudzakhala osakhazikika mopitirira, odzazidwa ndi mantha usiku ndi usana womwe, osowa chitsimikizo cha pa moyo wanu.
וְהָיוּ חַיֶּיךָ תְּלֻאִים לְךָ מִנֶּגֶד וּפָֽחַדְתָּ לַיְלָה וְיוֹמָם וְלֹא תַאֲמִין בְּחַיֶּֽיךָ׃
67 Mmawa muzidzati, “Chikhala anali madzulo!” ndipo madzulo mudzati, “Chikhala unali mmawa!” Mudzanena zimenezi chifukwa cha mantha amene adzakhale mu mtima mwanu ndi chifukwa cha zomwe muzidzaziona.
בַּבֹּקֶר תֹּאמַר מִֽי־יִתֵּן עֶרֶב וּבָעֶרֶב תֹּאמַר מִֽי־יִתֵּן בֹּקֶר מִפַּחַד לְבָֽבְךָ אֲשֶׁר תִּפְחָד וּמִמַּרְאֵה עֵינֶיךָ אֲשֶׁר תִּרְאֶֽה׃
68 Yehova adzakubwezani ku Igupto pa sitima zapamadzi paulendo umene Ine ndinati musawuyendenso. Kumeneko mudzadzitsatsa nokha kwa adani anu monga akapolo aamuna ndi aakazi, koma palibe amene adzakuguleni.
וֶהֱשִֽׁיבְךָ יְהֹוָה ׀ מִצְרַיִם בׇּאֳנִיּוֹת בַּדֶּרֶךְ אֲשֶׁר אָמַרְתִּֽי לְךָ לֹא־תֹסִיף עוֹד לִרְאֹתָהּ וְהִתְמַכַּרְתֶּם שָׁם לְאֹיְבֶיךָ לַעֲבָדִים וְלִשְׁפָחוֹת וְאֵין קֹנֶֽה׃

< Deuteronomo 28 >