< Deuteronomo 25 >
1 Anthu akasemphana mawu, ayenera kupita ku bwalo la milandu ndipo woweruza adzaweruza mlanduwo. Adzamasula wosalakwa nalanga wolakwa.
2 Munthu akapezeka wolakwa ayenera kukwapulidwa, woweruza amugoneke pansi wolakwayo ndipo akwapulidwe pamaso pake zikoti zochuluka molingana ndi mlandu wake,
3 koma asamukwapule zikoti zopitirira makumi anayi. Akakwapulidwa kupitirira apo ndiye kuti mʼbale wanuyo anyozeka pamaso panu.
4 Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu.
5 Ngati abale akukhala pamodzi ndipo wina mwa iwo akamwalira wosasiya mwana wamwamuna, mkazi wamasiyeyo asakakwatiwe ndi mlendo. Mʼbale wake wa mwamuna wakeyo amukwatire kukwaniritsa chimene akuyenera kuchita kwa mlamu wakeyo.
6 Mwana wamwamuna woyamba amene mayiyo angabereke ayenera kutenga dzina la mwamuna wake womwalirayo kuti dzina lake lisafafanizike mu Israeli.
7 Komabe, ngati munthu sakufuna kukwatira mkazi wa mʼbale wakeyo, mkaziyo ayenera kupita kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda ndi kukanena kuti, “Mʼbale wake wa mwamuna wanga akukana kupitiriza dzina la mʼbale wake mu Israeli. Iye akukana kulowa chokolo.”
8 Pamenepo akuluakulu a mu mzinda wawowo adzamuyitanitsa nakamba naye. Ngati alimbikirabe kunena kuti, “Ine sindikufuna kumukwatira mkaziyu,”
9 mkazi wamasiye wa mʼbale wakeyo adzapita kwa iye pamaso pa akuluakuluwo namuvula nsapato imodzi, adzamulavulire kumaso nʼkunena kuti, “Izi ndi zimene amachitira munthu amene safuna kupitiriza mbiri ya banja la mʼbale wake.”
10 Mbiri ya banja la munthu ameneyo idzadziwika mu Israeli kuti ndi Banja la Wovulidwa nsapato.
11 Ngati anthu awiri akuchita ndewu ndipo mkazi wa mmodzi wa iwo abwera kudzaleretsa mwamuna wake kwa mnzakeyo natambasula dzanja lake kugwira ku maliseche kwa winayo,
12 muyenera kumudula dzanja, osamumvera chisoni.
13 Musamakhale ndi miyeso iwiri yosiyana mʼthumba mwanu, wolemera ndi wopepuka.
14 Musamakhale ndi milingo iwiri yosiyana mʼnyumba mwanu, waukulu ndi waungʼono.
15 Muyenera kukhala ndi miyeso ndi milingo yoyenera ndi yosanyenga kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
16 Pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita za chinyengo zoterezi.
17 Kumbukirani zimene Aamaleki anakuchitirani pamene munali pa ulendo wochokera ku Igupto.
18 Pamene munali otopa ndi ofowoka, iwo anakumana nanu pa ulendo wanu ndi kukantha onse otsalira mʼmbuyo ndipo iwo sanaope Mulungu.
19 Pamene Yehova Mulungu wanu akupumulitsani kwa adani onse okuzungulirani mʼdziko limene akupatsani inu ngati cholowa chanu, mudzawafafanize Aamaleki, asadzawakumbukirenso pa dziko lapansi. Musadzayiwale chimenechi!