< Deuteronomo 14 >

1 Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu. Osamadzichekacheka kapena kudzimeta pamphumi chifukwa cha abale anu amene amwalira,
Be ye children of the Lord your God: you shall not cut yourselves, no, make any baldness for the dead;
2 pakuti ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu. Pakati pa anthu onse pa dziko lonse lapansi, Yehova wasankha inu kuti chikhale chuma chake chamtengo wapatali.
Because thou art a holy people to the Lord thy God: and he chose thee to be his peculiar people of all nations that are upon the earth.
3 Musamadye chinthu chilichonse chonyansa.
Eat not the things that are unclean.
4 Nyama zomwe mukhoza kudya ndi izi: ngʼombe, nkhosa, mbuzi,
These are the beasts that you shall eat, the ox, and the sheep, and the goat,
5 mbawala, gwape, mphoyo, mphalapala, ngoma, nyumbu ndi mbalale.
The hart and the roe, the buffle, the chamois, the pygarg, the wild goat, the camelopardalus.
6 Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya.
Every beast that divideth the hoof in two parts, and cheweth the cud, you shall eat.
7 Komabe pakati pa nyama zimene zimabzikula kapena zogawikana zipondero, zimene simukuyenera kudya ndi ngamira, kalulu ndi mbira. Zimenezi ngakhale zimabzikula, zipondero zake sizogawikana, choncho ndi zodetsedwa, musadye.
But of them that chew the cud, but divide not the hoof, you shall not eat, such as the camel, the hare, and the cherogril: because they chew the cud, but divide not the hoof, they shall be unclean to you.
8 Nkhumba simabzikula ndi yodetsedwanso ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa.
The swine also, because it divideth the hoof, but cheweth not the cud, shall be unclean, their flesh you shall not eat, and their carcasses you shall not touch.
9 Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi, mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba.
These shall you eat of all that abide in the waters: All that have fins and scales, you shall eat.
10 Koma chilichonse chimene chilibe minga ya pa msana ndi mamba musadye pakuti nʼchodetsedwa.
Such as are without fins and scales, you shall not eat, because they are unclean.
11 Mukhoza kudya mbalame iliyonse yoyenera kudya.
All birds that are clean you shall eat.
12 Koma simukuyenera kudya izi: mphungu, nkhwazi, mwimba,
The unclean eat not: to wit, the eagle, and the grype, and the osprey,
13 nankapakapa, akamtema, akhungubwi a mitundu yonse, ndi mtundu uliwonse wa miphamba,
The ringtail, and the vulture, and the kite according to their kind:
14 mtundu uliwonse wa khwangwala,
And all of the raven’s kind:
15 kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo, mtundu uliwonse wa akabawi,
And the ostrich, and the owl, and the larus, and the hawk according to its kind:
16 kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi,
The heron, and the swan, and the stork,
17 tsekwe, vuwo, dembo,
And the cormorant, the porphyrion, and the night crow,
18 indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.
The bittern, and the charadrion, every one in their kind: the hoop also and the bat.
19 Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa. Musamadye zimenezi.
Every thing that creepeth, and hath little wings, shall be unclean, and shall not be eaten.
20 Koma chowuluka chilichonse choyenera kudya mukhoza kudya.
All that is clean, you shall eat.
21 Musamadye chilichonse chimene mwachipeza chofaifa. Mukhoza kupatsa mlendo amene akukhala mu mzinda wina uliwonse wa mizinda yanu. Iyeyo akhoza kudya kapena mukhoza kugulitsa kwa wina aliyense amene sali wa mtundu wanu. Koma inu ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu. Musamaphike mwana wambuzi mu mkaka wa mayi wake.
But whatsoever is dead of itself, eat not thereof. Give it to the stranger, that is within thy gates, to eat, or sell it to him: because thou art the holy people of the Lord thy God. Thou shalt not boil a kid in the milk of his dam.
22 Muzionetsetsa kuti mukupatula chakhumi pa zokolola zanu chaka chilichonse.
Every year thou shalt set aside the tithes of all thy fruits that the earth bringeth forth,
23 Muzidyera chakhumi cha tirigu wanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta, ndi ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene adzasankhe ngati kokhalako dzina lake, kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu.
And thou shalt eat before the Lord thy God in the place which he shall choose, that his name may be called upon therein, the tithe of thy corn, and thy wine, and thy oil, and the firstborn of thy herds and thy sheep: that thou mayst learn to fear the Lord thy God at all times.
24 Koma ngati malo amenewa ali kutali kwambiri ndipo kuti inu mwadalitsidwa ndi Yehova Mulungu wanu, ndipo simungathe kunyamula chakhumi chanu (chifukwa chakuti malo amene Yehova adzasankha kukayikako dzina lake ali kutali kwambiri),
But when the way and the place which the Lord thy God shall choose, are far off, and he hath blessed thee, and thou canst not carry all these things thither,
25 ndiye musinthitse chakhumi chanucho ndi siliva, ndipo mutenge silivayo ndi kupita naye kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.
Thou shalt sell them all, and turn them into money, and shalt carry it in thy hand, and shalt go to the place which the Lord shall choose:
26 Gwiritsani ntchito silivayo kugula chilichonse chimene muchifuna monga ngʼombe, nkhosa, vinyo kapena zakumwa zina zosasitsa, kapena china chilichonse chimene muchifuna. Ndipo inu ndi anthu a pa banja panu mudzazidyera komweko pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kukondwera.
And thou shalt buy with the same money whatsoever pleaseth thee, either of the herds or of sheep, wine also and strong drink, and all that thy soul desireth: and thou shalt eat before the Lord thy God, and shalt feast, thou and thy house:
27 Alevi okhala mʼmizinda yanu musaleke kuwathandiza popeza alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo.
And the Levite that is within thy gates, beware thou forsake him not, because he hath no other part in thy possession.
28 Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzibweretsa zakhumi zonse pa zokolola za chaka chimenecho ndi kuzisunga mʼmidzi yanu,
The third year thou shalt separate another tithe of all things that grow to thee at that time, and shalt lay it up within thy gates.
29 kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse.
And the Levite that hath no other part nor possession with thee, and the stranger and the fatherless and the widow, that are within thy gates, shall come and shall eat and be filled: that the Lord thy God may bless thee in all the works of thy hands that thou shalt do.

< Deuteronomo 14 >