< Deuteronomo 13 >
1 Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa,
If there rise in the midst of thee a prophet or one that saith he hath dreamed a dream, and he foretell a sign and a wonder,
2 chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe),
And that come to pass which he spoke, and he say to thee: Let us go and follow strange gods, which thou knowest not, and let us serve them:
3 musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
Thou shalt not hear the words of that prophet or dreamer: for the Lord your God trieth you, that it may appear whether you love him with all your heart, and with all your soul, or not.
4 Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo.
Follow the Lord your God, and fear him, and keep his commandments, and hear his voice: him you shall serve, and to him you shall cleave.
5 Mneneri kapena wolotayo ayenera kuphedwa, popeza analalikira zopandukira Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo. Wolalikirayo anafuna kukupatutsani pa njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani kuti muyitsatire. Muzichotsa choyipa pakati panu.
And that prophet or forger of dreams shall be slain: because he spoke to draw you away from the Lord your God, who brought you out of the land of Egypt, and redeemed you from the house of bondage: to make thee go out of the way, which the Lord thy God commanded thee: and thou shalt take away the evil out of the midst of thee.
6 Ngati mʼbale wanu weniweni kapena mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena mnzanu wapamtima akukakamizani mwachinsinsi, nʼkumati, “Tiyeni tipite tikapembedze milungu ina” (milungu imene inuyo kapena makolo anu sanayidziwe,
If thy brother the son of thy mother, or thy son, or daughter, or thy wife that is in thy bosom, or thy friend, whom thou lovest as thy own soul, would persuade thee secretly, saying: Let us go, and serve strange gods, which thou knowest not, nor thy fathers,
7 milungu ya anthu okuzungulirani, kaya ndi apafupi kapena akutali, kuchokera kumapeto mpaka kumapeto kwina kwa dziko lapansi),
Of all the nations round about, that are near or afar off, from one end of the earth to the other,
8 musamugonjere kapena kumumvera. Musamumvere chisoni. Musamuleke kapena kumutchinjiriza.
Consent not to him, hear him not, neither let thy eye spare him to pity and conceal him,
9 Mumuphe ndithu. Dzanja lanu likhale loyambirira kumupha, kenaka manja a anthu ena onse.
But thou shalt presently put him to death. It Let thy hand be first upon him, and afterwards the hands of all the people.
10 Mumuponye miyala mpaka kumupha, chifukwa anafuna kukupatutsani pa njira ya Yehova Mulungu amene anakutulutsani ku Igupto, dziko la ukapolo.
With stones shall he be stoned to death: because he would have withdrawn thee from the Lord thy God, who brought thee out of the land of Egypt, from the house of bondage:
11 Tsono Aisraeli onse adzamva nachita mantha, ndipo palibe mmodzi pakati panu amene adzachitenso choyipa chotere.
That all Israel hearing may fear, and may do no more any thing like this.
12 Ngati mumvetsedwa kuti ku umodzi mwa mizinda imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mukhalemo,
If in one of thy cities, which the Lord thy God shall give thee to dwell in, thou hear some say:
13 kwapezeka anthu ena oyipa pakati panu ndipo asocheretsa anthu ambiri mʼmizinda yanu, pomanena kuti, “Tiyeni tikapembedze milungu ina” (milungu imene simunayidziwe),
Children of Belial are gone out of the midst of thee, and have withdrawn the inhabitants of their city, and have said: Let us go, and serve strange gods which you know not:
14 mukuyenera kufunsa, kulondola ndi kufufuza bwino nkhaniyo. Ndipo ngati zitatsimikizikadi kuti ndi zoona kuti chinthu chonyansa chotere chachitikadi pakati panu,
Inquire carefully and diligently, the truth of the thing by looking well into it, and if thou find that which is said to be certain, and that this abomination hath been really committed,
15 muyenera kuwapha onse okhala mu mzinda umenewo. Muwonongeretu kwathunthu mzindawo, anthu ake ndi ziweto zake zomwe.
Thou shalt forthwith kill the inhabitants of that city with the edge of the sword, and shalt destroy it and all things that are in it, even the cattle.
16 Katundu yense wa anthu mu mzindawo mumuwunjike pamodzi pakatikati pa bwalo losonkhanako ndipo mutenthe mzindawo pamodzi ndi katundu wake yense monga nsembe yathunthu yopsereza ya kwa Yehova Mulungu wanu. Mzinda umenewo ukhale bwinja mpaka muyaya, usadzamangidwenso.
And all the household goods that are there, thou shalt gather together in the midst of the streets thereof, and shalt burn them with the city itself, so as to consume all for the Lord thy God, and that it be a heap for ever: it shall be built no more.
17 Musapezeke ndi kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa kuti Yehova abweze mkwiyo wake wochititsa manthawu. Adzakuchitirani chifundo ndi kukumverani chisoni, ndipo adzakuchulukitsani monga analonjeza mwa lumbiro kwa makolo anu,
And there shall nothing of that anathema stick to thy hand: that the Lord may turn from the wrath of his fury, and may have mercy on thee, and multiply thee as he swore to thy fathers,
18 chifukwa mumamvera Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino ndi kuchita zoyenera pamaso pake.
When thou shalt hear the voice of the Lord thy God, keeping all his precepts, which I command thee this day, that thou mayst do what is pleasing in the sight of the Lord thy God.