< Deuteronomo 10 >

1 Pa nthawi imeneyo Yehova anati kwa ine, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo ubwere nayo kwa Ine ku phiri. Upangenso bokosi lamatabwa.
那時上主對我說:「你再鑿兩塊石版,與先前的一樣,然後上山到我跟前來;還要做一個木櫃。
2 Ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. Ndipo iwe ukuyenera kuyika miyalayo mʼbokosimo.”
我要把你先前摔碎的那兩塊版上的話,寫在這兩塊版上。你要將這兩塊石版放在櫃裏。」
3 Choncho ndinapanga bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha ndi kusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo ndinapita ku phiri nditanyamula miyala iwiri mʼmanja mwanga.
我於是做了一個皂莢木櫃,鑿了兩塊與先前一樣的石版,手裏拿著這兩塊石版上山去了。
4 Yehova analemba pa miyala iwiriyo zimene analemba poyamba, Malamulo Khumi amene analengeza kwa inu pa phiri paja, mʼmoto, pa tsiku la msonkhano. Ndipo Yehova anawapereka kwa ine.
上主將先前所寫的,即在集會之日,在山上由火中對你們所說的那十句話,寫在這兩塊版上,交給了我。
5 Tsono ndinatsika ku phiri kuja ndi kuyika miyalayo mʼbokosi ndinapanga lija monga Yehova anandilamulira, ndipo panopa ili mʼmenemo.
我遂轉身下山,照上主吩咐我的,將版放在我做的櫃內,存在那裏。
6 Aisraeli anayenda kuchokera ku Beeroti Beni Yaakani mpaka ku Mosera. Kumeneko Aaroni anamwalira nayikidwa mʼmanda, ndipo mwana wake Eliezara anakhala wansembe mʼmalo mwake.
以色列子民由貝洛特貝乃雅干起程,到了摩色辣,亞郎在那裏死了,也埋在那裏;他的兒子厄肋阿匝爾繼他做了大司祭。
7 Kuchokera kumeneko Aisraeli anapita ku Gudigoda, napitirira mpaka ku Yotibata, ku dziko la mitsinje ya madzi.
又從那裏起程,到了古德哥達,又從古德哥達到了多溪水之地約特巴達。
8 Pa nthawi imeneyo Yehova anapatula fuko la Levi kuti anyamule bokosi la pangano la Yehova lija, kuti ayimirire pamaso pa Yehova, kutumikira ndi kunena madalitso pa dzina lake monga amachitira mpaka lero.
那時,上主選拔了肋未支派,叫他們抬上主的約櫃,侍立在上主面前事奉他,並奉他的名祝福,直到今日。
9 Nʼchifukwa chake Alevi alibe gawo kapena cholowa pakati pa abale awo. Yehova ndiye cholowa chawo monga momwe Yehova Mulungu wanu anawawuzira.
為此,肋未人同自己的兄弟沒有分得產業,因為照上主你的天主對他們所說的:上主自己是他們的產業。
10 Tsopano ndinakhala ku phiri kuja kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku monga ndinachitira poyamba, ndipo Yehova anandimveranso nthawi iyi. Sichinali chifuniro chake kuti akuwonongeni.
我如先前一樣,在山上逗留了四十天四十夜;上主這一次又俯聽了我,放棄了消滅你的意思。
11 Yehova anati kwa ine, “Pita ndi kutsogolera anthuwa pa njira yawo, kuti alowe ndi kulandira dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndiwapatse.”
上主且對我說:「起來,在人民前面領路,叫他們去佔領我對他們祖先誓許要賜給他們的地方。」
12 Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,
以色列! 現今上主你的天主向你要求什麼﹖是要求你敬畏上主你的天主,履行他的一切道路,愛他,全心全靈事奉上主你的天主,
13 ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero kuti zizikuyenderani bwino.
遵守我今天吩咐你的天主的誡命和法令,好使你能獲得幸福。
14 Yehova Mulungu wanu ndiye mwini wake kumwamba ngakhale mmwambamwamba, dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
看天與天上的天,地和地上的一切,都屬於上主你的天主;
15 Yehova anayika mtima wake pa makolo anu okha ndipo anawakondadi nasankha adzukulu awo mwa mitundu yonse pa dziko lapansi, kunena inuyo monga mulili lero.
但上主只喜歡了你的祖先,鍾愛他們,由萬民中揀選了他們的後裔,就是你們,正如你們今日所見的一樣。
16 Motero chitani mdulidwe wa mitima yanu ndipo musakhalenso opulupudza.
為此,你們要心受割損,不要執拗,
17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu.
因為上主你們的天主是萬神之神,萬主之主,偉大、有力、可畏的天主,是不顧情面,不受賄賂,
18 Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala.
為孤兒、寡婦主持正義,友愛外方人,供給他們食糧和衣服的天主。
19 Muzikonda alendo popeza inuyo munali alendo mʼdziko la Igupto.
為此,你們也應友愛外方人,因為你們在埃及也曾做過外方人。
20 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye. Mumukakamire Iyeyo ndi kuchita malumbiro anu mʼdzina lake.
你應敬畏上主你的天主,事奉依賴他,奉他的名起誓。
21 Iye ndiye matamando anu, Mulungu wanu amene anakuchitirani zodabwitsa zazikulu ndi zoopsa zimene munaona ndi maso anu zija.
他是你的光榮,是你的天主,是他為你做了你親眼所見的奇異可畏的事。
22 Makolo anu amene anapita ku Igupto analipo makumi asanu ndi awiri onse pamodzi, ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.
你的祖先下到埃及時,總共不過七十人,現在上主你的天主卻使你多得有如天上的繁星。

< Deuteronomo 10 >