< Akolose 4 >
1 Mabwana, antchito anu muzikhala nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziwa kuti nanunso muli nawo Ambuye anu mmwamba.
2 Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika.
3 Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende.
4 Pempherani kuti ndilalikire momveka bwino, monga ndikuyenera.
5 Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo.
6 Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.
7 Tukiko adzakuwuzani zonse za ine. Iye ndi mʼbale wokondedwa, mtumiki wokhulupirika ndiponso wantchito mnzanga mwa Ambuye.
8 Ine ndikumutumiza kwa inu ndi cholinga choti mudziwe zimene tikukumana nazo ndiponso kuti alimbikitse mitima yanu.
9 Iye akubwera ndi Onesimo, mʼbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ndi mmodzi mwa inu. Iwo adzakuwuzani zonse zimene zikuchitika kuno.
10 Aristariko, wamʼndende mnzanga akupereka moni, Marko akuperekanso moni, msuweni wa Barnaba. (Inu munawuzidwa kale za Iye. Iye akabwera kwanuko, mulandireni).
11 Yesu wotchedwa Yusto, akuperekanso moni. Amenewa ndi Ayuda okhawo pakati pa atumiki anzanga mu ufumu wa Mulungu, ndipo aonetsa kuti ndi chitonthozo kwa ine.
12 Epafra ndi mmodzi mwa inu ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu, akupereka moni. Iyeyu nthawi zonse amakupemphererani mwamphamvu, kuti mukhazikike pa chifuniro chonse cha Mulungu, mukhale okhwima ndi otsimikiza kwathunthu.
13 Ine ndikumuchitira umboni kuti amagwira ntchito mwamphamvu chifukwa cha inu ndiponso kwa amene ali ku Laodikaya ndi Herapoli.
14 Luka, dotolo wathu wokondedwa ndi Dema, akupereka moni.
15 Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake.
16 Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya.
17 Uzani Arkipo kuti, “Wonetsetsa kuti wamaliza ntchito imene unayilandira mwa Ambuye.”
18 Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa moni uwu. Kumbukirani kuti ndili mu unyolo. Chisomo chikhale ndi inu.