< Akolose 3 >
1 Tsono popeza munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mitima yanu pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
Therfor if ye han risun togidere with Crist, seke ye tho thingis that ben aboue, where Crist is sittynge in the riythalf of God.
2 Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi.
Sauere ye tho thingis, that ben aboue, not tho that ben on the erthe.
3 Pakuti munafa, ndipo moyo wanu tsopano wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
For ye ben deed, and youre lijf is hid with Crist in God.
4 Khristu, amene ndiye moyo wanu, akadzaonekanso, pamenepo inunso mudzaoneka naye pamodzi mu ulemerero.
For whanne Crist schal appere, youre lijf, thanne also ye schulen appere with hym in glorie.
5 Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano.
Therfor sle ye youre membris, whiche ben on the erthe, fornycacioun, vnclennesse, letcherie, yuel coueitise, and aueryse, which is seruyse of mawmetis;
6 Chifukwa cha zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa ana osamvera.
for whiche thingis the wraththe of God cam on the sones of vnbileue;
7 Inunso kale munkachita zomwezi, mʼmoyo wanu wakale uja.
in whiche also ye walkiden sum tyme, whanne ye lyueden in hem.
8 Koma tsopano mukuyenera kuzichotsa zinthu zonsezi monga: mkwiyo, ukali, dumbo, chipongwe ndi mawu onyansa.
But now putte ye awei alle thingis, wraththe, indignacioun, malice, blasfemye and foule word of youre mouth.
9 Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake
Nyle ye lie togidere; spuyle ye you fro the elde man with his dedes, and clothe ye the newe man,
10 ndipo mwavala munthu watsopano, amene nzeru zake zikukonzedwanso kuti afanane ndi Mlengi wake.
that is maad newe ayen in to the knowing of God, aftir the ymage of hym that made hym;
11 Pano palibe kusiyana pakati pa Mgriki ndi Myuda, wochita mdulidwe ndi wosachita, wosaphunzira kapena wosachangamuka, kapolo kapena mfulu, koma Khristu yekha basi ndipo amakhala mwa onse.
where is not male and female, hethene man and Jew, circumcisioun and prepucie, barbarus and Scita, bonde man and fre man, but alle thingis and in alle thingis Crist.
12 Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.
Therfor ye, as the chosun of God, hooli and louyd, clothe you with the entrailis of merci, benygnite, and mekenesse, temperaunce, pacience;
13 Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu.
and support ye echon other, and foryyue to you silf, if ony man ayens ony hath a querele; as the Lord foryaf to you, so also ye.
14 Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
And vpon alle these thingis haue ye charite, that is the boond of perfeccioun.
15 Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika.
And the pees of Crist enioye in youre hertis, in which ye ben clepid in o bodi, and be ye kynde.
16 Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika.
The word of Crist dwelle in you plenteuousli, in al wisdom; and teche and moneste you silf in salmes, and ympnes, and spiritual songis, in grace synginge in youre hertis to the Lord.
17 Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Al thing, what euere thing ye don, in word or in dede, alle thingis in the name of oure Lord Jhesu Crist, doynge thankyngis to God and to the fadir bi hym.
18 Inu akazi, gonjerani amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.
Wymmen, be ye sugetis to youre hosebondis, as it bihoueth in the Lord.
19 Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima.
Men, loue ye youre wyues, and nyle ye be bittere to hem.
20 Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.
Sones, obeie ye to youre fadir and modir bi alle thingis; for this is wel plesinge in the Lord.
21 Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.
Fadris, nyle ye terre youre sones to indignacioun, that thei be not maad feble hertid.
22 Inu antchito, mverani mabwana anu mu zonse, ndipo muzichita zimenezi osati nthawi yokhayo imene akukuonani kuti akukondeni, koma muzichite moona mtima ndi mopereka ulemu kwa Ambuye.
Seruauntis, obeie ye bi alle thingis to fleischli lordis, not seruynge at iye, as plesynge to men, but in symplenesse of herte, dredinge the Lord.
23 Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu.
What euer ye doen, worche ye of wille, as to the Lord and not to men;
24 Inu mukudziwa kuti mudzalandira mphotho monga cholowa kuchokera kwa Ambuye. Ndi Ambuye Khristu amene mukumutumikira.
witinge that of the Lord ye schulen take yelding of eritage. Serue ye to the Lord Crist.
25 Aliyense amene amachita zolakwa adzalandira malipiro molingana ndi kulakwa kwake, ndipo palibe tsankho.
For he that doith iniurie, schal resseyue that that he dide yuele; and acceptacioun of persoones is not anentis God.