< Akolose 2 >
1 Ndikufuna mudziwe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo pamodzi ndi anzanu a ku Laodikaya, ndi ena onse amene sitinaonane maso ndi maso.
Wherefore, I wish you to know how great a combat I have for you, and for them in Laodicea, and for as many as have not seen my face in the flesh;
2 Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu.
that being compacted together in love, their hearts may be comforted, even by all the riches of the full assurance of understanding, to the acknowledgment of the secret of God,
3 Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso.
in whom are laid up all the treasures of wisdom and knowledge.
4 Ndikukuwuzani zimenezi kuti wina aliyense asakunamizeni ndi kukukopani ndi mawu ake.
Now this I say, that no one may deceive you with plausible speech.
5 Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu.
For though I am absent in the flesh, yet I am with you in the spirit, rejoicing and beholding your order, and the steadfastness of your faith in Christ.
6 Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo.
Now as you have received Christ Jesus the Lord, walk in him;
7 Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.
rooted and built up in him, and established in the faith, even as you have been taught, abounding in it with thanksgiving.
8 Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu.
Beware lest any one make a prey of you through an empty and deceitful philosophy, --according to the tradition of men, according to the elements of the world, and not according to Christ.
9 Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu.
For all the fullness of the Deity resides substantially in him.
10 Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse.
And you are complete in him, who is the head of all government and power.
11 Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija.
By whom, also, you have been circumcised with the circumcision made without hands, in the putting off of the body of the flesh, by the circumcision of Christ;
12 Mu ubatizo, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa.
having been buried with him in immersion, by which also you have been raised with him, through the belief of the strong working of God, who raised him from the dead.
13 Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse.
For you, who were dead on account of trespasses, and by the uncircumcision of your flesh, he had made alive together with him, having forgiven you all trespasses: --
14 Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda.
having blotted out the handwriting of the ordinances concerning us, which was contrary to us, he has taken it away, nailing it to the cross: --
15 Ndipo atalanda zida maufumu ndi maulamuliro, Iye anawachititsa manyazi powayendetsa pamaso pa anthu onse atawagonjetsa ndi mtanda.
having spoiled governments and powers, he made a show of them openly, having triumphed over them by it.
16 Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata.
Let no one, therefore, judge you in meat, or in drink, or in respect of a festival, or of a new moon, or of sabbaths;
17 Zimenezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zimene zikubwera, koma choonadi chenicheni chikupezeka mwa Khristu.
which are a shadow of the things which were to come, but the substance is of Christ.
18 Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu.
Let no one beguile you of your reward, --delighting in humility, and the worship of messengers, intruding into things which he has not seen, being without cause, puffed up by his own carnal mind:
19 Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire.
and not holding firmly the head, by whom the whole body, through the joints and ligaments, being served and compacted, increases with the increase of God.
20 Popeza munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nayo miyambo ya dziko lapansi lino, nʼchifukwa chiyani mukukhalanso ngati a dziko lapansi lino? Bwanji mukumvera malamulo monga awa:
Now, if you have died with Christ from the elements of the world, why, as living in the world, you are subject to ordinances,
21 “Usagwire chakuti,” “Usalawe chakuti,” “Usakhudze chakuti?”
Touch not, taste not, handle not;
22 Malamulo amenewa amakhudza zinthu zimene zimatha zikamagwiritsidwa ntchito, ndipo malamulo ndi zophunzitsa za anthu chabe.
(which are all to perish with the using; ) after the commandments and doctrines of men;
23 Ndithu malamulo oterewa amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamulira anthu ambiri pa zachipembedzo ndi pa zakudzichepetsa kwa chiphamaso, ndi pa zakuzunza thupi lawo, koma alibe mphamvu zoletsa kuchita zofuna za thupilo.
which things have, indeed, a show of wisdom in will-worship, and humility, and not sparing the body--without any respect to the gratification of the flesh.