< Amosi 1 >
1 Mawu a Amosi, mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa. Zimene iye anaona mʼmasomphenya zokhudza Israeli patatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike, nthawi imene Uziya anali mfumu ya Yuda ndipo Yeroboamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya Israeli.
2 Amosi anati: “Yehova akubangula mu Ziyoni ndipo akumveka ngati bingu mu Yerusalemu; msipu wa abusa ukulira, ndipo pamwamba pa Karimeli pakuwuma.”
3 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira za mano achitsulo,
4 Ine ndidzatumiza moto pa nyumba ya Hazaeli umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.
5 Ndidzathyola chipata cha Damasiko; ndidzawononga mfumu yokhala ku Chigwa cha Aveni, ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu mu Beti-Edeni. Anthu a ku Aramu adzapita ku ukapolo ku Kiri,” akutero Yehova.
6 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatenga ukapolo mtundu wathunthu ndi kuwugulitsa ku Edomu,
7 ndidzatumiza moto pa makoma a Gaza umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.
8 Ndidzawononga mfumu ya ku Asidodi komanso amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni. Ndidzalanga Ekroni, mpaka wotsala mwa Afilisti atafa,” akutero Ambuye Yehova.
9 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Turo akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo anagulitsa mtundu wathunthu ku ukapolo ku Edomu, osasunga pangano laubale lija,
10 Ine ndidzatumiza moto pa makoma a Turo umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.”
11 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga, popanda nʼchifundo chomwe. Popeza mkwiyo wake unakulabe ndipo ukali wake sunatonthozeke,
12 Ine ndidzatumiza moto pa Temani umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Bozira.”
13 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Amoni akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatumbula akazi oyembekezera a ku Giliyadi nʼcholinga choti akuze malire awo,
14 Ine ndidzayatsa moto pa makoma a ku Raba umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu. Padzakhala kulira kwakukulu pa tsiku la nkhondoyo, kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvuluvulu.
15 Mfumu yawo idzatengedwa kupita ku ukapolo, iyo pamodzi ndi akuluakulu ake,” akutero Yehova.